9 Zili choncho podziwa mfundo iyi yakuti, lamulo siliikidwa chifukwa cha munthu wolungama. Limaikidwa chifukwa cha anthu osamvera malamulo,+ osalamulirika,+ osaopa Mulungu, ochimwa, osakoma mtima,+ onyoza zinthu zopatulika, opha abambo ndi amayi awo, opha anthu,