March
Lachitatu, March 1
Pa mlingo umene munachitira zimenezo mmodzi wa abale anga aang’ono awa, munachitira ine amene.—Mat. 25:40.
“Nkhosa” zotchulidwa mufanizo la pa Mateyu 25:31-36, zikuimira olungama mu nthawi ya mapeto ino omwe ali ndi chiyembekezo chodzakhala padzikoli kapena kuti a nkhosa zina. Iwo amathandiza mokhulupirika abale ake a Khristu odzozedwa pogwira ntchito yolalikira ndi kuphunzitsa anthu padziko lonse. (Mat. 24:14; 28:19, 20) Chaka chilichonse kutatsala milungu ingapo kuti tsiku la Chikumbutso lifike, a nkhosa zina amasonyeza kuti amathandiza abale ake a Khristu pogwira nawo ntchito yapadera yomwe imachitika padziko lonse yoitanira anthu achidwi ku Chikumbutso. Iwo amayesetsanso kuthandiza pokonzekera kuti Chikumbutso chichitike mumpingo uliwonse. A nkhosa zina amasangalala kuthandiza abale ake a Khristu m’njira zimenezi. Iwo amadziwa kuti Yesu amaona zimene amachita pothandiza abale ake odzozedwa ngati kuti akuchitira iyeyo.—Mat. 25:37-40. w22.01 22 ¶11-12
Lachinayi, March 2
Amene waona ine waonanso Atate.—Yoh. 14:9.
Tiyenera kutsanzira makhalidwe a Yesu komanso mmene ankachitira zinthu ndi anthu ena. Mwachitsanzo, iye anachitira chifundo munthu wakhate, mayi amene ankadwala matenda aakulu komanso ankamvera chisoni anthu amene aferedwa. Choncho tikamatsanzira Yesu, timakhalanso tikutsanzira Yehova. (Maliko 1:40, 41; 5:25-34; Yoh. 11:33-35) Tikamatsanzira kwambiri makhalidwe a Yehova, m’pamenenso ubwenzi wathu ndi iye umalimba kwambiri. Tikamatsatira mapazi a Yesu sitidzasokonezedwa ndi dziko loipali. Usiku woti aphedwa mawa lake, Yesu ananena kuti: “Ine ndaligonjetsa dziko.” (Yoh. 16:33) Iye ankatanthauza kuti sanalole kutengera maganizo, zolinga komanso zochita za anthu a m’dzikoli. Yesu sanaiwale cholinga chimene anamutumizira padzikoli, chomwe chinali kudzasonyeza kuti Yehova ndiye woyenera kulamulira. Nanga bwanji ifeyo? M’dzikoli muli zinthu zambiri zimene zingatisokoneze. Koma mofanana ndi Yesu, ngati tingaike maganizo athu onse pakuchita chifuniro cha Yehova, ifenso tingathe ‘kugonjetsa’ dziko.—1 Yoh. 5:5. w21.04 3-4 ¶7-8
Lachisanu, March 3
[Palibe chidzathe] kutilekanitsa ndi chikondi cha Mulungu chimene chili mwa Khristu Yesu Ambuye wathu.—Aroma 8:39.
Mtumwi Paulo ankadziwa bwino zimene Yesu analonjeza kuti “aliyense wokhulupirira mwa iye [Yesu]. . . akhale ndi moyo wosatha.” (Yoh. 3:16; Aroma 6:23) Mwachionekere, Paulo anali mmodzi mwa anthu amene ankakhulupirira kwambiri dipo. Iye sankakayikira ngakhale pang’ono kuti Yehova ndi wokonzeka kukhululukira anthu amene achita machimo akuluakulu koma alapa. (Sal. 86:5) Ankakhulupiriranso kwambiri kuti Mulungu amamukonda ndipo anatumiza Khristu kuti adzamufere. Taonani mawu olimbikitsa amene ali kumapeto kwa Agalatiya 2:20. Iye anati: “Mwana wa Mulungu . . . anandikonda ndi kudzipereka yekha chifukwa cha ine.” Onani kuti Paulo sanaone kuti chikondi cha Mulungu chili ndi malire. Iye sananene kuti, ‘Ndikuona kuti Yehova akhoza kumakonda abale anga, koma ineyo sangandikonde.’ Iye anakumbutsa Akhristu a ku Roma kuti: “Moti pamene tinali ochimwa, Khristu anatifera.” (Aroma 5:8) Choncho chikondi cha Mulungu chilibe malire. Paulo ankakhulupirira kwambiri kuti Mulungu amamukonda. Iye ankadziwa kuti Yehova anachita zinthu moleza mtima ndi mtundu wa Aisiraeli. w21.04 22 ¶8-10
Loweruka, March 4
Chifukwa kukonda Mulungu kumatanthauza kusunga malamulo ake.—1 Yoh. 5:3.
Mukamachititsa phunziro la Baibulo, muziyesetsa kupeza mipata yothandiza wophunzirayo kudziwa makhalidwe a Yehova. Muzimuthandiza kuona kuti Yehova ndi Mulungu wachimwemwe amene amathandiza anthu omwe amamukonda. (1 Tim. 1:11; Aheb. 11:6) Muzimufotokozera kuti zinthu zingamuyendere bwino kwambiri akamagwiritsa ntchito zimene akuphunzirazo, ndipo muzimuuza kuti umenewo ndi umboni woti Yehova amamukonda. (Yes. 48:17, 18) Wophunzirayo akamakonda kwambiri Yehova m’pamene angathe kusintha zinthu pa moyo wake. Kuti afike pobatizidwa, wophunzira Baibulo ayenera kudzimana zinthu zambiri. Ophunzira ena amafunika kusiya zinthu zina zomwe ali nazo. Ambiri amafunika kusiya kucheza ndi anzawo omwe sakonda Yehova. Enanso angakanidwe ndi achibale awo omwe sasangalala ndi a Mboni za Yehova. Yesu analonjeza kuti anthu amene angamutsatire sadzanong’oneza bondo. M’malomwake Yehova adzawapatsa abale ndi alongo, omwe adzakhale ngati banja lawo.—Maliko 10:29, 30. w21.06 4 ¶8-9
Lamlungu, March 5
Kwezani maso anu muone m’mindamo, mwayera kale ndipo m’mofunika kukolola.—Yoh. 4:35.
