14 Ndiyeno Yehova anandiyankha kuti: “Aneneriwo akulosera monama m’dzina langa.+ Ine sindinawatume, kuwalamula, kapena kulankhula nawo.+ Maulosi amene akukuuzaniwo anthu inu, ndiwo masomphenya onama, maula, mawu opanda pake+ ndi chinyengo cha mumtima mwawo.+