Nehemiya
7 Mpanda utangotha kumangidwanso,+ ndinaika zitseko zake.+ Kenako ndinaika pa udindo alonda amʼmageti,+ oimba+ ndi Alevi.+ 2 Kenako ndinaika Haneni mʼbale wanga+ ndi Hananiya, mkulu wa mʼNyumba ya Chitetezo Champhamvu,+ kuti aziyangʼanira Yerusalemu. Hananiya anali munthu wodalirika ndiponso woopa Mulungu woona+ kuposa anthu ena ambiri. 3 Choncho ndinawauza kuti: “Mageti a Yerusalemu sayenera kutsegulidwa mpaka dzuwa litakwera. Alonda amʼmageti aime pafupi ndipo atseke zitseko nʼkuzikhoma ndi anamphatika. Muikenso alonda a anthu a ku Yerusalemu, ena muwaike pamalo awo olondera ndipo ena muwaike kutsogolo kwa nyumba zawo.” 4 Mzindawo unali wotakasuka ndiponso waukulu. Munali anthu ochepa+ ndipo nyumba zinali zisanamangidwenso.
5 Koma Mulungu wanga anaika nzeru mumtima mwanga kuti ndisonkhanitse anthu olemekezeka, atsogoleri ndi anthu onse kuti alembetse mayina motsatira mndandanda wa makolo awo.+ Ndiyeno ndinapeza buku la mndandanda wa mayina wa anthu amene anabwera moyambirira kuchokera ku ukapolo. Ndinapeza kuti mʼbukumo analembamo izi:
6 Awa ndi anthu amʼchigawo amene anachoka ku ukapolo, anthu omwe Nebukadinezara+ mfumu ya ku Babulo anawatenga nʼkupita nawo ku ukapolo.+ Anthuwa anabwerera ku Yerusalemu ndi ku Yuda, aliyense mumzinda wakwawo.+ 7 Amenewa anabwera pamodzi ndi Zerubabele,+ Yesuwa,+ Nehemiya, Azariya, Raamiya, Nahamani, Moredikayi, Bilisani, Misiperete, Bigivai, Nehumu ndi Bana.
Chiwerengero cha amuna a Isiraeli chinali ichi:+ 8 Ana a Parosi, 2,172. 9 Ana a Sefatiya, 372. 10 Ana a Ara,+ 652. 11 Ana a Pahati-mowabu,+ ochokera mwa ana a Yesuwa ndi Yowabu,+ 2,818. 12 Ana a Elamu,+ 1,254. 13 Ana a Zatu, 845. 14 Ana a Zakai, 760. 15 Ana a Binui, 648. 16 Ana a Bebai, 628. 17 Ana a Azigadi, 2,322. 18 Ana a Adonikamu, 667. 19 Ana a Bigivai, 2,067. 20 Ana a Adini, 655. 21 Ana a Ateri, a mʼbanja la Hezekiya, 98. 22 Ana a Hasumu, 328. 23 Ana a Bezai, 324. 24 Ana a Harifi, 112. 25 Ana a Gibiyoni,+ 95. 26 Amuna a ku Betelehemu ndi ku Netofa, 188. 27 Amuna a ku Anatoti,+ 128. 28 Amuna a ku Beti-azimaveti, 42. 29 Amuna a ku Kiriyati-yearimu,+ Kefira ndi ku Beeroti,+ 743. 30 Amuna a ku Rama ndi ku Geba,+ 621. 31 Amuna a ku Mikemasi,+ 122. 32 Amuna a ku Beteli+ ndi ku Ai,+ 123. 33 Amuna a ku Nebo wina, 52. 34 Ana a Elamu wina, 1,254. 35 Ana a Harimu, 320. 36 Ana a Yeriko, 345. 37 Ana a Lodi, Hadidi ndi Ono,+ 721. 38 Ana a Senaya, 3,930.
39 Ansembe:+ Ana a Yedaya, a mʼbanja la Yesuwa, 973. 40 Ana a Imeri, 1,052. 41 Ana a Pasuri,+ 1,247. 42 Ana a Harimu,+ 1,017.