Mtumwi Paulo anayerekezera ntchito yophunzitsa anthu ndi ulimi. Zimenezi zikusonyeza kuti pali zambiri zimene timayenera kuchita, osati kungodzala mbewu. Iye anakumbutsa Akhristu a ku Korinto kuti: “Ineyo ndinabzala, Apolo anathirira . . . Inuyo ndinu munda wa Mulungu umene ukulimidwa.” (1 Akor. 3:6-9) Popeza ndife antchito ‘m’munda wa Mulungu,’ sikuti timangodzala mbewu koma timazithirira pafupipafupi n’kumaona mmene zikukulira. Pa nthawi imodzimodziyo, timazindikira kuti Mulungu ndi amene amakulitsa mbewuzo. Ndi mwayitu waukulu kwambiri kugwira nawo ntchito yolalikira komanso kuphunzitsa anthu choonadi. Ntchito imeneyi imatithandiza kuti tizisangalala kwambiri. Mtumwi Paulo, yemwe anathandiza anthu ambiri a ku Tesalonika kuti akhale ophunzira, anafotokoza mmene ankamvera, ndipo anati: “Kodi chiyembekezo chathu, kapena chimwemwe chathu n’chiyani? Inde, mphoto yathu yoinyadira pamaso pa Ambuye wathu Yesu, pa nthawi ya kukhalapo kwake n’chiyani? Si inu amene kodi? Ndithudi, inu ndinudi ulemerero wathu ndi chimwemwe chathu.”—1 Ates. 2:19, 20; Mac. 17:1-4. w21.07 3 ¶5; 7 ¶17
Lolemba, March 6
Musanyoze mmodzi wa tianati.—Mat. 18:10.
Yehova anatikokera tonsefe kwa iye. (Yoh. 6:44) Tangoganizirani zimenezi. Pamene Yehova ankafufuza mitima ya anthu mabiliyoni padzikoli anaona kanthu kena kamtengo wapatali mwa inu. Anaona kuti muli ndi mtima wabwino ndipo mukhoza kumukonda. (1 Mbiri 28:9) Yehova amakudziwani, amakumvetsani komanso amakukondani. Zimenezitu ndi zolimbikitsa kwambiri. Yehova amakukondani kwambiri ndipo amakondanso abale ndi alongo anu onse. Pofuna kutithandiza kumvetsa mfundoyi, Yesu anayerekezera Yehova ndi m’busa. Ngati nkhosa imodzi pa nkhosa 100 itasochera, kodi m’busa amachita chiyani? Iye ‘amasiya nkhosa 99 zija m’phiri ndi kupita kukafunafuna yosocherayo.’ Akaipeza, samaikwiyira koma amasangalala. Kodi tikuphunzirapo chiyani? Nkhosa iliyonse ndi yofunika kwa Yehova. Yesu anati: “Atate wanga wakumwamba sakufuna kuti mmodzi wa tianati akawonongeke.”—Mat. 18:12-14. w21.06 20 ¶1-2
Lachiwiri, March 7
Yandikirani Mulungu.—Yak. 4:8.
Tikamaganizira chikondi chosatha chimene Mulungu anatisonyeza, timayamba kumukonda kwambiri ndipo ubwenzi wathu ndi iye umalimba. (Aroma 8:38, 39) Timalimbikitsidwa kutengera chitsanzo cha Yesu. (1 Pet. 2:21) Kutatsala masiku ochepa kuti Chikumbutso chichitike, timaganizira nkhani za m’Baibulo zofotokoza zimene zinachitika pa mlungu womaliza wa moyo wa Yesu padzikoli, imfa yake komanso kuukitsidwa kwake. Kenako pa tsiku la Chikumbutso madzulo, nkhani imene imakambidwa imatikumbutsa chikondi chimene Yesu anatisonyeza. (Aef. 5:2; 1 Yoh. 3:16) Tikamawerenga komanso kuganizira chitsanzo cha Yesu chololera kuvutikira ena, timalimbikitsidwa “kupitiriza kuyenda mmene iyeyo anayendera.” (1 Yoh. 2:6) Timakhala otsimikiza kukhalabe mabwenzi a Yehova. (Yuda 20, 21) Timapitiriza kukhalabe pa ubwenzi ndi Mulungu tikamayesetsa kumumvera, kuyeretsa dzina lake komanso kusangalatsa mtima wake. (Miy. 27:11; Mat. 6:9; 1 Yoh. 5:3) Kupezeka pa Chikumbutso kumatichititsa kuti tikhale otsimikiza kuti tsiku lililonse tizichita zinthu zomwe zingakhale ngati tikumuuza Yehova kuti, ‘Ndikufuna kukhala bwenzi lanu mpaka kalekale.’ w22.01 23 ¶17; 25 ¶18-19
Lachitatu, March 8
Sankhani . . . amene mukufuna kum’tumikira.—Yos. 24:15.
