10Mfumukazi ya ku Sheba+ inali kumva za Solomo, ndi zoti anatchuka chifukwa cha dzina la Yehova.+ Choncho inabwera kuti idzamuyese pomufunsa mafunso ovuta.+
6 Chikhamu cha ngamila zamphongo zing’onozing’ono za ku Midiyani ndi ku Efa+ chidzadzaza dziko lako. Anthu onse a ku Sheba+ adzabwera atanyamula golide ndi lubani. Iwo adzatamanda Yehova pamaso pa anthu onse.+