Mbiri ya Moyo Wanga
Tinamuyesa Yehova
YOSIMBIDWA NDI PAUL SCRIBNER
“MWADZUKA bwanji mayi Stackhouse. Ine ndikulemba mayina a ofuna makeke a Isitala. Ndiganiza kuti inu ndi banja lanu mungaifune.” Munali mu 1938 m’chilimwe, ku Atco New Jersey, U.S.A., ndipo ndinkalankhula ndi mmodzi wa makasitomala athu akuluakulu pamene ndinali kugulitsa buledi wa kampani ya General Baking. Ndinadabwa kwambiri pamene mayi Stackhouse anakana.
“IWO anati: “Sindikuwafuna makekewo. Ife sitikondwerera Isitala.”
Ndinasoŵa chonena. Sakondwerera Isitala? N’zoona kuti mfundo yoyamba pamalonda imati maganizo a ogula n’ngolondola nthaŵi zonse. Tsono nditani? Kenako ndinati: “Chabwino, ndi keke yabwino kwambiri, ndipo ndikudziŵa kuti m’makonda zinthu zathu. Koma simukuganiza kuti mungakondwere nayo ngakhale kuti simukondwerera Isitala?”
Poyankha, anabwerezanso kuti: “Ayi bambo Scribner, koma ndimafuna kukuuzani zinazake mwina uwu ndi mwayi wanga.” Zomwe tinakambirana pamenepo zinasinthiratu moyo wanga! Mayi Stackhouse omwe anali m’Gulu (kapena mpingo) wa Mboni za Yehova wa Berlin, New Jersey, anandifotokozera chiyambi cha chikondwerero cha Isitala, n’kundipatsa timabuku titatu. Mitu ya timabukuto inali; Safety, Uncovered ndi Protection. Ndinapita nato kunyumba timabukuto ndili ndi chidwi komanso timantha pang’ono. Zimene mayi Stackhouse anandiuza zinali zofananako ndi zimene ndinamvapo ndili mwana.
Kudziŵana Ndi Ophunzira Baibulo Koyamba
Ndinabadwa pa January 31, 1907, ndipo mu 1915, ndili ndi zaka zisanu ndi zitatu, bambo anga anamwalira ndi matenda a kansa. Choncho ine ndi amayi tinakakhala ndi makolo awo m’nyumba yaikulu ku Malden, Massachusetts. Amalume anga a Benjamin Ransom ndi akazi awo, ankakhalanso komweko. A Ben anali kusonkhana ndi Ophunzira Baibulo Apadziko Lonse, amene tsopano ndi Mboni za Yehova. Anayamba kusonkhana nawo kale tisanafike m’zaka za m’ma 1900. Ndinkawakonda kwambiri amalumewo, koma ena onse m’banja lawo omwe anali a tchalitchi cha Methodist, sankakondwera nawo. Patapita zaka, akazi awo anathetsa ukwati. Koma asanatero, anawapititsa kuchipatala cha amisala chifukwa cha zikhulupiriro zawo zachipembedzo. Madokotala atapeza kuti a Ben analibe vuto lililonse, anawapepesa ndi kuwatulutsa.
Malumewo ankanditenga popita kumisonkhano ya Ophunzira Baibulo Apadziko Lonse ku Boston, makamaka kukabwera alendo odzakamba nkhani ndi pazochitika zapadera. Tsiku lina, mlendo wodzakamba nkhani anali Charles Taze Russell, yemwe anali woyang’anira ntchito yolalikira masiku amenewo. Tsiku linanso chochitika chapadera chinali “Seŵero la Pakanema la Chilengedwe.” Ngakhale kuti n’kalekale mu 1915, ndikukumbukirabe bwino Abrahamu atatenga Isake kukwera naye phiri kukam’pereka nsembe. (Genesis, chaputala 22) Ndimaonabe Abrahamu ndi Isake akukwera phirilo ndi mtolo wa nkhuni, Abrahamu atasiya zonse m’manja mwa Yehova. Poti ndinalibe atate, zinandichititsa chidwi kwambiri.
