13 Kenako amuna awiri opanda pake anabwera n’kukhala patsogolo pa Naboti. Ndiyeno amuna opanda pakewo anayamba kupereka umboni wotsutsana ndi Naboti pamaso pa anthuwo, wakuti: “Naboti watemberera Mulungu ndi mfumu!”+ Pambuyo pake anamutulutsira kunja kwa mzindawo n’kumuponya miyala mpaka anafa.+