Kodi Mulungu Ndiye Amachititsa Mavuto Athu?
MWANA wamkazi wachikulire wa mayi wotchedwa Marion atavulala moopsa kumutu, Marion anachita zimene ambirife tingachite.a Iye anapemphera kwa Mulungu. Marion anati: “Sindinasoŵepo pogwira ndiponso sindinasungulumwepo ngati mmene ndinachitira panthaŵiyi.” Kenaka, matenda a mwana wake aja anafika poipa, ndipo Marion anayamba kutaya chikhulupiriro mwa Mulungu. Iye anafunsa kuti: “Kodi zimenezi zikuchitika chifukwa chiyani?” Sankamvetsa kuti zatani kuti Mulungu wachikondi ndiponso woganizira anthu ake amutaye chonchi.
Si Marion yekha amene anakumanapo ndi zoterezi. Anthu ambirimbiri padziko lonse akhala akuona kuti Mulungu wawataya panthaŵi yamavuto. Mdzukulu wake ataphedwa, Lisa anati: “Sindikumvetsabe kuti n’chifukwa chiyani Mulungu amalola kuti pazichitika zinthu zoipa zoterezi. . . . Sikuti ndinasiyiratu kukhulupirira Mulungu, koma kunena zoona chikhulupiriro changa chachepa.” Mayi wina ananenanso mawu aŵa mwana wake wakhanda ataphedwa mosamvetsetseka: “Mulungu sanandilimbikitse m’njira iliyonse pa zimene zachitikazi. Sanasonyeze ngakhale pang’ono kuti amandiganizira kapena kuti akundimvera chisoni.” Mayiyu anatinso: “Mulungu sindidzamukhululukira mpaka kalekale.”
Anthu ena amaipidwa ndi Mulungu akaona mmene zinthu zilili m’dziko. Amaona anthu m’mayiko osiyanasiyana akusautsidwa ndi umphaŵi ndiponso njala. Amaona anthu othaŵa nkhondo omwe akusoŵa pogwira, ana ochuluka mosaneneka omwe ali amasiye chifukwa cha matenda a Edzi, ndiponso anthu ena ambirimbiri amene akuvutika ndi matenda ena. Akaona zovuta ngati zimenezi, anthu ambiri amaimba mlandu Mulungu chifukwa choona ngati kuti iye sakuchitapo kanthu.
Komatu zoona zake n’zakuti Mulungu si amene amachititsa mavuto amene akusautsa anthu. Kwenikweni, pali zifukwa zomveka zokhulupirira kuti posachedwapa Mulungu adzathetsa zovuta zonse zimene anthu akukumana nazo. Tikukupemphani kuŵerenga nkhani yotsatirayi kuti muone kuti Mulungu amatiganiziradi.
[Mawu a M’munsi]
a Mayina tawasintha.