Kenako a Ben ndi akazi awo anasamukira ku Maine. Amayi anakwatiwanso ndipo tinasamukira ku New Jersey. Choncho sindinaonanenso ndi a Ben kwa nthaŵi yaitali. Pamene ndinali kamnyamata ku New Jersey, ndinakumana ndi Marion Neff. Iye anali wochokera m’banja la ana asanu ndi atatu la mpingo wa Presbyterian komwe ndinkakonda kupitako kukacheza. Ndinkakonda kucheza kumeneko ndi kagulu ka achinyamata a tchalitchi chawo pafupifupi Lamlungu lililonse. Ndipo mapeto ake ndinaloŵa tchalitchi cha Presbyterian. Komabe ndinkakumbukira zimene ndinaphunzira pamisonkhano ya Ophunzira Baibulo. Ine ndi Marion tinakwatirana mu 1928 ndipo mu 1935 ndi mu 1938 tinabereka ana aakazi Doris ndi Louise. Pokhala ndi ana aang’ono m’banja lathu, tinaona kuti n’kofunika malangizo auzimu polera anawo.
Kupeza Choonadi M’timabuku Tija
Ine ndi Marion tinkafunafuna tchalitchi choti tiloŵe. Ndiye tinagwirizana kuti, Lamlungu lililonse, wina azikhala pakhomo ndi ana ndipo wina azipita kukafufuza tchalitchi. Lamlungu lina, Marion anali wokhala panyumba, koma ine ndinadzipereka kukhala ndi ana kuti ndiŵerenge kabuku kakuti Safety koyamba pa mabuku atatu aja omwe mayi Stackhouse anandipatsa. Nditayamba kuliŵerenga, sindinathe kulekeza. Popitiriza kuŵerenga, ndinazindikira kuti palibe tchalitchi chomwe chikanandiphunzitsa zimenezo. Lamlungu lotsatiralo ndinachitanso chimodzimodzi podzipereka kulera ana pakhomo kuti ndiŵerenge buku lachiŵiri lakuti Uncovered. Zomwe ndinali kuŵerenga sizinali zachilendo kwenikweni. Kodi n’zimene ankakhulupirira malume a Ben aja? A m’banja lathu ankaona kuti chipembedzo chimenecho si chabwino. Kodi Marion aganiza bwanji? Koma panalibe chifukwa chodandaulira. Patapita masiku ochepa chabe nditaŵerenga buku lakuti Uncovered, Marion anandidabwitsa. Tsiku lina n’tangofika kuchokera kuntchito, iye anati: “Ndaŵerenga mabuku omwe munabweretsa aja, n’ngosangalatsa bwanji!” Atatero ndinamasuka ndithu.
Kumapeto kwa timabukuto kunali chidziŵitso cha buku lina latsopano lomwe linadzudzula mwamphamvu chipembedzo chonyenga lotchedwa Enemies. Tinagwirizana kuti tiliitanitse. Koma tisanatumize pempho lathu, munthu wina wa Mboni anagogoda pachitseko n’kutipatsa bukulo. Buku limeneli linatithandiza kwambiri kusankha choyenera kuchita. Tinaleka kupita kumatchalitchi osiyanasiyana koma kuyamba kusonkhana ndi Gulu la Mboni za Yehova la Camden, New Jersey. Patapita miyezi yochepa chabe, Lamlungu pa July 31, 1938, anthu pafupifupi 50, tinasonkhana pakapinga, kunyumba ya mlongo Stackhouse, kuja ndinkafuna kugulitsako makeke a Isitala. Kumeneko tinamvetsera kaseti ya nkhani ya ubatizo yomwe Woweruza Rutherford anakamba. Kenako tinaloŵa m’nyumba n’kusintha zovala ndipo anthu 19 tinabatizidwa mu mtsinje womwe unali pafupi.
Kutsimikiza Mtima Kukhala Mpainiya
N’tangobatizidwa, mlongo wina mu mpingowo anandiuza za anthu otchedwa apainiya amene amasankha kulalikira kukhala ntchito yawo yaikulu. Nthaŵi yomweyo ndinachita chidwi ndipo posapita nthaŵi ndinadziŵana ndi banja lina lomwe onse m’banjamo anali apainiya. Mbale wina wachikulire dzina lake Konig, mkazi wake, ndi mwana wawo wamkazi anali apainiya mu mpingo woyandikana ndi wathu. Monga tate wa banja laling’ono, ndinachita chidwi kwambiri ndi chimwemwe chimene banja la a Konig linali nacho mu utumiki. Kaŵirikaŵiri ndinkadzera kunyumba kwawo pagalimoto ya kuntchito n’kulalikira nawo pang’ono kunyumba ndi nyumba. Kenako ndinafuna kukhala mpainiya. Koma zimenezi zikanatheka bwanji? Ine ndi Marion tinali ndi ana aŵiri ang’onoang’ono ndipo ntchito yanga inali yotangwanitsa kwambiri. Pamene nkhondo yachiŵiri yapadziko lonse imayamba ku Ulaya, achinyamata ambiri anali kuloŵa usilikali ku United States. Choncho panali ntchito zambiri zofuna ife otsalafe. Kuntchito, ankandipempha kuti ndiwonjezere madera omwe ndinkagulitsa katundu, ndiye ndinadziŵa kuti sindingathe kuchita upainiya ndi ntchito ya mtunduwu.
