Mutu 11
Yesu Atiphunzitsa Ife Kupemphera
KODI inu mumalankhula ndi Yehova Mulungu?—Iye amakufunani inu kulankhula kwa iye. Pamene inu mulankhula ndi Mulungu, kumeneku kumachedwa pemphero.
Yesu kawirikawiri analankhula ndi Atate wache wa kumwamba. Nthawi zina iye anafuna kukhala yekha pamene iye analankhula ndi Mulungu. Nthawi ina, Baibulo limati: “anakwera m’phiri pa yekha, kukapemphera: ndipo pamene panali madzulo, Iye anakhala kumeneko yekha.”—Mateyu 14:23.
Kodi mungapite kuti kukapemphera kwa Yehova muli nokha?—Mwinamwache mungalankhule ndi Mulungu nokha musanapite kogona usiku. Yesu anati: “Pamene inu mupemphera, lowani m’chipinda chanu chanokha ndipo, mutatseka chitseko chanu, pempherani kwa Atate wanu.” Kodi inu mumapemphera kwa Mulungu usiku uli wonse musanapite kogona?—Chiri chinthu chabwino kuchichita—Mateyu 6:6, NW.
Yesunso anapemphera pamene anthu ena anali limodzi naye. Pamene iye anali ndi misonkhano limodzi ndi ophunzira ache, Yesu ankapemphera. Inu mungathe kupita ku misonkhano Yachikristu kumene pemphero limaperekedwa. Pa misonkhano imeneyi kawirikawiri munthu wachikulire adzapemphera. Mvetserani mosamalitsa zimene iye amazinena, chifukwa chakuti iye ali kumalankhula ndi Mulungu kaamba ka inu. Pamenepo inu mudzakhala wokhoza kunena kuti “Amen” ku pempherolo.
Kodi mukuchidziwa chimene chimatanthauzidwa pomati “Amen” pa mapeto a pemphero?—Kumatanthauza kuti inu mukulikonda pempherolo. Iko kumatanthauza kuti inu mukugwirizana nalo, ndi kuti inu mukulifuna ilo kukhala pemphero lanunso.
Yesu anapempheranso pa nthawi za chakudya. Iye anamthokoza Yehova kaamba ka chakudya chache. Kodi inu masiku onse mumapemphera musandye zakudya zanu?—
Kuli bwino kaamba ka ife kumthokoza Yehova kaamba ka chakudya ife tisanayambe kudya. Atate wanu angalipereke pemphero pamene mukudya limodzi. Koma bwanji ngati inuyo mukudya nokha? Kapena bwanji ngati inu muli kudya chakudya ndi anthu amene samamthokoza Yehova?—Pamenepo inuyo mufunikira kulipereka pemphero lanu.
Kodi inu masiku onse mufunikira kupemphera mopfuula?—Ai. Yehova angathe kulimva pemphero lanu ngakhale ngati inu mulipereka ilo mu mtima mwanu. Chotero inu mungathe kulipereka pemphero lakachetechete kwa Yehova pamene inu muli limodzi ndi anthu amene samapemphera kwa Mulungu. Mwachitsanzo, inu mungapereke pemphero lakachetechete pamene inu mukudya chakudya cha masana pa sukulu.
Kodi muyenera kuweramitsa mutu wanu pamene mukupemphera? Kodi muyenera kugwada pansi? Kodi mukuganiza bwanji?—
Nthawi zina Yesu anapinda maondo ache pamene iye anapemphera. Nthawi zina ankakweza mutu wache kuyang’ana kumwamba pamene iye anapemphera. Ndipo iye analankhulanso za kumapemphera kwa Mulungu uli chiimire.
Chotero kodi chimenechi chimasonyeza chiani? Kodi inuyo masiku onse mufunikira kukhala mu mkhalidwe umodzimodziwo pamene mukupemphera?—Mkhalidwe umene inuyo muli siuli chinthu chofunika. Koma nthawi zina kuli bwino kuweramitsa mutu wanu. Pa nthawi zina mungafunenso kugwada pansi monga anachitira Yesu. Koma, kumbukirani kuti, ife tingathe kupemphera kwa Mulungu pa nthawi iri yonse mkati mwa tsiku kapena usiku ndipo iye adzatimva ife.