Yehova anatipatsa ufulu wosankha. Tingathe kusankha zimene tikufuna kuchita pa moyo wathu. Mulungu wathu wachikondi amasangalala tikasankha kumutumikira. (Sal. 84:11; Miy. 27:11) Tikhoza kugwiritsa ntchito ufulu umenewu posankha zochita mwanzeru. Tingatengere chitsanzo cha Yesu tikamaika zofuna za ena patsogolo m’malo mwa zofuna zathu. Pa nthawi ina Yesu ndi atumwi ake atatopa kwambiri, anapita kumalo ena kuti akapume. Komabe zimenezi sizinatheke. Khamu la anthu linawatsatira ndipo ankafunitsitsa kuti Yesu awaphunzitse. Koma Yesu sanawakwiyire anthuwo. M’malomwake iye anawamvera chisoni. Ndiye kodi Yesu anatani? Iye “anayamba kuwaphunzitsa zinthu zambiri.” (Maliko 6:30-34) Tikamatsanzira Yesu pogwiritsa ntchito nthawi ndi mphamvu zathu pothandiza ena, timalemekeza Atate wathu wakumwamba.—Mat. 5:14-16. w21.08 3 ¶7-8
Lachinayi, March 9
Aliyense payekha . . . adzakhala ndi chifukwa chosangalalira ndi ntchito yake, osati modziyerekezera ndi munthu wina.—Agal. 6:4.
Yehova amakonda zinthu zosiyanasiyana ndipo sayembekezera kuti zonse zizikhala zofanana. Umboni wa zimenezi ndi wakuti iye analenga mitundu yosiyanasiyana ya zinthu, kuphatikizapo anthu. Munthu aliyense ndi wosiyana ndi mnzake. Choncho Yehova samakuyerekezerani ndi anthu ena. Iye amafufuza mmene mtima wanu ulili. (1 Sam. 16:7) Amaganiziranso zinthu zimene mumachita bwino, zofooka zanu komanso mmene munaleredwera. Ndipo sayembekezera kuti muzichita zimene simungakwanitse. Tiyenera kutsanzira Yehova pomadziona ngati mmene iye amationera. Tikatero tidzasonyeza kuti ndife “munthu woganiza bwino,” osati kumadziona kuti ndife munthu wapamwamba kapena wolephera. (Aroma 12:3) N’zoona kuti tingapindule kwambiri tikamachita chidwi ndi zimene m’bale kapena mlongo wina wokhulupirika amachita pa nkhani yolalikira. (Aheb. 13:7) Tikutero chifukwa tikhoza kuphunzira njira zolalikirira zimene zingatithandize kuti ifenso tizichita bwino mu utumiki. (Afil. 3:17) Koma pali kusiyana pakati pa kutengera chitsanzo chabwino cha munthu wina, ndi kudziyerekezera ndi munthuyo. w21.07 20 ¶1-2
Lachisanu, March 10
Kwezani maso anu kumwamba muone. Kodi ndani amene analenga zinthu zimenezo?—Yes. 40:26.
Tingalimbitse chikhulupiriro chathu tikamachita chidwi ndi zinthu monga nyama, zomera komanso nyenyezi. (Sal. 19:1) Mukamaphunzira kwambiri zokhudza zinthu zimenezi m’pamenenso mumapeza umboni wokwanira woti Yehova ndi Mlengi. Mukamaphunzira zokhudza chilengedwe muziganizira zimene zinthuzo zikukuphunzitsani ponena za Mlengi wathu. (Aroma 1:20) Mwachitsanzo, mwina mukudziwa kuti kuwonjezera pa kutulutsa kutentha komwe kumathandiza zamoyo, dzuwa limatulutsanso kuwala komwe kungakhale kowononga. Anthufe timafunika kutetezedwa kuti kuwala kumeneku kusativulaze ndipo timatetezedwadi. Kodi timatetezedwa bwanji? Dziko lathu lili ndi mpweya wina mlengalenga womwe umachepetsa mphamvu ya kuwala kumeneku. Kuwala kowonongaku kukamawonjezereka, mpweyawonso umawonjezereka. Ndiye pamenepa, kodi simukuvomereza kuti pali winawake amene amachititsa zimenezi, yemwe ndi Mlengi wanzeru komanso wachikondi? w21.08 17 ¶9-10
Loweruka, March 11
Munthu amene amakonda Mulungu azikondanso m’bale wake.—1 Yoh. 4:21.
Munthu akabatizidwa, tiyenera kupitiriza kumusonyeza chikondi komanso kumulemekeza. (1 Yoh. 4:20) Kodi tingachite bwanji zimenezi? Njira ina imene tingachitire zimenezi, ndi kusonyeza kuti sitikukayikira zolinga zake. Mwachitsanzo, ngati sitinamvetse chifukwa chake wachitira zinazake sitingafulumire kuganiza kuti wachita zimenezo ndi zolinga zoipa. M’malomwake, tidzalemekeza m’bale wathuyo n’kumamuona kuti ndi wotiposa. (Aroma 12:10; Afil. 2:3) Tizichitira chifundo komanso kukomera mtima anthu onse. Ngati tikufuna kupitiriza kukhala m’banja la Yehova, tiyenera kumagwiritsa ntchito zimene timaphunzira m’Mawu a Mulungu pa moyo wathu. Mwachitsanzo, Yesu anatiphunzitsa kuti tiyenera kumachitira chifundo komanso kukomera mtima anthu onse kuphatikizapo adani athu. (Luka 6:32-36) Koma nthawi zina kuchita zimenezi kungakhale kovuta. Ngati zili choncho, tiyenera kuphunzira kuti tiziganiza komanso kuchita zinthu ngati Yesu. Tikamayesetsa kuchita zonse zomwe tingathe pomvera Yehova komanso kutsanzira Yesu, timasonyeza Atate wathu wakumwamba kuti tikufuna kukhala m’banja lake mpaka kalekale. w21.08 6 ¶14-15
Lamlungu, March 12
Muone ngati sindidzakutsegulirani zipata za kumwamba ndi kukukhuthulirani madalitso.—Mal. 3:10.