Nditauza mbale Konig za cholinga changa cha upainiya iye anati: “Pitirizani kutumikira Yehova mwakhama ndi kumamuuza cholinga chanucho m’pemphero. Adzakuthandizani kuchikwaniritsa.” Ndinachita zimenezo koposa chaka chathunthu. Kaŵirikaŵiri ndinkalingalira malemba monga Mateyu 6:8, lomwe limatitsimikizira kuti Yehova amadziŵa zosowa zathu ngakhale tisanam’pemphe. Ndinkayesetsa kutsatira mawu a pa Mateyu 6:33, kufunafuna Ufumu wa Mulungu choyamba ndi chilungamo chake. Nayenso mbale Melvin Winchester yemwe anali mtumiki wadera (tsopano woyang’anira dera), anandilimbikitsa kwambiri.
Ndinamuuza Marion zolinga zangazo. Tinakambirana mawu a pa Malaki 3:10, omwe amatilimbikitsa kumuyesa Yehova ndi kuona ngati sadzatikhuthulira madalitso. Zomwe anayankha zinandilimbikitsa. Iye anati: “Ngati mukufuna kuchita upainiya, musalephere chifukwa cha ine. Ndikhoza kusamalira anaŵa inu mukuchita upainiya. Ndiponso sitifunikira zinthu zambiri.” Pazaka zonse 12 zomwe tinali m’banja, ndinkadziŵa kuti Marion ndi mkazi wosawononga zinthu ndiponso wosamala kwambiri. M’zaka zonse 60 zomwe takhala mu utumiki wanthaŵi zonse, wakhala mpainiya mzanga wokondweretsa. Chimodzi mwa zinsinsi zake n’chakuti amakhutira ndi zinthu zochepa ndi kuzipanga kuoneka ngati zambiri.
Pofika m’chilimwe mu 1941, ine ndi Marion tinasunga ndalama ndi kugula kalavani ya mamita asanu ndi theka kuti tizikhalamo. Tinali titakonzekera mwapemphero kwa miyezi yambiri. Mu 1941, ndinasiya ntchito n’kuyamba upainiya wanthaŵi zonse ndipo ndakhala mu utumiki wanthaŵi zonse mpaka lero. Gawo langa loyamba linali malo khumi pamsewu Nambala 50 pakati pa New Jersey ndi St. Louis, Missouri, komwe tinali kukonzekera kukachitirako msonkhano kumayambiriro kwa August. Ananditumizira mayina ndi maadiresi a abale a m’mphepete mwa msewu ndipo ndinawauziratu tsiku limene ndidzafika kwawoko. Kumsonkhanoko, ndinkafunika kukapita ku ofesi ya apainiya kuti akandipatse gawo lina.
“Ndimuyesa Yehova”
Tinalongedza mabuku m’kalavani yathu kupita komaliza ku msonkhano ku Camden kukatsanzikana ndi abale. Ndi ana aŵiri ang’onong’ono, ndiponso osadziŵa kumene tikapita msonkhano ukakatha, abale ena anakayikira ngati zimenezi zinali zoyenera ndipo ambiri anati: “Mukabwererako posachedwa.” Ndikukumbukira kuti ndinati: “Sindikukana kuti ndikabwerako. Yehova anati andisamala, ndipo ndimuyesa.”
Patapita zaka 60 tikuchita upainiya m’matauni 20 kuchokera ku Massachusetts mpaka ku Mississippi, taonadi kuti Yehova wachita zoposa kukwaniritsa lonjezo lake. Madalitso omwe watikhuthulira, ine, Marion ndi ana athu aakazi aŵiri, sitinawayembekezere n’komwe mu 1941. Ena mwa madalitsowo ndi akuti ana athu ndi apainiya okhulupirika m’mipingo yapafupi, ndiponso (pomaliza pake) tili ndi ana auzimu aamuna ndi aakazi pafupifupi 100 m’madera a m’mphepete mwa nyanja kum’maŵa kwa United States. Ine ndaphunzira Baibulo ndi anthu 52 omwe anapereka miyoyo yawo kwa Yehova Mulungu ndipo Marion waphunzira ndi anthu 48.
