8 Nditayang’ana, ndinaona hatchi yotuwa. Wokwerapo wake dzina lake anali Imfa. Ndipo Manda+ anali kumutsatira pafupi kwambiri. Iwo anapatsidwa ulamuliro pa gawo limodzi la magawo anayi a dziko lapansi, kuti aphe anthu ndi lupanga lalitali,+ njala,+ mliri wakupha, ndi zilombo+ za padziko lapansi.