Muzidalira Yehova. Iye amalonjeza kuti azitipatsa madalitso ochuluka tikamamudalira komanso kuchita zonse zomwe tingathe pomutumikira. M’Baibulo muli zitsanzo za anthu ambiri omwe anachita khama potumikira Yehova. Nthawi zambiri, anthuwa ankafunika kuchita kaye zinazake zosonyeza kuti akumudalira kuti iye awadalitse. Mwachitsanzo, panali pambuyo poti Abulahamu wachoka kwawo, “ngakhale sanadziwe kumene anali kupita,” pamene Yehova anamudalitsa. (Aheb. 11:8) Yakobo analandiranso madalitso apadera pambuyo poti walimbana ndi mngelo. (Gen. 32:24-30) Komanso Aisiraeli atatsala pang’ono kulowa m’Dziko Lolonjezedwa, panali pamene ansembe anaponda mumtsinje wa Yorodano pomwe anthu anatha kuwoloka. (Yos. 3:14-16) Mukhozanso kuphunzira zambiri kwa a Mboni za Yehova amasiku ano, omwe asonyeza kudalira Yehova n’kudzipereka kuti achite zambiri pomutumikira. w21.08 29-30 ¶12-14
Lolemba, March 13
Usanene kuti: “N’chifukwa chiyani kale zinthu zinali bwino kuposa masiku ano?”—Mlal. 7:10.
Abale ndi alongo achikulirenu mumadziwa mmene zinthu zinkachitikira kalelo koma mumazindikiranso kuti n’kofunika kuti muzichita zinthu mogwirizana ndi mmene zilili masiku ano. Inunso achikulire amene mwangobatizidwa kumene mungathandize ena. Achinyamata angasangalale kumva zimene mwakumana nazo pa moyo wanu komanso zimene mwakhala mukuphunzira. ‘Mukakhala opatsa’ kapena kuti kugawirako ena zimene zili munkhokwe yanu ya zinthu zimene mukudziwa, Yehova adzakudalitsani kwambiri. (Luka 6:38) Ngati achikulirenu mutamachita zinthu limodzi ndi achinyamata, nonse mukhoza kumathandizana. (Aroma 1:12) Aliyense amakhala kuti ali ndi chinthu china chake chamtengo wapatali chimene wina alibe. Achikulire amadziwa zinthu zambiri komanso amakhala ndi nzeru zimene apeza pa nthawi imene akhala ndi moyo, pomwe achinyamata amakhala ndi mphamvu. Achinyamata ndi achikulire akamagwirizana n’kumachitira zinthu limodzi, amapereka ulemerero kwa Atate wathu wachikondi komanso amathandiza kwambiri mumpingo. w21.09 8 ¶3; 13 ¶17-18
Lachiwiri, March 14
Timalalikira za Khristu amene anapachikidwa. Kwa Ayuda, chimenechi ndi chinthu chokhumudwitsa.—1 Akor. 1:23.
Kodi mmene Yesu anafera, zinachititsa bwanji kuti Ayuda ambiri amukane? Kwa iwo, kuphedwa kwa Yesu pamtengo wozunzikirapo kunachititsa kuti azimuona ngati wachifwamba komanso wochimwa, osati Mesiya. (Deut. 21:22, 23) Ayuda omwe anakana Yesu analephera kuzindikira kuti iye anali wosalakwa, anaimbidwa milandu yabodza komanso anachitiridwa zinthu zopanda chilungamo. Anthu amene ankaweruza mlandu wa Yesu, anapotoza chilungamo. Oweruza a Khoti Lalikulu la Ayuda anakumana mofulumira ndipo poweruza mlanduwo sankatsatira malamulo. (Luka 22:54; Yoh. 18:24) M’malo momvetsera mlanduwo komanso maumboni ake mosakondera, iwo ankafunafuna “umboni wonama kuti amunamizire mlandu Yesu ndi kumupha.” (Mat. 26:59; Maliko 14:55-64) Komanso Yesu ataukitsidwa, oweruza opanda chilungamowa anapereka ndalama zasiliva zambiri kwa asilikali a Chiroma, omwe ankalondera manda ake kuti afalitse nkhani yabodza yokhudza zimene zinachitika kuti thupi la Yesu lisapezeke m’mandamo.—Mat. 28:11-15. w21.05 11 ¶12-13
Lachitatu, March 15
Kunena za tsikulo ndi ola lake, palibe amene akudziwa, ngakhale angelo akumwamba kapenanso Mwana, koma Atate yekha.—Mat. 24:36.
Yehova akanatha kuthetsa dziko loipali nthawi ina iliyonse. Koma zimene wachita pokhala woleza mtima zathandiza kwambiri tonsefe. Ana onse a Adamu ndi Hava amabadwa ali ochimwa. Komabe Yehova amawakonda ndipo amawasamalira ndiponso akulonjeza kuti adzawononga dziko loipali. (1 Yoh. 4:19). Iye wakonza nthawi imene adzathetse mavuto onse amene anthu akukumana nawo. Kodi zimenezi siziyenera kutichititsa kupirira naye limodzi mpaka nthawi imeneyo? Yehova ndi chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhani ya kupirira. Yesu anatengera chitsanzo cha Atate wake chifukwa ali padzikoli anapirira kunyozedwa, zinthu zochititsa manyazi komanso kuzunzidwa pamtengo wozunzikirapo chifukwa cha ife. (Aheb. 12:2, 3) N’zosakayikitsa kuti chitsanzo cha Yehova cha kupirira chinamuthandiza kwambiri Yesu, ndipo ifenso chingatithandize. w21.07 12-13 ¶15-17
Lachinayi, March 16
Pitirizani kukhala achifundo, potengera Atate wanu amenenso ali wachifundo.—Luka 6:36.