43 Alevi:+ Ana a Yesuwa, a mʼbanja la Kadimiyeli+ ochokera pakati pa ana a Hodeva, 74. 44 Oimba:+ ana a Asafu,+ 148. 45 Alonda apageti:+ ana a Salumu, ana a Ateri, ana a Talimoni, ana a Akubu,+ ana a Hatita ndi ana a Sobai, 138.
46 Atumiki apakachisi:*+ Ana a Ziha, ana a Hasufa, ana a Tabaoti, 47 ana a Kerosi, ana a Siya, ana a Padoni, 48 ana a Lebana, ana a Hagaba, ana a Salimai, 49 ana a Hanani, ana a Gideli, ana a Gahara, 50 ana a Reyaya, ana a Rezini, ana a Nekoda, 51 ana a Gazamu, ana a Uziza, ana a Paseya, 52 ana a Besai, ana a Meyuni, ana a Nefusesimu, 53 ana a Bakibuki, ana a Hakufa, ana a Harihuri, 54 ana a Baziliti, ana a Mehida, ana a Harisa, 55 ana a Barikosi, ana a Sisera, ana a Tema, 56 ana a Neziya komanso ana a Hatifa.
57 Ana a atumiki a Solomo:+ Ana a Sotai, ana a Sofereti, ana a Perida, 58 ana a Yaala, ana a Darikoni, ana a Gideli, 59 ana a Sefatiya, ana a Hatili, ana a Pokereti-hazebaimu ndi ana a Amoni. 60 Atumiki apakachisi*+ onse ndiponso ana a atumiki a Solomo analipo 392.
61 Amene anachokera ku Tele-mela, Tele-harisa, Kerubi, Adoni ndi Imeri koma sanathe kufotokoza mzere wa makolo awo ndi kumene anachokera, komanso kuti anali Aisiraeli kapena ayi,+ ndi awa: 62 Ana a Delaya, ana a Tobia ndi ana a Nekoda, 642. 63 Ansembe anali awa: ana a Habaya, ana a Hakozi+ ndiponso ana a Barizilai amene anatenga mkazi pakati pa ana aakazi a Barizilai+ wa ku Giliyadi nʼkuyamba kutchedwa ndi dzina lawo. 64 Amenewa ndi amene mayina awo anawayangʼana mʼkaundula kuti atsimikizire za mzere wawo wobadwira koma sanapezekemo. Choncho anawaletsa kuti asatumikire ngati ansembe.*+ 65 Bwanamkubwa*+ anawauza kuti asamadye zinthu zopatulika koposa,+ mpaka patakhala wansembe amene angagwiritse ntchito Urimu ndi Tumimu.+
66 Anthu onse analipo 42,360.+ 67 Apa sanawerengere akapolo awo aamuna ndi akapolo awo aakazi+ amene analipo 7,337. Iwo analinso ndi oimba aamuna ndi aakazi 245.+ 68 Anali ndi mahatchi 736 ndi nyulu* 245. 69 Ngamila zawo zinalipo 435 ndipo abulu awo analipo 6,720.
70 Atsogoleri ena a nyumba za makolo anapereka zinthu zothandizira pa ntchito.+ Bwanamkubwa* anapereka kumalo osungira chuma ndalama za dalakima* zagolide 1,000, mbale zolowa 50 ndi mikanjo ya ansembe 530.+ 71 Panalinso atsogoleri ena a nyumba za makolo amene anapereka mphatso zothandizira pa ntchitoyo kumalo osungira chuma. Iwo anapereka ndalama za dalakima zagolide 20,000 ndi ndalama za mina* zasiliva 2,200. 72 Ndipo anthu ena onse anapereka ndalama za dalakima zagolide 20,000, ndalama za mina zasiliva 2,000 ndi mikanjo ya ansembe 67.
73 Ndiyeno ansembe, Alevi, alonda apageti, oimba,+ anthu ena, atumiki apakachisi* ndiponso Aisiraeli onse anayamba kukhala mʼmizinda yawo.+ Pofika mwezi wa 7,+ Aisiraeli anali atakhala mʼmizinda yawo.+