Madalitso a Umulungu kwa “Awo Okhala ndi Chidziŵitso”
“Ndipo anthu okhala ndi chidziwitso adzawala ngati kuwala kwa thambo; ndipo awo otembenuzira ambiri ku chilungamo ngati nyenyezi ku nthawi yosatha, ngakhale kwa muyaya.”—DANIELI 12:3, NW.
1. Pambuyo pa kulongosola nthawi yowawitsa pa anthu oyambitsa nkhondo, ndi kuti kumene m’ngelo kenaka akutembenuzira chidwi chake?
ULOSI wa m’ngelowo kwa Danieli watibweretsa tonse a ife kuchokera ku zana lachinayi B. C.E. kufika ku Armagedo. Iwo wasonyeza kuti Mikaeli adzabweretsa mtendere padziko lapansi mnjira imodzi yokha yothekera mwa kuwononga odzetsa nkhondo. Tsopano, pambuyo pa kufufuzafufuza kotsimikizirika mu mbiri pasadakhale, m’ngeloyo akuneneratu ena a madalitso olemera osangalalidwa ndi anthu a Mulungu [“mbali yomalizira ya masiku.” NW]—Danieli 10:14.
Nthawi ya Ziukiriro
2. Kodi ndimotani mmene akufa “akuuka” mkati mwa “mbali yomalizira ya masiku”?
2 M’ngelo akuuza Danieli: “Ndipo padzakhala ambiri a iwo ogona m’fumbi lapansi amene adzauka, awo kumka ku moyo wosatha, ndipo awa kumka ku manyazi ndi [kunyozeka kosatha.” NW] (Danieli 12:2) Mwachiwonekere, “mbali yomalizira ya masiku” iri nthawi kaamba ka ziukiriro, za kuukitsa awo “ogona m’fumbi lapansi.” Kumodzi kwa kuukitsidwa kotero kunayambika mwamsanga pambuyo pakukhala Mfumu kwa Yesu mu 1914. (Mateyu 24:3) Akuyang’ana kutsogolo ku nthawi imeneyo, mtumwi Paulo analemba: “Ife okhala ndi moyo otsalira kufikira kufikanso kwa Ambuye, sitidzatsogolera ogonawo. . . Ndipo akufa mwa Ambuye adzayamba kuuka.” (1 Atesalonika 4:15, 16; Chivumbulutso 6:9-11) Mwachiwonekere, ndiyeno, mwamsanga pambuyo pa 1914 Yesu anaukitsa ku moyo wauzimu kumwamba awo amene anali “a Israyeli wa Mulungu” omwe anali atafa kale okhulupirika. (Agalatiya 6:16) Kwa iwo, kuukako kunali ku “moyo wosatha.”
3, 4. Kodi ndimotani mmene gulu la atumiki okhulupirika a Mulungu linakhalira ‘lakufa’ mu 1918?
3 Koma mawu a m’ngelo mosakaikira akuphatikiza kuuka kwina. Kwa chifupifupi zaka 40 pambuyo pa 1914, gulu laling’ono la Akristu lakhala likuchenjeza kuti chaka chimenecho chikaika chizindikiro kutha kwa Nthawi za Akunja monga kunalosedwera ndi Yesu. (Luka 21:24) Akristu amenewa anakhazikitsa Zion’s Watch Tower Tract Society mu 1884, ndipo anafalitsa zotulukapo za kufufuzafufuza kwawo mu Baibulo mu magazini yotchedwa Zion’s Watch Tower and Herald of Christ’s Presence.
4 Mu 1914 chowonadi cha uthenga wawochinatsimikiziridwa poyera pamene nkhondo yoyamba ya dziko inaulika, ndipo “zowawa” zonenedweratu ndi Yesu zinayamba. (Mateyu 24:7, 8) Mosasamala kanthu za chimenecho, adani awo achipembedzo anagwiritsira ntchito mantha a nkhondo kuzunza iwo kufikira pomalizira, mu 1918, ntchito yawo yolalikira inaimitsidwa, ndipo atumiki odziwika a Watch Tower Society anaikidwa mu ndende mopanda chilungamo. Ichi chinapangitsa chimwemwe chachikulu mu mbali zina. Chinakwaniritsanso ulosi wolembedwa mu bukhu la Chivumbulutso: “Ndipo pamene zidzatsiriza umboni wawo chirombo chokwera kutuluka m’phompho chidzachita nazo nkhondo, nichidzazilaka, nichidzazipha izo.”—Chivumbulutso 11:7.