Tsiku lililonse Atate wathu wakumwamba amatisonyeza kuti ndi wachifundo. (Sal. 103:10-14) Otsatira a Yesu sanali anthu angwiro komabe iye ankawasonyeza chifundo komanso kuwakhululukira. Iye anali wofunitsitsa ngakhale kupereka moyo wake n’cholinga choti machimo athu akhululukidwe. (1 Yoh. 2:1, 2) Timayamba kukondana kwambiri ndi abale athu ‘tikamakhululukirana ndi mtima wonse.’ (Aef. 4:32) N’zoona kuti nthawi zina kukhululukira ena kungakhale kovuta kwambiri koma tiyenera kuyesetsa kuti tizikhululuka. Mlongo wina anaona kuti nkhani ya mu Nsanja ya Olonda, yamutu wakuti, “Muzikhululukirana ndi Mtima Wonse” inamuthandiza kwambiri. Iye analemba kuti: “Nkhaniyi inafotokoza kuti kukhululukira ena sikutanthauza kuti ukuona kuti zimene akuchitirazo ndi zabwino kapena ndi zazing’ono. M’malomwake kumatanthauza kusasunga zifukwa n’kupitiriza kukhala ndi mtendere wa mumtima.” Tikamakhululukira abale ndi alongo athu ndi mtima wonse timasonyeza kuti timawakonda komanso timatsanzira Atate wathu Yehova. w21.09 23-24 ¶15-16
Lachisanu, March 17
Onse omulambira [Mulungu] ayenera kumulambira motsogoleredwa ndi . . . choonadi.—Yoh. 4:24.
Yesu ankakonda choonadi, chimenechi ndi choonadi chonena za Mulungu komanso chifuniro chake. Iye ankachita zinthu mogwirizana ndi choonadi komanso ankadziwitsa ena choonadicho. (Yoh. 18:37) Otsatira oona a Yesu amakondanso kwambiri choonadi. (Yoh. 4:23) Ndipotu mtumwi Petulo ananena kuti Chikhristu ndi “njira ya choonadi.” (2 Pet. 2:2) Chifukwa chokonda kwambiri choonadi Akhristu oyambirira ankakana ziphunzitso zachipembedzo, miyambo komanso maganizo a anthu osemphana ndi choonadi. (Akol. 2:8) Mofanana ndi zimenezi, masiku ano Akhristu oona “akuyendabe m’choonadi” poyesetsa kuti zonse zimene amakhulupirira komanso kuchita zizichokera m’Mawu a Yehova. (3 Yoh. 3, 4) Anthu a Mulungu masiku ano sanena kuti nthawi zonse amamvetsa mfundo zonse za choonadi. Nthawi zina iwo amalakwitsa akamafotokoza mfundo zina za m’Baibulo kapena malangizo oyendetsera gulu la Yehova. Akazindikira zoona zake, iwo amakonza zimene analakwitsazo. w21.10 21-22 ¶11-12
Loweruka, March 18
Wokhulupirira Yehova amazunguliridwa ndi kukoma mtima kosatha.—Sal. 32:10.
Mofanana ndi mipanda imene inkateteza mizinda kalelo, chikondi chokhulupirika cha Yehova chimatitchinga n’kumatiteteza ku zinthu zimene zingawononge ubwenzi wathu ndi iye. Kuwonjezera pamenepo, chikondi chimenechi chimamuchititsa kuti atikokere kwa iye. (Yer. 31:3) Wolemba salimo Davide anagwiritsa ntchito mawu abwino pofotokoza mmene Mulungu amatetezera anthu ake. Iye anati: “Mulungu ndiye malo anga okwezeka ndiponso achitetezo, Mulungu wandisonyeza kukoma mtima kosatha.” Ndipo ponena za Yehova, Davide anawonjezera kuti: “Iye amandisonyeza kukoma mtima kwake kosatha ndipo ndiye malo anga achitetezo, malo anga okwezeka ndi wopereka chipulumutso, chishango changa ndi malo anga othawirako.” (Sal. 59:17; 144:2) N’chifukwa chiyani ponena za chikondi chokhulupirika cha Yehova, Davide anatchulanso za malo othawirako ndi achitetezo? Kaya timakhala kuti padzikoli, ngati tili atumiki ake, Yehova adzatipatsa zonse zimene timafunikira kuti titeteze ubwenzi wathu ndi iye. w21.11 6 ¶14-15
Lamlungu, March 19
Ndidzasinkhasinkha za ntchito zanu zonse.—Sal. 77:12.
Yesu ndi ophunzira ake atakumana ndi mphepo yamphamvu panyanja, iye anagwiritsa ntchito zomwe zinachitikazo powathandiza kuona mbali zimene ankafunika kulimbitsa chikhulupiriro chawo. (Mat. 8:23-26) Pamene mphepoyo komanso madzi zinkawomba botilo, Yesu anali akugona. Ophunzirawo omwe anali ndi mantha, atamudzutsa n’kumupempha kuti awapulumutse, iye anawadzudzula mokoma mtima kuti: “N’chifukwa chiyani mukuchita mantha chonchi, anthu achikhulupiriro chochepa inu?” Kodi mukukumana ndi mavuto omwe ali ngati “mphepo yamphamvu” pa moyo wanu? Mwina ndi mavuto obwera chifukwa cha ngozi zam’chilengedwe. Mwinanso ikhoza kukhala mphepo yamphamvu yophiphiritsa monga matenda aakulu omwe akuchititsani kuti mufooke moti simukudziwa zoti muchite. Nthawi zina mukhoza kumada nkhawa, koma musamalole kuti nkhawazo zikulepheretseni kudalira Yehova. Muzipemphera kwa iye mochokera pansi pa mtima. Muzilimbitsa chikhulupiriro chanu poganizira kwambiri mmene Yehova anakuthandizirani pa nthawi zina m’mbuyomo. (Sal. 77:11) Ndipo mungakhale otsimikiza kuti iye sadzakusiyani ngakhale pang’ono, kaya panopa kapena m’tsogolo. w21.11 22 ¶7, 10
Lolemba, March 20
Musabe.—Lev. 19:11.