Mu August 1941, tinapita ku St. Louis, komwe ndinakumana ndi mbale T. J. Sullivan wa ku Beteli. Anali ndi kalata yanga yosonyeza kuti ndine mtumiki wa chipembedzo yofunika panthaŵi ya nkhondo yomwe inali pafupi kuyamba popewa kukakamizidwa kulowa usilikali. Ndinauza mbale Sullivan kuti mkazi wanga amalalikiranso kwa nthaŵi yofanafana ndi ine ndipo akufuna kukhala mpainiya. Ngakhale kuti ofesi ya apainiya inali isanakhazikitsidwe pamsonkhanopo, mbale Sullivan anavomereza Marion nthaŵi yomweyo monga mpainiya. Kenako anatifunsa kuti: “Mukachitira kuti upainiya msonkhano ukatha?” Sitinkadziŵa. Ndiye anati: “Musadandaule, mukumana ndi munthu wina pamsonkhanowu wa komwe kukufunika apainiya ndipo mupita kumeneko. Mutilembere kalata yotiuza kumene muli ndipo tidzakulemberani kalata yokudziŵitsani kumene muzikatumikira.” N’zimene zinachitika. Mbale Jack DeWitt yemwe kale anali mtumiki wadera ankadziŵa anthu ena a ku New Market, ku Virginia omwe anali ndi nyumba ya apainiya, ndipo ankafuna apainiya ena. Choncho msonkhano utatha, tinanyamuka kupita ku New Market.
Ku New Market, kunachitika zosangalatsa kwambiri. Benjamin Ransom anabwera kuchokera ku Philadelphia kudzakhala nafe monga mpainiya. Inde, malume aja, a Ben! Zinali zosangalatsa kwambiri kugwira nawo ntchito yolalikira ku nyumba ndi nyumba patapita zaka zoposa 25 kuchokera pamene anadzala mbewu za choonadi mu mtima mwanga ku Boston. Ngakhale kuti sanakondedwe ndiponso ananyozedwa ndi kuzunzidwa ndi abale awo, a Ben sanasiye kukonda Yehova ndi kum’tumikira.
Tinakhala limodzi mosangalala kwa miyezi isanu ndi itatu pa nyumba ya apainiya ya New Market. Panthaŵiyo tinaphunziranso kusinthanitsa mabuku ndi nkhuku kapena mazira. Kenako ine, Marion, malumewo, ndi anthu ena atatu, tinatumizidwa kukachita upainiya wapadera ku Hanover, Pennsylvania. Ili linali gawo lathu loyamba mwa magawo asanu ndi limodzi omwe tinakhala nawo ku Pennsylvania kuchokera mu 1942 mpaka mu 1945.
Apainiya Apadera M’nthaŵi ya Nkhondo Yachiŵiri Yadziko Lonse
Nthaŵi zina nkhondo yachiŵiri yadziko lonse ili m’kati, tinkakumana ndi mavuto chifukwa chosaloŵerera nkhondo, koma Yehova sanalephere kutithandiza. Nthaŵi ina tili ku Provincetown ku Massachusetts, galimoto yathu ya mtundu wa Buick inawonongeka. Choncho ndinayenda pansi mtunda wautali m’dera lomwe munali Akatolika achiwawa kwambiri popita komwe ndinalalikirako kale. Ndinakumana ndi gulu la anyamata achipongwe omwe anandizindikira n’kuyamba kundikuwiza. Powanyalanyaza, ndinangoyenda ndawala, miyala yomwe anyamatawo ankaponya ikudutsa pafupi ndi mutu wanga, ubwino wake sanali kunditsatira. Ndinafika kunyumba kwa munthu wachidwi kuja osavulazidwa. Koma mwininyumbayo, yemwe anali wolemekezeka m’gulu lankhondo la America, anandipepesa nati: “Sinditha kucheza nanu, chifukwa ndinaiŵala kuti tipita kukaonera kanema madzulo ano.” Ndinachita mantha pokumbukira gulu la anyamata amandigenda aja, omwe ankandidikira kuti ndibwerere. Komabe ndinasangalala pamene munthuyo anati: “Bwanji tiyendere limodzi? Tikhoza kukambirana m’njira.” Choncho tinayendera limodzi kudutsa anyamata aja bwinobwino ndikumuuza choonadi.
