18 Anachita zimenezo kuti mwa zinthu ziwiri zosasinthika, zimene chifukwa cha zinthu zimenezo n’zosatheka kuti Mulungu aname,+ ife amene tathawira kumalo otetezeka tilimbikitsidwe kwambiri, kuti tigwire mwamphamvu chiyembekezo+ chimene chaikidwa patsogolo pathu.