Anthu ena anganene kuti, ngati munthu atamapewa kutenga zinthu zomwe si zake ndiye kuti akutsatira lamulo limeneli. Komatu munthuyo akhoza kukhala kuti akuba m’njira zina. Mwachitsanzo, wamalonda yemwe ankagwiritsa ntchito masikelo kapena zoyezera zina zachinyengo n’cholinga choti apusitse anthu omwe akuchita nawo malonda, ankakhala kuti akuwabera. Chaputala 19 cha Levitiko, chikusonyeza kugwirizana pakati pa kuba ndi kuchita bizinezi mwachinyengo ponena kuti: “Usabere mnzako mwachinyengo.” Choncho kuchita malonda mwachinyengo n’kogwirizana ndi kuba komanso uchifwamba. Ngakhale kuti lamulo la 8, limanena za kuba, mfundo za mu Levitiko zingatithandize kuona mmene tingagwiritsire ntchito lamuloli. N’zofunika kuti tiziganizira mmene Yehova amaonera chinyengo komanso kuba. Tingadzifunse kuti: ‘Mogwirizana ndi Levitiko 19:11-13, kodi pali mbali zina pa moyo wanga zimene ndiyenera kukonza? Kodi ndikufunika kusintha mmene ndimachitira zinthu pa nkhani ya bizinezi komanso ntchito?’ w21.12 9-10 ¶6-8
Lachiwiri, March 21
Monga Yehova anakukhululukirani ndi mtima wonse, inunso teroni.—Akol. 3:13.
Tsiku lililonse mukamapemphera panokha, muziganizira zimene munalakwitsa patsikulo n’kupempha Yehova kuti akukhululukireni. Koma ngati mwachita tchimo lalikulu mungafunike kuuzanso akulu. Iwo adzakuthandizani mwachikondi komanso kukupatsani malangizo ochokera m’Mawu a Mulungu. Akuluwo adzapemphera nanu kupempha Yehova kuti akukhululukireni pogwiritsa ntchito dipo la Yesu kuti “muchiritsidwe” kapena kuti mukhalenso naye pa ubwenzi. (Yak. 5:14-16) Kuganizira mozama zokhudza dipo n’kothandiza kwambiri. N’kutheka kuti mumamva chisoni mukaganizira mmene Mwana wa Mulungu anavutikira. Koma mukamaganizira kwambiri nsembe ya Yesu m’pamene mumayamba kumukonda kwambiri iyeyo komanso Atate wake. Chaka chilichonse timasonyeza kuti timayamikira kwambiri dipo tikapezeka pamwambo wokumbukira imfa ya Yesu komanso tikamachita khama kuitanira ena kumwambowu. Apatu Yehova anatipatsa mwayi wamtengo wapatali wophunzitsa ena zokhudza Mwana wake. w21.04 18-19 ¶13-16
Lachitatu, March 22
Anayamba kuwaphunzitsa zinthu zambiri.—Maliko 6:34.
Taganizirani zimene Yesu anachita ataona khamu la anthu likubwera kwa iye ali m’mbali mwa phiri. Iye anali atachezera kupemphera usiku wonse. Ayenera kuti anali atatopa kwambiri. Koma ataona khamu la anthulo, iye anayamba kuganizira kwambiri za odwala komanso osauka amene anali pamenepo. Sikuti Yesu anangochiritsa odwalawo, koma anakambanso imodzi mwa nkhani zolimbikitsa kwambiri yomwe imadziwika kuti ulaliki wa paphiri. (Luka 6:12-20) Yesu ankathandizanso ena ngakhale panthawi imene ankafunika kuchita zinthu payekha. Taganizirani mmene Yesu anamvera atadziwa kuti mnzake, Yohane M’batizi waphedwa. Baibulo limati: “Yesu atamva zimenezi, [zokhudza kuphedwa kwa Yohane], anachoka kumeneko pa ngalawa n’kupita kumalo kopanda anthu kuti akakhale payekha.” (Mat. 14:10-13) Koma khamu la anthu linakafika kumaloko iye asanafikeko n’komwe. (Maliko 6:31-33) Iye ankachita kuoneratu kuti anthuwo akufunika kulimbikitsidwa mwauzimu, moti anawalimbikitsadi.—Luka 9:10, 11. w22.02 21 ¶4, 6
Lachinayi, March 23
Khalani mwamtendere ndi anthu onse.—Aroma 12:18.
Kodi tiyenera kuchita chiyani tikazindikira kuti takhumudwitsa Mkhristu mnzathu? Tiyenera kupemphera kwa Yehova mochokera pansi pamtima. Tingamupemphe kuti atithandize pamene tikuyesetsa kuti tikhalenso pamtendere ndi m’bale wathuyo. Tingachitenso bwino kudzifufuza. Tingadzifunse mafunso ngati awa: ‘Kodi ndimavomereza ndikalakwitsa zinthu, n’kupepesa modzichepetsa komanso kukhazikitsa mtendere? Kodi Yehova ndi Yesu amamva bwanji ndikamayesetsa kukhazikitsa mtendere ndi m’bale kapena mlongo?’ Mayankho athu pamafunso amenewa angatilimbikitse kumvera Yesu ndipo modzichepetsa tingapite kukakambirana ndi Mkhristu mnzathuyo kuti tikhale nayenso pamtendere. Tikapita kukakhazikitsa mtendere ndi m’bale wathu timafunika kukhala odzichepetsa. (Aef. 4:2, 3) Tiyenera kupita kwa munthu amene tamukhumudwitsayo n’cholinga choti tikhalenso naye pa ubwenzi wabwino. Kumbukirani kuti kukhazikitsa mtendere ndi m’bale wanuyo n’kofunika kwambiri kuposa kufufuza yemwe analakwa ndi yemwe sanalakwe.—1 Akor. 6:7. w21.12 26 ¶13-16
Lachisanu, March 24
Anaona mzindawo n’kuyamba kuulirira.—Luka 19:41.