5, 6. Kodi ndimotani mmene zokumana nazo za gulu limeneli mu 1919 zinaperekera kukwaniritsidwa kwa ulosi wakuti “ambiri a awo ogona m’fumbi lapansi. . . adzauka”?
5 Komabe, malinga ndi ulosiwo, iwo sanayenera kukhala ‘akufa.’ “Ndipo atapita masiku atatu ndi nusu lake mzimu wamoyo wochokera kwa Mulungu unawalowera, ndipo anakhala chiriri, ndipo mantha akulu anawagwera iwo akuwapenya. . . Ndipo anakwera kumka kumwamba mu mtambo; ndipo adani awo anawapenya.” (Chivumbulutso 11:11, 12; Ezekieli 37:1-14) Mwachiwonekere chiukiriro chawo chinali chophiphiritsira, popeza chiukiriro chenicheni ku moyo wauzimu kumwamba chikanakhala chosawoneka kwa adani awo. M’malo mwake, iwo anaukitsidwa kuchokera ku mkhalidwe wonga imfa wakusagwira ntchito kufika ku mkhalidwe wamphamvu wa ntchito yamphamvu mu kapenyedwe kotheratu ka awo amene anapanga mapeto awo. Mu 1919 oyimira a Watch Tower Society anamasulidwa kuchokera ku ndende, ntchito yolalikira inalinganizidwanso, ndipo dziko linawona chiyambi cha ndawala yaikulu koposa ya umboni wa Ufumu mu mbiri.—Mateyu 24:14. ’
6 Mu lingaliro lophiphiritsira, ‘ambiri a awo ogona m’fumbi lapansi anauka.’ Kenaka, kuyambira mu 1919, gulu laling’ono loukitsidwa la Ophunzira Baibulo limenelo linayamba kufunafuna ndi kusonkhanitsa otsalira a abale a Yesu kotero kuti chiwerengero chotheratu cha 144, 000 chiikidwe chizindikiro. (Mateyu 24:31; Chivumbulutso:1-3) Pamene anthu anavomereza, anadzipereka iwo eni kwa Mulungu kupyolera mwa Kristu ndi kukhala amodzi a gulu lowonekala Yehova padziko. Akulandira mphatso yaulere ya mzimu woyera, iwo analalikidwa olungama pa maziko a chikhulupiriro chawo mu nsembe ya dipo ya Yesu ndipo anatengedwa monga ana a Mulungu mnjira ya uzimu.-Aroma 8:16; Agalatiya 2:17; 3:8.
7. Kwa ambiri amenewa, kodi ndimotani mmene ichi chidzatsimikizirira kukhala kuuka “ku moyo wosatha”?
7 Awo amene anakhalabe okhulupirika kufikira kumapeto a moyo wawo wa padziko lapansi ali ndi chiyembekezo champhamvu chakutenga malo awo kumwamba limodzi ndi Yesu Kristu. (1 Akorinto 15:50-53) Chotero, kuuka kwawo kwauzimu kuli ku moyo wosatha. Pamene adakali ndi moyo padziko lapansi, iwo amayang’anizana ndi mtendere pakati pa iwo eni ngakhale kuti akukhala mu dziko lankhondo. (Aroma 14:19) Koma chofunika koposa, iwo amasangalala ndi mtendere ndi Yehova Mulungu iye mwini, “mtendere wa Mulungu wakupambana chidziwitso chonse.”—Afilipi 4:7.
Kuuka “ku Manyazi”
8, 9. Kodi ndi mwanjira yotani mmene kuuka kwauzimu kumeneku kungakhalire “ku manyazi ndi ku kunyozeka kosatha”?