Kusamalira Banja ndi Utumiki
Nkhondo itatha, tinagwira ntchito zingapo ku Virginia ndiponso upainiya wa nthaŵi zonse ndi wapadera kwa zaka 8 ku Charlottesville. Pofika mu 1956 atsikana aja anali atakula ndi kukwatiwa. Koma ine ndi Marion tinali kuyendayendabe pokhala apainiya ku Harrisonburg, Virginia, ndiponso apainiya apadera ku Lincolnton, kumpoto kwa Carolina.
Mu 1966 ndinakhala woyang’anira dera, kuyendera mpingo ndi mpingo kulimbikitsa abale monga mmene mbale Winchester anandilimbikitsira kalekale m’ma 1930 ku New Jersey. Kwa zaka ziŵiri ndinali woyang’anira dera ku Tennessee. Kenako ine ndi Marion tinapemphedwa kuyambanso ntchito yathu yokondedwa ya upainiya wapadera. Kuchokera mu 1968 mpaka mu 1977, tinali apainiya apadera kumwera kwa United States kuchokera ku Georgia mpaka ku Mississippi.
Ku Eastman, Georgia, ndinakhala woyang’anira wampingo (tsopano wotchedwa wong’anira wotsogolera) mmalo mwa mbale wokondedwa wachikulire Powell Kirkland yemwe anali woyang’anira dera kwa zaka zambiri koma tsopano analibe thanzi labwino. Anali wokondwa ndi wothandiza kwambiri. Thandizo lake linali lofunika chifukwa mumpingowo munali mikangano ndipo anthu ena odziwika anakhudzidwa. Mkanganowo unakula kwambiri ndipo nthaŵi zambiri ndinali kupemphera kwa Yehova. Ndinakumbukira Malemba monga Miyambo 3:5, 6: “Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, osachirikizika pa luntha lako; um’lemekeze m’njira zako zonse, ndipo Iye adzawongola mayendedwe ako.” Poyesetsa kukambirana momasuka, tinabwezeretsa mgwirizano mu mpingowo ndipo zotsatira zake zinali zabwino kwa aliyense.
Pofika mu 1977, tinaona kuti tikukalamba, ndiye anatisamutsira ku dera la Charlottesville kumene kunali ana athu aŵiri aja ndi mabanja awo. N’zosangalatsa kwambiri kuti kwa zaka 23, takhala tikugwira ntchito m’derali kuthandiza kukhazikitsa mpingo wa Ruckersville,Virginia, ndi kuona ana ndi adzukulu a anthu omwe tinaphunzira nawo Baibulo poyambirira akukhala akulu, apainiya, ndi otumikira pa Beteli. Ine ndi Marion, tikutsatirabe ndandanda ya ulaliki, ndipo ndili ndi mwayi wotumikira monga mkulu mu mpingo wa East Congregation ku Charlottesville, kuchititsa phunziro la buku ndi kukamba nkhani za anthu onse.
M’zaka zonsezi, takumana ndi mavuto monga mmene aliyense amakhalira. Mwachitsanzo, ngakhale kuti tinayesetsa, Doris anafooka mwauzimu kwa kanthaŵi ali mtsikana n’kukwatiwa ndi munthu yemwe sanali Mboni. Koma sanasiye kutumikira Yehova, ndipo mwana wake Bill wakhala akutumikira pa Beteli ku Wallkill, New York kwa zaka 15. Doris ndi Louise ndi akazi amasiye tsopano, koma akusangalala ndi upainiya wanthaŵi zonse chapafupi ndi ife.
Zomwe Taphunzira M’zaka Zonsezi
Ndaphunzira kugwiritsa ntchito malangizo ochepa osavuta ofunika potumikira Yehova akuti: Musafune zambiri pamoyo wanu. Sonyezani chitsanzo chabwino m’zochita zanu, ngakhale zokhudza moyo wanu weniweni. Gwiritsani ntchito malangizo a “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” pa chilichonse.—Mateyu 24:45.