Yesu anamva kupweteka mumtima chifukwa Ayuda ambiri anali atasonyeza kuti sankafuna kumvetsera uthenga wa Ufumu. Chifukwa cha zimenezi, mzinda wa Yerusalemu ukanawonongedwa ndipo Ayuda omwe akanapulumuka akanatengedwa kupita ku ukapolo. (Luka 21:20-24) N’zomvetsa chisoni kuti monga mmene iye ananenera, anthu ambiri anamukanadi. Kodi anthu ambiri kudera limene mumakhala amamvetsera uthenga wa Ufumu? Ngati ndi anthu ochepa amene amamvetsera mukamayesetsa kuwaphunzitsa choonadi, kodi mungaphunzire chiyani pa misozi ya Yesu? Yehova amadera nkhawa anthu. Misozi ya Yesu imatikumbutsa kuti Yehova amaganizira kwambiri anthu. “Safuna kuti wina aliyense adzawonongedwe, koma amafuna kuti anthu onse alape.” (2 Pet. 3:9) Masiku ano timasonyeza kuti timakonda anthu ena poyesetsa kuwathandiza kuti amve uthenga wabwino wa Ufumu.—Mat. 22:39. w22.01 16 ¶10-12
Loweruka, March 25
Ndakulondolani kulikonse, dzanja lanu lamanja landigwira mwamphamvu.—Sal. 63:8.
Chikhulupiriro chanu chingalimbe kwambiri mukamaganizira zimene Yehova wachitira anthu ake komanso zimene wakuchitirani inuyo panokha. Chofunika kwambiri ndi chakuti, mudzayamba kukonda kwambiri Yehova. Kuposa makhalidwe ena onse, chikondi chingakuthandizeni kuti muzimvera Yehova, kulolera kusiya zinthu zina kuti mumusangalatse komanso kupirira mayesero alionse. (Mat. 22:37-39; 1 Akor. 13:4, 7; 1 Yoh. 5:3) Palibe chinthu china chofunika kwambiri kuposa kukonda komanso kukhala pa ubwenzi ndi Yehova. (Sal. 63:1-7) Muzikumbukira kuti kupemphera, kuphunzira komanso kuganizira mozama zimene tikuphunzirazo ndi mbali ya kulambira kwathu. Mofanana ndi Yesu, muzipeza malo opanda phokoso kuti muchite zinthu ndi Yehova. Muzipewa zilizonse zimene zingakusokonezeni. Muzipempha Yehova kuti akuthandizeni kuika maganizo anu onse pa zinthu zokhudza kulambira zomwe mukuchita. Mukamagwiritsa ntchito bwino nthawi yanu panopa, Yehova adzakudalitsani ndipo mudzakhala ndi moyo m’dziko latsopano la Mulungu mpaka kalekale.—Maliko 4:24. w22.01 31 ¶18-20
Lamlungu, March 26
Nyansidwani ndi choipa.—Aroma 12:9.
Anthufe timachita zimene timaganiza. N’chifukwa chake Yesu anaphunzitsa kuti tizikana maganizo omwe angachititse kuti tichite tchimo lalikulu. (Mat. 5:21, 22, 28, 29) Timafuna kusangalatsa Atate wathu wakumwamba. Choncho n’zofunika kwambiri kuti tizichotsa mwamsanga maganizo alionse oipa omwe tingakhale nawo. Yesu anati: “Zotuluka m’kamwa zimachokera mumtima.” (Mat. 15:18) Zimenetu ndi zoona, chifukwa zimene timalankhula zimasonyeza kuti ndife anthu otani. Choncho muzidzifunsa kuti: ‘Kodi ndimapewa kunama ngakhale kuti kunena zoona kungachititse kuti ndikumane ndi mavuto? Ngati ndili pa banja, kodi ndimapewa kukopana ndi anthu amene si amuna kapena akazi anzanga? Kodi ndimapeweratu kulankhula mawu otukwana? Kodi ndimalankhula modekha munthu wina akandikhumudwitsa?’ Ndi zothandiza kwambiri kumaganizira mafunso ngati amenewa. Mukamayesetsa kupewa mawu oipa, kunama kapena kulankhula mawu otukwana mukamalankhula ndi ena, mudzaona kuti n’zosavuta kuvula umunthu wakale. w22.03 5 ¶12-14
Lolemba, March 27
Anthu amene amakhala pamodzi n’kumakambirana amakhala ndi nzeru.—Miy. 13:10.
Anthu amene amapempha malangizo m’malo modikira kuti ena awapatse malangizowo amapita patsogolo kwambiri mwauzimu kusiyana ndi anthu amene safufuza malangizo. Choncho muziyamba ndi inuyo kupempha ena kuti akupatseni malangizo. Kodi ndi pa nthawi iti pamene tingapemphe malangizo kwa Akhristu anzathu? Tingapemphe malangizo pa zochitika ngati izi: (1) Mlongo wina akupempha wofalitsa waluso kuti apite naye kuphunziro la Baibulo ndipo kenako akumupempha malangizo amene angamuthandize kuti aziphunzitsa bwino. (2) Mlongo wina wosakwatiwa akufuna kugula zovala ndiye akupempha mlongo wina wolimba mwauzimu kuti amuthandize kusankha zovala zabwino. (3) M’bale wapemphedwa kuti akambe nkhani ya onse kwa nthawi yoyamba. Iye akupempha m’bale amene ali ndi luso lokamba nkhani kuti amvetsere nkhani yakeyo komanso kumupatsa malangizo amene angamuthandize kuwonjezera luso lake. Ngakhale m’bale amene wakhala akukamba nkhani kwa zaka zambiri angachite bwino kupempha malangizo kwa abale aluso n’kuwagwiritsa ntchito.—Miy. 19:20. w22.02 13 ¶15-17
Lachiwiri, March 28
[Sindili] ndekha, pakuti Atate amene anandituma ali ndi ine.—Yoh. 8:16.