8 Nchifukwa ninji, nanga, ena “amauka . . . ku manyazi ndi kunyozeka kosatha”? Nsonga iri yakuti, si onse amene amalandira chiitano chakukhala mbali ya gulu la Ufumu limenelo amakhala okhulupirika. Ena amalola chikhulupiriro chawo kufooka ndipo amalephera kupirira. (Ahebri 2:1) Ochepera amakhala ngakhale ampatuko ndipo amayenera kuchotsedwa mu mpingo Wachikristu. (Mateyu 13:41, 42) Oterowo alongosoledwa ndi Yesu monga “kapolo woipa” amene Mbuye amulanga “namdula kumuika iye ndi onyenga. “Pomwepo padzakhala kulira ndi kukukuta mano.”—Mateyu 24:48-51; Aefeso 4:18; 5:6-8.
9 Ndi tsoka lotani nanga, kulandira mwawi wapamwamba kwambiri womwe sunaperekedwe nkomwe kwa anthu opanda ungwiro ndipo kenaka kuutaya iwo! Kwa awo amene amachita mwanjira imeneyi, mtumwi Paulo anati: “Pakuti sikutheka kuwakonzanso, atembenuke mtima, iwo amene anaunikidwa pa nthawi yake, nalawa mphatso ya kumwamba, nakhala olandirana naye mzimu woyera, nalawa mawu okoma a Mulungu, ndi mphamvu ya nthawi irinkudza, koma anagwa m’chisokero, popeza adzipachikiranso okha Mwana wa Mulungu, namchititsa manyazi poyera.” (Ahebri 6:4-6) Mu njira imeneyi, kuuka kwawo kumatembenukira kukhala “ku manyazi ndi kunyozeka kosatha.” Iwo alibe chiyembekezo chowonjezereka cha moyo wosatha.
“Kuwala monga Miuni”
10. Kodi ndani amene ali “awo okhala ndi chidziwitso,” ndipo kodi ndimotani mmene iwo ‘akuwalira monga miuni’?
10 Koma kwa awo omwe amakhalabe okhulupirika, ulosiwo ukuti: “Ndipo anthu okhala ndi chidziwitso adzawala ngati kuwala kwa thambo; ndipo awo otembenuzira ambiri ku chilungamo, ngati nyenyezi ku nthawi yosatha, ngakhale kwamuyaya.” (Danieli 12:3, NW) “Anthu okhala ndi chidziwitso” mwachiwonekere ali otsalira okhulupirika a ziwalo zodzozedwa za mpingo Wachikristu, omwe ali ‘odzazidwa ndi chidziwitso cholongosoka cha chifuno chake mu nzeru zonse ndi kumvetsetsa kwauzimu.’ Olimbikitsidwa ndi Yehova, iwo ‘amachitira chipiriro chonse ndi kuleza mtima konse pamodzi ndi chimwemwe, kuyamika Atate amene anawayeretsa iwo kaamba ka kulandira nawo cholowa cha oyera mtima mu kuunika.’ (Akolose 1:9, 11, 12) Kuyambira 1919, ngakhale kuti ‘mdima unaphimba dziko lapansi, ndi mdima wabii wa mitundu ya anthu,’ iwo akhala “akuwala monga miuni” pakati pa mtundu wa anthu. (Yesaya 60:2; Afilipi 2: 15; Mateyu 5:14-16) Iwo “amawalitsa monga dzuwa mu ufumu wa Atate wawo.”—Mateyu 13:43.
11. Kodi ndi m’njira yotani mmene “awo okhala ndi chidziwitso, atsimikizirira kukhala “awo ote mbenuzira ambiri ku chilungamo”?
