20 “‘Ine ndinaphwanya goli lako kukhala zidutswazidutswa kalekale.+ Ndinadula zingwe zimene anakumanga nazo. Koma iwe unati: “Sindikutumikirani,” ndipo unagona motangadza+ paphiri lililonse lalitali ndi pansi pa mtengo uliwonse waukulu wa masamba ambiri obiriwira+ n’kumachita uhule+ pamenepo.