25 Iwo analanda mizinda yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri.+ Analandanso nthaka yachonde,+ nyumba zodzaza ndi zinthu zonse zabwino,+ zitsime,+ minda ya mpesa ndi ya maolivi+ ndi mitengo ya zipatso yochuluka. Atatero, anayamba kudya, kukhuta,+ kunenepa+ ndi kukondwera ndi ubwino wanu waukulu.+