11 Kodi ndimotani mmene iwo amatsimikizirira kukhala “awo otembenuzira ambiri ku chilungamo”? (Danieli 12:3) Chiyamikiro chipite ku umboni wawo wokhulupirika, omalizira a Israyeli wauzimu asonkhanitsidwa ndi kulalikidwa olungama kaamba ka moyo kumwamba. Mkuwonjezerapo, khamu lalikulu la “nkhosa zina” ladziwonetsera ilo lokha, likumapita ku kuwala kochokera kwa Yehova monga mmene kukuwunikiridwa ndi ‘anthu a Danieli.’ (Yohane 10:16; Zekariya 8:23) “Nkhosa zina” zimenezi modzipereka zagwirizana ndi odzozedwa mu ntchito yawo ya kulalikira “mbiri yabwino”. (Mateyu 24:14; Yesaya 61:5, 6) Iwo, nawonso, amasonyeza chikhulupiriro mu mwazi wokhetsedwa wa Yesu Kristu, kotero kuti iwo akulalikidwa olungama kudzasangalala ndi unansi ndi Mulungu. (Chivumbulutso 7:9- 15; yerekezani ndi Yakobo 2:23. ) Ngati iwo akhala okhulupirika kufika kumapeto, maina awo adzapitirizabe “kupezeka olembedwa m’bukhu.” Chotero, iwo angayembekezere kupulumuka nthawi yowopsya ya nthawi zowawa yomwe idzakantha mitundu.—Danieli 12:1; Mateyu 24:13, 21, 22.
“Iwo Adzawala. . .Kosatha”
12, 13. (a) Kodi ndimotani mmene ziriri kuti “awo okhala ndi chidziwitso” ali okhoza “kuwala . . . kwamuyaya”? (b) Ndimotani, m’njira ina, mmene iwo adzatsimikizirira kukhala “awo otembenuzira ambiri ku chilungamo”?
12 M’ngelo anauza Danieli: “Anthu okhala ndi chidziwitso adzawala ngati kuwala kwa thambo . . . , ngati nyenyezi ku nthawi yosatha, ngakhale kwamuyaya.” (Danieli 12:3) Kodi ndimotani mmene odzozedwa angawalire kosatha, popeza aliyense m’kupita kwanthawi adzafa? Mu chimenecho iwo adzapitiriza “kuwala” ngakhale pambuyo pa imfa. Kuwalongosola iwo mu mkhalidwe wawo wa kumwamba, Yesu akutiuza ife mu bukhu la Chivumbulutso: “Mpando wachifumu wa Mulungu ndi wa Mwanawankhosa udzakhala momwemo; ndipo akapolo ake adzamtumikira iye, nadzawona nkhope yake; ndipo dzina lake lidzakhala pamphumi pawo. Ndipo sikudzakhalanso usiku; ndipo sasowa kuunikira kwa nyali, ndi kuunika kwa dzuwa; chifukwa [Yehova, NW] Mulungu adzawaunikira; ndipo adzachita ufumu ku nthawi za nthawi.”—Chivumbulutso 22: 3-5.
13 Inde, oukitsidwa amenewa adzalamulira monga mafumu ngati nyenyezi m’mwamba, “ku nthawi zosatha ndi kwamuyaya.”Kuwala kwawo kwauzimu kudzabweretsa madalitso a akulu pa mtundu wa anthu. (Chivumbulutso 14:13) Kuwalongosola monga “Yerusalemu Watsopano,” bukhu la Chivumbulutso likusimba: “Ndipo pamzinda sipafunika dzuwa, kapena mwezi wakuuwalira; pakuti ulemerero wa Mulungu uUnikira umenewu, ndipo nyali yake ndiye Mwanawankhosa. Ndipo amitundu adzayendayenda mwa kuunika kwake, ndi mafumu a dziko atenga ulemerero wawo kulowa nawo momwemo.” (Chivumbulutso 21:2, 9, 23, 24) Oukitsidwawo adzathandiza mu kugwiritsira ntchito mapindu a nsembe ya dipo “kaamba ka kuchiritsa amitundu.” (Chivumbulutso 22:2) Pamene, pamapeto a Ulamulirowa Zaka Chikwi, Yesu ndi mafumu ndi ansembe anzake a 144, 000 abwezeretsa anthu okhulupirika ku ungwiro, iwo ndithudi adzakhala atabweretsa “ambiri ku chilungamo.” Pambuyo pa chiyeso chomalizira pa nthawi imeneyo, mtundu wa anthu wobwezeretsedwa udzapanga chitaganya cha anthu angwiro kukhala padziko lapansi la paradaiso ku nthawi yosatha. (Chivumbulutso 20:7-10; Masalmo 37:29) Mu njira imeneyi, zotulukapo zowonekera za ulemerero wa kumwamba wa ‘anthu a Danieli’ zidzakhalanso “ku nthawi yosatha, ngakhale kwamuyaya.”
