Lachinayi, March 28
Kufumbiko udzabwerera. —Gen. 3:19.
Ifeyo sitifuna kulakwitsa ngati mmene Adamu ndi Hava anachitira. Tingapewe zimenezi ngati titapitiriza kuphunzira zokhudza Yehova, kuyamikira makhalidwe ake komanso kuyesetsa kuti tizimvetsa mmene amaganizira. Tikatero tidzayamba kumukonda kwambiri. Taganizirani za Abulahamu. Iye ankakonda kwambiri Yehova. Ngakhale pamene zinkamuvuta kumvetsa zimene Yehova wasankha, iye ankamumverabe ndipo ankayesetsa kuti amudziwe bwino. Mwachitsanzo, atadziwa kuti Yehova akufuna kuwononga Sodomu ndi Gomora, poyamba Abulahamu ankaopa kuti mwina “Woweruza wa dziko lonse lapansi,” awononga oipa pamodzi ndi olungama omwe. Abulahamu ankaona kuti zimenezi ndi zosayenera choncho modzichepetsa anafunsa Yehova mafunso angapo. Yehova anamuyankha moleza mtima. Pamapeto pake Abulahamu anazindikira kuti Yehova amafufuza mtima wa munthu aliyense ndiponso kuti sapereka chilango kwa anthu oipa limodzi ndi osalakwa omwe.—Gen. 18:20-32. w22.08 28 ¶9-10
Lachisanu, March 29
Munthu wokhulupirika amasunga chinsinsi.—Miy. 11:13.
Mu 455 B.C.E., Bwanamkubwa Nehemiya atamaliza kumanga mpanda wa Yerusalemu, anafufuza amuna odalirika omwe anawaika pa udindo woyang’anira mzindawo. Pa anthu omwe anawasankha panalinso Hananiya kalonga wa m’Nyumba Yachitetezo Champhamvu. Baibulo limanena kuti Hananiya “anali munthu wodalirika ndiponso woopa kwambiri Mulungu woona kuposa anthu ena ambiri.” (Neh. 7:2) Kukonda Yehova komanso kuopa kumukhumudwitsa kunachititsa Hananiya kuona kuti utumiki uliwonse umene anapatsidwa unali wofunika kwambiri. Makhalidwe amenewa angatithandizenso ifeyo kukhala odalirika tikamatumikira Mulungu. Taganizirani chitsanzo cha Tukiko yemwe anali mnzake wodalirika wa mtumwi Paulo. Paulo ankadalira Tukiko ndipo anamufotokoza kuti anali “mtumiki wokhulupirika.” (Aef. 6:21, 22) Sikuti Paulo ankangomudalira pa nkhani yokapereka makalata ku Efeso ndi ku Kolose koma ankamudaliranso kuti akalimbikitsa ndi kutonthoza Akhristu kumeneko. Tukiko amatikumbutsa za abale okhulupirika komanso odalirika masiku ano, omwe amatithandiza kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova.—Akol. 4:7-9. w22.09 9-10 ¶5-6
Loweruka, March 30
Chikondi chimakwirira machimo ochuluka.—1 Pet. 4:8.
Yosefe anakumana ndi mayesero aakulu kwambiri kwa zaka pafupifupi 13. Yosefe akanatha kukayikira ngati Yehova ankamukondadi. Akanathanso kumaona ngati Yehova wamusiya pamene akufunikira thandizo. Koma iye sanalole kuti zimenezi zimukhumudwitse. Anapitirizabe kukhala woganiza bwino pokhala wodekha. Pamene anali ndi mpata woti akanatha kuwabwezera abale akewo, iye sanatero koma anawasonyeza chikondi komanso anawakhululukira. (Gen. 45:4, 5) Yosefe anakwanitsa kuchita zimenezi chifukwa ankaganiza bwino. M’malo moganizira mavuto omwe ankakumana nawo, iye ankaganizira nkhani yofunika kwambiri yokhudza cholinga cha Yehova. (Gen. 50:19-21) Kodi tikuphunzirapo chiyani? Mukachitiridwa zinthu zopanda chilungamo, musamakwiyire Yehova kapena kuyamba kuona kuti wakutayani. M’malomwake, muziganizira mmene akukuthandizirani kupirira mayeserowo. Kuwonjezera pamenepo, ena akakulakwirani muziphimba zolakwa zawo ndi chikondi chanu. w22.11 21 ¶4