Lingaliro la Baibulo
Kodi Miyala Yamlengalenga Idzagunda ndi Kuwononga Dziko?
PA March 12, 1998, manyuzipepala, ma TV, ndi ma internet padziko lonse lapansi analengeza nkhani yochititsa mantha yakuti: “Mwala wina wa za mlengalenga waukulu makilomita 1.5 unangotsala pang’ono kuombana ndi dziko lapansi.” Asayansi ndi anthu wamba omwe anatangwanika kuti afufuze mmene ngoziyo inaliri. Posapita nthaŵi, akatswiri opima za mlengalenga anati apeza kuti panalibe mpata wakuti pakanakhala kuombana.
Komabe, nkhaniyo idakali mkamwa, panabuka mfundo ina. “Chinthu chimodzi chodziŵika bwino chokhudza chenjezolo, ngakhale kuti ngoziyo sikanachitika nchakuti, anthu ambiri sanadabwe nalo kwenikweni chenjezolo,” inatero U. S. News & World Report. “Lingaliro lakuti ife pano Padziko Lapansi tiyenera kukhala tcheru kuona miyala yamtundu umenewu—ndi kukhala okonzekera kuchitapo kanthu—likanakhala lachilendo kwambiri zaka khumi kapena kuposerapo zapitazo, koma tsopano asayansi ngakhale ena mwa andale akuganiza kuti ngoziyo, ngakhale kuti ndi mwakamodzikamodzi kuti ichitike, koma ikhoza kuchitika.”
Akatswiri ena opima mlengalenga amakhulupirira kuti miyala yokwana 2000 yaikulu kwakuti nkuwononga dziko imayenda mothamanga m’njira zomwe zimadutsana ndi njira yomwe dzikoli limayendamo kapena kuyenda m’njira zoyandikana ndi njira ya dziko. Akatswiri ofufuzafufuza zinthu amati ngati umodzi wa iyo ngakhale waung’ono chabe utaomba dzikoli, kuphulika kwake kukhoza kufanana nkuphulika kwa mabomba a nyukiliya ambiri ataphulikira pamodzi. Mwalawo utaombana ndi dziko lathuli, lingawonongekeretu limodzi ndi anthu ndi nyama zomwe.
Mfundo imodzi imene amaiŵala kuganizira njakuti Mlengi wa miyambayi, Yehova Mulungu, amalingalira bwanji za ngozi yoopsa imene anthuwo amayerekezera kuti idzachitika. (Salmo 8:3; Miyambo 8:27) M’Baibulo iye ananena momveka bwino zimene akulinga kudzachita dziko lapansi ndi zimenenso akufuna kudzachitira mtundu wa anthu. Kodi iye adzalola kuti mwala wamlengalenga uwononge dziko?
Miyamba Imalamulidwa ndi Mulungu
Popeza Yehova ndiye Mlengi wamphamvu zonse yemwe analenga miyamba, nkwanzeru kukhulupirira kuti ali ndi mphamvu yowongolera ndi kulamulira zinthu zakumwamba. Mfumu yanzeru Solomo inati Yehova ‘anaika za mwamba ndi luntha.’ (Miyambo 3:19) Mneneri Yeremiya anati Mulungu “ndi luso anayala thambo.”—Yeremiya 51:15.
Yehova anakhazikitsa malamulo ndi mphamvu zoyendetsa zakumwamba zimenezi, kuphatikizapo nyenyezi, mapulaneti, makometi, ndi miyala ina yotchedwa ma asteroids. (Yesaya 40:26) Komabe zimaoneka ngati kuti iye amalola nyenyezi ndi mapulaneti kuti zizingoyenda zungulirezungulire monga mmene anazilengera, zatsopano kumapangika, kukhalapo ndi kuwonongeka popanda iye kumachitapo kanthu nthaŵi zonse. Izi zimaphatikizapo kuombana kodetsa nkhaŵa kwa zinthu zamlengalenga. Chitsanzo chimodzi cha kuombana kwa posachedwapa ndi cha pa July 1994 pamene zidutswa za comet yotchedwa Shoemaker-Levy zinaomba pulaneti yotchedwa Jupiter.