Chiukiriro China
14. Ulosi wakuti “ambiri a awo ogona m’fumbi lapansi . . . adzauka” udzaphatikizapo ndani enanso?
14 Chotero mawu a m’ngelo amatitenga ife kupyola mu nthawi ya ‘kuimirira’ kwa Mikaeli ndi nthawi yosayerekezereka ya “nthawi zowawa” kufika mu dongosolo la kachitidwe kazinthu katsopano. Mkuwonjezerapo, madalitso odzaperekedwa kupyolera mwa awo owala “ngati nyenyezi” sadzakhala ndi malire kwa awo omwe adzapulumuka “nthaŵi zowawa.” Yesu, pamene anali adakali munthu padziko lapansi, anati: “Ikudza nthawi, imene onse ali m’manda adzamva mawu ake, nadzatulukira, amene adachita zabwino, kukuuka kwa moyo; koma amene adachita zoipa kukuuka kwa kuweruza.” (Yohane 5:28, 29) Mawu amenewa amaloza ku chiukiriro chenicheni cha anthu akufa, ndipo mosakaikira chiukiriro chimenechi, kachiŵirinso, chiri kukwaniritsidwa kofutukulidwa kwa mawu a m’ngelo: “Ambiri a awo ogona m’fumbi lapansi. . . adzauka.”—Danieli 12:2.
15. Kwa awo amene adzaukitsidwa panthawi imeneyo, ndimotani mmene chingatsimikizirire kukhala kuuka ku “moyo wosatha ?
15 Pakati pa awo ophatikizidwa mu kuuka kumeneku padzakhala Danieli iyemwini. Iye anauzidwa ndi m’ngelo: “Koma iwe, muka mpaka chimaliziro; pakuti udzapumula [kugona tulo mu imfa], nudzaima m’gawo lako masiku otsiriza.” (Danieli 12:13) Awo onga Danieli omwe adzaukitsidwa panthawiyo ndi omwe amavomereza ku utumiki wa Yesu ndi abale ake kuchokera kumwamba adzaukitsidwa ku ungwiro wa munthu. Pamene apyola chiyeso chomaliza, maina awo adzalembedwa kotheratu m’bukhu la moyo. (Chivumbulutso 20:5) Kwa iwo kachiwirinso, kuuka kudzakhala “ku moyo wosatha.”
16. Kodi ndi kwa ndani kumene kuuka kwa mu dongosolo la kachitidwe kazinthu katsopano kudzatsimikizirira kukhala “kunyozeka kwamuyaya”?
16 Komabe, sikuti onse adzavomereza motero. Ena mosakaikira adzayesa kubweretsa machitachita omwe akhala akubera munthu mtendere kwanthawi yaitali. Oterowo ali ndi chenjezo labwino mu Baibulo: “Koma amantha, osakhulupirira, ndi onyansa, ndi ambanda, ndi achigololo, ndi olambira mafano, ndi onse a mabodza, cholandira chawo chidzakhala m’nyanja yotentha ndi moto ndi sulfure; ndiyo imfa yachiwiri.” (Chivumbulutso 21:8) “Imfa yachiwiri” imeneyi iri chiweruzo chachindunji chochokera kwa Yehova kuchokera ku chimene kulibe chiukiriro. Iyo iri ya nthawi zonse, kuiwalidwa kopanda mapeto. Awo oukitsidwa omwe adzatsimikizira kukhala osayamikira adzavutika ndi imfa yachiwiri imeneyi; chotero, kuuka kwawo kudzakhala “ku manyazi ndi kunyozeka kosatha.”—Danieli 12:2.
“Chidziŵitso Chowona Chidzachuluka”
17. Kodi ndimotani mmene timadziwira kuti ulosi wonena za mfumu ya kumpoto ndi mfumu ya kum’mwera unalembedwa makamaka kaamba ka phindu lathu lerolino?
