CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MATEYU 1-3
“Ufumu Wakumwamba Wayandikira”
Zovala za Yohane zinkasonyezeratu kuti ankakhala moyo wosalira zambiri komanso kuti anali wodzipereka pochita chifuniro cha Mulungu
Yohane anali ndi mwayi wapadera kwambiri wogwira ntchito yodziwitsa anthu za kubwera kwa Yesu
Kukhala ndi moyo wosalira zambiri kungatithandize kuti tizichita zochuluka potumikira Mulungu ndipo tingamakhale osangalala. Kuti tikhale ndi moyo wosalira zambiri tiyenera . . .
kuzindikira zinthu zomwe ndi zofunikadi
kusiya kugula zinthu zosafunika kwenikweni
kulemba bajeti
kuchotsa zinthu zimene sitizigwiritsa ntchito
kulipira ngongole zonse
kuchepetsa nthawi imene timagwira ntchito
Kodi ndingakwaniritse cholinga chiti ngati nditamakhala moyo wosalira zambiri?