Marion anapeza njira zochepa koma zothandiza za mmene munthu angapangire upainiya pamene akulera ana: Konzani ndi kutsatira ndandanda yoyenera. Upainiya ukhale ntchito yanu yeniyeni. Muzidya chakudya cha magulu. Muzipuma mokwanira. Musachite zosangalatsa mopyola muyeso. Pangitsani choonadi ndi mbali zonse za utumiki kukhala zosangalatsa kwa ana anu. Pangitsani ntchito yolalikira kuwasangalatsa nthaŵi zonse.
Tsopano tili ndi zaka zoposa 90. Papita zaka 62 kuchokera pamene tinamvetsera nkhani yaubatizo wathu pakapinga kunyumba ya a Stackhouse, ndipo takhala mu utumiki wanthaŵi zonse zaka 60. Ine ndi Marion tinganene moona mtima kuti takhutira kwambiri ndi moyo wathu. Ndikuthokoza kwambiri malangizo amene ndinalandira a kukhala ndi zolinga zauzimu choyamba ndi kuyesetsa kuzikwaniritsa ndili bambo wachinyamata, ndipo ndikuthokoza mkazi wanga wokondeka Marion, ndi atsikana athu pondithandiza zaka zonsezi. Ngakhale kuti sindife olemera, kaŵirikaŵiri ndimagwiritsa ntchito lemba la Mlaliki 2:25: ‘Ndani angadye ndi kumwa kuposa ine?’
Ndithudi, kwa ife, Yehova wakwaniritsadi lonjezo lake la pa Malaki 3:10. ‘Watitsanuliradi madalitso oti tasoŵa malo akuwalandirira’!
[Bokosi/Chithunzi patsamba 29]
ZOCHITIKA M’NTHAŴI YA NKHONDO
Ngakhale kuti papita zaka pafupifupi 60 kuchokera pamene nkhondo inatha, banja lonse likukumbukira zomwe zinachitika.
Doris anati: “Ku Pennsylvania kumazizira. Tsiku lina usiku kunazizira -30 degrees Celsius.” Ndipo Louise anawonjezera kuti, “Ine ndi Doris tinkakhala pampando wakumbuyo m’galimoto lathu n’kukhalirana pamiyendo kuti mapazi athu asazizidwe.”
“Koma sitinadandaule kapena kudzimvera chisoni. Tinkadziŵa kuti ndife oyendayenda kwambiri kusiyana ndi anthu ena, ndipo nthaŵi zonse tinali ndi chakudya chokwanira, ndi zovala zabwino zomwe anzathu ena okulirapo pang’ono a ku Ohio ankatipatsa,” anatero Doris.
Louise anati: “Nthaŵi zonse mayi ndi bambo ankatisonyeza chikondi ndi kutiyamikira. Nthaŵi zambiri tinkapita nawo kolalikira, choncho tinkaona kuti ndife ofunika ndi okondedwa.”
“Ndinali ndi galimoto ya mtundu wa 1936 Buick Special. Zikuoneka kuti injini yake inali yamphamvu kwambiri, ndiye kaŵirikaŵiri zitsulo zogwira matayala zinkaduka. Zimenezi zinkakonda kuchitika tsiku lozizira kwambiri pamwezi ndiye ndinkapita kudzala la magalimoto kukafunafuna chitsulo china. Mapeto ake ndinakhala katswiri woikirira zitsulozi,” anatero Paul.
“Komanso tisaiwale makadi olandirira katundu ndi chakudya. Chilichonse monga nyama, mafuta, matayala a galimoto, chinali kugaŵidwa pang’onopang’ono. Nthaŵi zonse tikasamukira ku gawo latsopano tinkapita kwa akuluakulu a boma kukafuna khadi lolandirira zinthu. Zimatenga miyezi kuti tilipeze khadilo ndipo nthaŵi zonse zimaoneka kuti tikangolipeza, timasamukira ku gawo lina n’kukayambiranso kufuna khadi lina. Koma Yehova anatisamala nthaŵi zonse,” anatero Marion.
[Chithunzi]
Ine, Marion ndi Doris (kumanzere) ndi Louise, mu 2000
[Chithunzi patsamba 25]
Ine ndi amayi mu 1918 ndili ndi zaka 11
[Chithunzi patsamba 26]
Ine, Louise, Marion ndi Doris mu 1948, pa ubatizo wa atsikanawa
[Chithunzi patsamba 26]
Chithunzi cha ukwati wathu mu October 1928
[Chithunzi patsamba 26]
Ine ndi ana anga (kumanzere kwenikweni ndi kumanja kwenikweni) ku Yankee Stadium, mu 1955