Chinthu chofunika m’pemphero ndicho chakuti ife timakhulupiliradi kuti Yehova ali kumvetsera. Kodi inu mumakhulupilira kuti Yehova amakumvani?—
Kodi nchiani chimene ife tiyenera kuchinene m’mapemphero athu kwa Yehova?—Ndiuzeni: Pamene inuyo mukupemphera, kodi mumalankhula za chiani kwa Mulungu?—
Yehova amatipatsa ife zinthu zabwino zambirimbiri, ndipo kuli koyenera kumthokoza iye kaamba ka izo, kodi sichoncho?—Ife timamthokoza iye kaamba ka chakudya chimene ife timadya. Koma kodi munayamba mwamthokoza iye kaamba ka thambo lobiriwiralo, mitengo yobiriwira ndi maluwa okongolawo?—Iye anazipanganso zimenezo.
Ophunzira a Yesu pa nthawi ina anampempha iye kuwaphunzitsa iwo kupemphera. Ndipo Mphunzitsi Wamkuruyo anawasonyeza iwo zimene zinali zinthu zofunika kuzipemphelera. Kodi inu mukuzidziwa zimene ziri zinthu zimenezi?—Tengani Baibulo lanu ndi kulitsegula ilo pa Mateyu chaputara 6. Mu vesi 9 kufikira 13 timachipeza chimene anthu ambiri amachicha “Pemphero la Ambuye.” Tiyeni tiliwerenge ilo limodzi.
Panopo ife tikuphunzira kuti Yesu anatiuza ife kupemphera ponena za dzina la Mulungu. Iye anati tipemphere kuti dzina la Mulungu liyeretsedwe kapena lionedwe monga loyera. Kodi dzina la Mulungu ndani?—Baibulo limatiuza ife kuti ilo ndilo Yehova, ndipo tiyenera kulikonda dzina limenelo.
Chachiwiri, Yesu anatiphunzitsa ife kupempha ufumu wa Mulungu kuti udze. Ufumu umenewu uli wofunika kwambiri chifukwa chakuti uwo udzadzetsa mtendere ku dziko lapansi ndi kulipanga ilo kukhala paradaiso.
Chachitatu, Mphunzitsi Wamkuruyo anati tipemphelere chifuniro cha Mulungu kuti chichitidwe pa dziko lapansi monga momwe icho chachitidwira kumwamba. Chimenecho chimatanthauza kuti ife tiyenera kuchita chifuniro cha Mulungu.
Yesu anatiphunzitsanso ife kupemphelera chakudya chimene tikuchifuna kaamba ka tsikulo. Ndipo iye ananena kuti ife tiyenera kumuuza Mulungu kuti ife tiri ndi chisoni pamene ife timazichita zinthu zimene ziri zolakwa. Ife tiyenera kumpempha Mulungu kutikhululukira. koma iye asanatikhululukire, ife tiyenera kuwakhululukira ena ngati iwo atilakwira ife. Kodi inuyo mumachichita chimenecho?—
Chotsirizira, Yesu anati, ife tiyenera kupempha kuti Yehova Mulungu adzatitetezera ife kwa woipayo, Satana Mdierekezi. Chotero, zonsezi ziri zinthu zabwino za kuzipempha kwa Mulungu.
Ife tiyenera kukhulupilira kuti Yehova amawamva mapemphero athu ndipo ife tiyenera kupitirizabe kumamthokoza iye, kuphatikiza pa kumampempha iye kutithandiza ife. Yehova amakonda kutimva ife tikumampempha iye. Iye ali wokondwa pamene ife timachitanthauza chimene ife timachinena m’pemphero ndi pamene ife timpempha iye zinthu zoyenera. Ndipo iye adzatipatsa ife zinthu zimenezi. Kodi mukuchikulupilira chimenecho?—
(Uphungu wabwino woojezereka wonena za pemphero ukupezeka pa 1 Petro 3:12, 1 Yohane 5:14 ndi Aroma 12:12.)