A sayansi yopenda miyala yadziko anapeza umboni wakuti miyala yochokera mu mlengalenga inaombapo dziko lathuli kale pasanakhale anthu. Koma kodi zimenezi zidzachitika padzikoli pali anthu? Mwachitsanzo, kodi chingachitike nchiyani ngati mwala waukulu makilomita 1.5 utaombana ndi dziko? Wa sayansi ya zamlengalenga Jack Hills anati mphamvu zake zikhoza kukhala ngati bomba limene linawononga Hiroshima kuŵirikiza nthaŵi mamiliyoni ambiri. Ngati utagwera m’nyanja mafunde ake akhoza kusefukira ndi kuwononga kugombe. Hills anati, “Pamene kale panali mizinda pangathe kungokhala matope okhaokha.” Utakhala waukulu kwambiri ndiye kuti anthu onse padziko akhoza kufa. Kodi ngozi yonenedweratu imeneyi imagwirizana motani ndi zolinga za Mlengi wathu ponena za dziko? Baibulo limasonyeza kuti pulaneti lino ndi lapadera pa zifuno za Yehova.
Dziko Lathu—Polipanga Panali Cholinga
Ponena za pulaneti lathuli, wamasalmo anati: “Kumwamba, kumwamba ndiko kwa Yehova; koma dziko lapansi analipereka kwa ana a anthu.” (Salmo 115:16) Yesaya ananena za Yehova monga “amene anaumba dziko lapansi . . . . Iye analikhazikitsa, sanalilenga mwachabe, Iye analiumba akhalemo anthu.” (Yesaya 45:18) Dziko lapansi Yehova anapatsa anthu. Ndipo popeza kuti Mlengi wathu amalingalira zoti anthu amene amamuopa adzakhalepo kosatha, dziko lapansi lidzakhalapo kosatha monga mudzi wawo wokhalamo. Salmo 104:5 limatitsimikizira kuti: “[Yehova] anakhazika dziko lapansi pa maziko ake, silidzagwedezeka ku nthaŵi yonse.”
Nzoona kuti Mulungu walola masoka ena kugwera dziko, ndi kupha anthu ambiri. Ena mwa masoka amenewa monga—nkhondo, njala, ndi miliri—amachitika chifukwa cha umbombo, umbuli, ndi nkhanza za anthu. (Mlaliki 8:9) Ena monga—zivomezi, ma volokano, kusefukira kwa madzi, ndi mkuntho—zakhala zikupangika mwachilengedwe, mwanjira imene anthu samamvetsa. Mosiyana ndi zolinga za Mulungu za poyamba, anthu tsopano salinso angwiro; koma ochimwa. Nchifukwa chake pakali pano, aliyense payekha, sitingayembekezere Mulungu kutitchinjiriza pa masoka achilengedwe.
Komabe, Yehova sanavomereze kuti anthu padziko akhale pangozi yaikulu kwambiri. Kuyambira pamene munthu analengedwa, mbiri yakale yodziŵika ndiyakuti sipanayambe pachitikapo tsoka lachilengedwe lomwe linawonongapo anthu nkutsala pang’ono kuwatsiriza onse.a
Nzotsimikizika Kuti Anthu Adzapulumuka
Kuyambira pamene anthu analengedwa, cholinga cha Mlengi wathu nchakuti anthu ‘achuluke ndi kudzaza dziko lapansi.’ (Genesis 1:28; 9:1) Iye walonjeza kuti “Olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.” (Salmo 37:9, 11, 22, 29) Ponena za malonjezo ake, Yehova amatsimikizira kuti: “Uphungu wanga udzakhala, ndipo ndidzachita zofuna zanga zonse.”—Yesaya 46:10; 55:11; Salmo 135:6.
Baibulo silinena kuti padziko sipangachitike ngakhale ngozi yaing’ono yochititsidwa ndi miyala yamlengalenga. Komabe tingakhale otsimikizira kuti Yehova sadzalola kuti miyalayi ipangitse ngozi padziko ndi kulepheretsa zimene akufuna kudzachita padziko ndi zimenenso akufuna kudzachitira mtundu wa anthu. Chifukwa cha malonjezo a m’Baibulo, tingatsimikizire kuti pa pulaneti lathuli padzakhala anthu kosatha—inde, lidzakhala mudzi wa anthu ku nthaŵi zosatha!—Mlaliki 1:4; 2 Petro 3:13.
[Mawu a M’munsi]
a Chigumula cha m’tsiku la Nowa chinali njira ya Mulungu yolangira anthu, koma Yehova anaonetsetsa kuti anthu ena ndi nyama zipulumuke.—Genesis 6:17-21.