Yehova amatikonda komanso kutisamalira ngati mmene anachitira ndi Yesu pa nthawi yonse imene ankachita utumiki wake padzikoli, womwe unali wovuta kwambiri. (Yoh. 5:20) Iye anathandiza Yesu kuti akhalebe ndi chikhulupiriro cholimba, kumulimbikitsa pamene anali ndi nkhawa komanso anaonetsetsa kuti ali ndi zofunika pa moyo. Yehova ankauzanso Mwana wakeyu kuti amamukonda ndipo ankasangalala naye. (Mat. 3:16, 17) Popeza ankadziwa kuti Atate wake wachikondi sangamusiye, Yesu sankadziona kuti ali yekhayekha. Mofanana ndi Yesu, tonsefe takhala tikuona Yehova akutisonyeza chikondi m’njira zosiyanasiyana. Tangoganizani, Yehova watilola kuti tikhale mabwenzi ake komanso watipatsa abale ndi alongo ambiri omwe amatithandiza kukhala osangalala komanso kutilimbikitsa tikakumana ndi mavuto. (Yoh. 6:44) Yehova amatipatsanso zonse zofunikira kuti tikhale ndi chikhulupiriro cholimba. Iye amatithandizanso kuti tizipeza zinthu zimene timafunikira pa moyo wathu wa tsiku ndi tsiku. (Mat. 6:31, 32) Tikamaganizira chikondi chimene Yehova amatisonyeza, ifenso timayamba kumukonda kwambiri. w21.09 22 ¶8-9
Lachitatu, March 29
Vulani umunthu wakale pamodzi ndi ntchito zake.—Akol. 3:9.
Kodi zinthu zinali bwanji pa moyo wanu musanayambe kuphunzira Baibulo ndi a Mboni za Yehova? Ambirife sitingakonde n’komwe kuti tiziganizira zimenezo. N’kutheka kuti mfundo za m’dzikoli zokhudza chabwino ndi choipa ndi zimene zinaumba umunthu wathu. Ngati ndi choncho, ndiye kuti ‘tinalibe chiyembekezo ndipo tinalibe Mulungu m’dzikoli.’ (Aef. 2:12) Koma mutayamba kuphunzira Baibulo munazindikira kuti muli ndi Atate wanu wakumwamba yemwe amakukondani kwambiri. Munazindikiranso kuti, kuti muzisangalatsa Yehova komanso kukhala m’banja lake la anthu amene amamulambira, muyenera kusintha moyo wanu, mmene mumaganizira komanso mmene mumaonera zinthu. Munkafunika kuphunzira kuti muzichita zinthu mogwirizana ndi mfundo zake zapamwamba. (Aef. 5:3-5) Yehova ndi Mlengi komanso Atate wathu wakumwamba. Choncho ali ndi ufulu wosankha mmene anthu a m’banja lake ayenera kumachitira zinthu. Ndipo iye amafuna kuti tisanabatizidwe, tiyesetse ‘kuvula umunthu wakale pamodzi ndi ntchito zake.’ w22.03 2 ¶1-3
Lachinayi, March 30
Ndili ndi nkhosa zina.—Yoh. 10:16.
A nkhosa zina amasangalala kupezeka pa Chikumbutso monga oonerera ndipo kupezekapo kumawathandiza kuganizira za chiyembekezo chawo. Iwo amayembekezera mwachidwi kumvetsera nkhani ya Chikumbutso yomwe imafotokoza kwambiri zimene Khristu ndi olamulira anzake okwana 144,000 adzachitire anthu okhulupirika mu Ulamuliro wa Zaka 1,000. Motsogoleredwa ndi Mfumu Yesu Khristu, olamulira anzakewa adzathandiza kusintha dzikoli kukhala Paradaiso komanso anthu omvera kuti akhale angwiro. Zimakhalatu zosangalatsa kwa anthu mamiliyoni ambiri omwe amapezeka pa Chikumbutso akamaganizira maulosi a m’Baibulo omwe adzakwaniritsidwe m’tsogolo, monga opezeka pa Yesaya 35:5, 6; 65:21-23 ndi Chivumbulutso 21:3, 4. Akamadziyerekezera ali m’dziko latsopano limodzi ndi okondedwa awo, chiyembekezo chawo cham’tsogolo chimalimba ndipo amatsimikiza mtima kuti asasiye kutumikira Yehova.—Mat. 24:13; Agal. 6:9. w22.01 21 ¶5-7
Kuwerenga Baibulo pa nyengo ya Chikumbutso (Zochitika pa Nisani 9 dzuwa litalowa) Mateyu 26:6-13
Lachisanu, March 31
Mwana wa munthu [anabwera] . . . kudzapereka moyo wake dipo kuwombola anthu ambiri.—Maliko 10:45.
Kodi dipo n’chiyani? Ndi malipiro amene Yesu anapereka powombola zimene Adamu anataya. (1 Akor. 15:22) N’chifukwa chiyani timafunikira dipo? Chifukwa mogwirizana ndi Chilamulo, chilungamo cha Yehova chinkafuna kuti moyo uzilipira moyo. (Eks. 21:23, 24) Adamu anataya moyo wangwiro choncho pofuna kukwaniritsa chilungamo cha Mulungu, Yesu anaperekanso moyo wake wangwiro. (Aroma 5:17) Apatu Yesu anakhala “Atate Wosatha” kwa onse amene amakhulupirira dipo. (Yes. 9:6; Aroma 3:23, 24) Yesu anali wofunitsitsa kupereka moyo wake chifukwa choti amakonda kwambiri Atate wake wakumwamba komanso anthu. (Yoh. 14:31; 15:13) Chikondi chimenechi chinamuthandiza kukhalabe wokhulupirika kwa moyo wake wonse ndi kukwaniritsa chifuniro cha Atate wake. Zimene anachitazi zinathandiza kuti cholinga chimene Yehova anali nacho chokhudza anthu ndi dziko lapansili chidzakwaniritsidwe. w21.04 14 ¶2-3
Kuwerenga Baibulo pa nyengo ya Chikumbutso (Zochitika pa Nisani 9 kutacha) Mateyu 21:1-11, 14-17