17 M’ngeloyo kenaka akupereka mawu auphungu kwa Danieli: “Ndipo ponena za iwe, 0 Danieli usaulule mawu ndipo matira bukhulo, kufikira nthawi ya mapeto. Ambiri adzayendayenda, ndipo chidziwitso chowona chidzachuluka.” (Danieli 12:4) Mawu amenewa amagwira chidwi chathu. Ngakhale kuti ulosi wa m’ngelowo ponena za mafumu awiri unayamba kukwaniritsidwa zaka 2, 300 zapita, kumvetsetsa kwa iwo kwakhala kutatsegulidwa choyambirira mkati mwa “nthawi za mapeto,” makamaka kuyambira 1919. Mu masiku awa, “ambiri . . . amayendayenda” mu Baibulo, ndipo chidziwitso chowona chachulukadi. Tsopano iri nthawi pamene Yehova wapereka chidziwitso kwa ozindikira.
18. (a) Kodi ndi mbali zazikulu ziti za ulosi zimene zikukwaniritsidwa tsopano kapena ziri pafupi kukwaniritsidwa? (b) Kodi ndi kawonedwe kolinganizika kotani kamene ichi chimatipatsa ife?
18 Chenicheni chakuti mbali zochuluka za ulosiwo zinakwaniritsidwa zaka zana zapita chimatumikira kulimbikitsa chikhulupiriro chathu mu mbali za ulosi zomwe zidzatenga mbali. (Yoswa 23:14) Dziko lerolino lalowetsedwa mu mkhalidwe wa nkhondo pakati pa mfumu ya kumpoto ndi mfumu ya kum’mwera, monga mmene m’ngeloyo ananeneratu. Mkuwonjezera, ulosiwo ukuchenjeza ngakhale ponena za nthawi zowopsya kwambiri mtsogolo. Chotero tikuthandizidwa kusunga kulinganizidwa kwathu ndi kupewa kukokedwa ndi chisonkhezero cha iriyo nse ya mafumuwo. Iyi iri nthawi ya kulimbikitsa chidaliro chathu mwa Yehova. Musai wale nkomwe kuti “Mikaeli . . . kalonga wamkulu” “akuimirira” kaamba ka anthu ake. Chipulumutso chathu chokha chotsimikizirika chiri mwa kugonjera ku Ufumu wa Mulungu pansi pa Kristu Yesu.—Machitidwe 4:12; Afilipi 2:9-11.
19. Kodi ndi kufunika kotani kumene mawu a m’ngelo kwa Danieli ali nako kwa aliyense wa ife?
19 Chotero, khalani pafupi, ndi “awo okhala ndi chidziwitso,” omwe ‘akuwala ngati kuwala kwa thambo.’ Khalani okangalika mu kugwira ntchito kaamba ka Ufumu wa Mulungu. (1 Akorinto 15:58; Aroma 15:5, 6) Zamitsani chikondi chanu cha Mawu a Mulungu, ndipo yamikirani mozama mtendere womwe ulipo ngakhale tsopano mu gulu la Mulungu. (Masalmo 119:165; Aefeso 4: 1-3; Afilipi 2:1-5) Kenaka, pamene Mikaeli “adzaimirira’ kuphwanya adani a Yehova, lolani kuti mupulumuke pamodzi ndi onse a anthu a Mulungu amene maina awo “akupezeka olembedwa m’bukhu.”
Kodi Mungayankhe?
◻ Ndi m’njira yotani mmene kwakhalira kale kuukitsidwa kwa “ambiri a awo ogona m’nthaka?”
◻ Kodi ndimotani mmene ‘kuukitsidwa’ kumeneku kungatembenukirire kukhala “ku manyazi”?
◻ Kodi ndimotani mmene “awo okhala ndi chidziwitso“ amawalira monga miuni ndi kutembenuzira ambiri ku chilungamo?
◻ Kodi ndi kukwaniritsidwa kwa mtsogolo kotani kumene kudzakhalapo ponena za kuwuka kwa ‘awo ogona m’nthaka’?
◻ Kodi ndimotani mmene Danieli 12:4 akukwaniritsidwira?
[Chithunzi patsamba 23]
Kuyambira 1919 awo okhala ndi chidziwitso akhala monga nyenyezi zowala akuunikira chowonadi chopatsa moyo
Mawu a Chithunzi
NASA photo