Lachitatu, March 27
Muziika Ufumu . . . pamalo oyamba.—Mat. 6:33.
Pamene Yesu anaphedwa, ophunzira ake anakhumudwa kwambiri. Sikuti iwo ankangoona kuti ataya mnzawo wapamtima koma ankaonanso kuti alibe chiyembekezo. (Luka 24:17-21) Komabe ataonekera kwa iwo, Yesu anawathandiza kumvetsa mmene zomwe zinamuchitikira zinakwaniritsira ulosi wa m’Baibulo. Anawapatsanso ntchito yofunika kwambiri yoti agwire. (Luka 24:26, 27, 45-48) Pamene Yesu ankakwera kumwamba, chisoni cha ophunzirawo chinasanduka chimwemwe chachikulu. Kudziwa kuti Mbuye wawo ali moyo komanso ndi wokonzeka kuwathandiza pantchito yatsopano imene anawapatsa, kunawathandiza kukhala osangalala. Chimwemwe chimene anali nacho chinawathandiza kuti azitamanda Yehova mwakhama. (Luka 24:52, 53; Mac. 5:42) Kuti titsanzire ophunzira a Yesu, m’pofunika kuti tiziika Ufumu wa Mulungu pamalo oyamba. Ngakhale kuti timafunika kupirira kuti tipitirize kutumikira Yehova, iye amalonjeza kuti adzatidalitsa kwambiri tikamachita zimenezo.—Miy. 10:22. w23.01 30-31 ¶15-16
Kuwerenga Baibulo pa nyengo ya Chikumbutso: (Zochitika pa Nisani 16 kutacha) Maliko 16:2-8
Lachinayi, March 28
Kufumbiko udzabwerera. —Gen. 3:19.
Ifeyo sitifuna kulakwitsa ngati mmene Adamu ndi Hava anachitira. Tingapewe zimenezi ngati titapitiriza kuphunzira zokhudza Yehova, kuyamikira makhalidwe ake komanso kuyesetsa kuti tizimvetsa mmene amaganizira. Tikatero tidzayamba kumukonda kwambiri. Taganizirani za Abulahamu. Iye ankakonda kwambiri Yehova. Ngakhale pamene zinkamuvuta kumvetsa zimene Yehova wasankha, iye ankamumverabe ndipo ankayesetsa kuti amudziwe bwino. Mwachitsanzo, atadziwa kuti Yehova akufuna kuwononga Sodomu ndi Gomora, poyamba Abulahamu ankaopa kuti mwina “Woweruza wa dziko lonse lapansi,” awononga oipa pamodzi ndi olungama omwe. Abulahamu ankaona kuti zimenezi ndi zosayenera choncho modzichepetsa anafunsa Yehova mafunso angapo. Yehova anamuyankha moleza mtima. Pamapeto pake Abulahamu anazindikira kuti Yehova amafufuza mtima wa munthu aliyense ndiponso kuti sapereka chilango kwa anthu oipa limodzi ndi osalakwa omwe.—Gen. 18:20-32. w22.08 28 ¶9-10
Lachisanu, March 29
Munthu wokhulupirika amasunga chinsinsi.—Miy. 11:13.
Mu 455 B.C.E., Bwanamkubwa Nehemiya atamaliza kumanga mpanda wa Yerusalemu, anafufuza amuna odalirika omwe anawaika pa udindo woyang’anira mzindawo. Pa anthu omwe anawasankha panalinso Hananiya kalonga wa m’Nyumba Yachitetezo Champhamvu. Baibulo limanena kuti Hananiya “anali munthu wodalirika ndiponso woopa kwambiri Mulungu woona kuposa anthu ena ambiri.” (Neh. 7:2) Kukonda Yehova komanso kuopa kumukhumudwitsa kunachititsa Hananiya kuona kuti utumiki uliwonse umene anapatsidwa unali wofunika kwambiri. Makhalidwe amenewa angatithandizenso ifeyo kukhala odalirika tikamatumikira Mulungu. Taganizirani chitsanzo cha Tukiko yemwe anali mnzake wodalirika wa mtumwi Paulo. Paulo ankadalira Tukiko ndipo anamufotokoza kuti anali “mtumiki wokhulupirika.” (Aef. 6:21, 22) Sikuti Paulo ankangomudalira pa nkhani yokapereka makalata ku Efeso ndi ku Kolose koma ankamudaliranso kuti akalimbikitsa ndi kutonthoza Akhristu kumeneko. Tukiko amatikumbutsa za abale okhulupirika komanso odalirika masiku ano, omwe amatithandiza kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova.—Akol. 4:7-9. w22.09 9-10 ¶5-6