Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu ya January 2018
JANUARY 1-7
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MATEYU 1-3
“Ufumu Wakumwamba Wayandikira”
nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Mat. 3:1, 2
kulalikira: Mawuwa m’chigiriki amatanthauza “kulengeza uthenga winawake woti anthu onse amve.” Mawuwa amasonyeza mmene munthu amachitira zimenezi, kuti amalengeza mokuwa kwa anthu osati kungolalikira kagulu ka anthu ochepa chabe omwe asonkhana.
Ufumu: Pavesili m’pamene pamapezeka koyamba mawu achigiriki akuti ba·si·leiʹa, omwe amamasuliridwa kuti Ufumu. Mawuwa amatanthauza boma, dera komanso anthu olamuliridwa ndi mfumu. M’Malemba Achigiriki, mawu amenewa amapezeka maulendo okwana 162 ndipo m’buku la Mateyu lokha amapezeka ka 55. Nthawi zambiri m’bukuli mawuwa amakhala akunena za Ufumu wa Mulungu. Mateyu anagwiritsa ntchito mawu amenewa mobwerezabwereza moti Uthenga wake umatchedwanso kuti Uthenga Wabwino wa Ufumu.
Ufumu wakumwamba: Mawuwa amapezeka maulendo 30, mu Uthenga Wabwino wa Mateyu wokha. Mu Uthenga Wabwino wa Maliko ndi Luka, anagwiritsa ntchito mawu ofanana nawo akuti “Ufumu wa Mulungu.” Zimenezi zikusonyeza kuti “Ufumu wa Mulungu” uli kumwamba ndipo uzidzalamulira dziko lapansili uli kumwambako.—Mat. 21:43; Maliko 1:15; Luka 4:43; Dan. 2:44; 2 Tim. 4:18.
wayandikira: Apa ankatanthauza kuti Wolamulira wa Ufumu wakumwambayu anali atatsala pang’ono kufika.
nwtsty zithunzi ndi mavidiyo
Zovala za Yohane M’batizi Komanso Maonekedwe Ake
Yohane ankavala chovala chaubweya wa ngamila ndipo ankamangira lamba wachikopa m’chiuno mwake. Palambapo ankatha kukolekapo zinthu zina zing’onozing’ono. Zovalazi ndi zofanana ndi zimene mneneri Eliya ankavala. (2 Maf. 1:8) Zovala zopangidwa ndi ubweya wa ngamila zinkakhala zokhakhala ndipo nthawi zambiri anthu osauka ndi amene ankavala zovalazi. Koma anthu olemera, ankavala zovala zofewa zopangidwa ndi nsalu. (Mat. 11:7-9) N’kutheka kuti Yohane anali asanametepo tsitsi lake chifukwa anakhala Mnaziri kuyambira ali mwana. Choncho zovala komanso maonekedwe ake, zinkasonyezeratu kuti ankakhala moyo wosalira zambiri ndipo anali wodzipereka kuchita chifuniro cha Mulungu.
Dzombe
M’Baibulo, mawu akuti “dzombe” angatanthauze mtundu uliwonse wa ziwala zimene zimakhala ndi tinyanga tifupitifupi ndipo zimauluka m’chigulu chachikulu. Malinga ndi kafukufuku wina amene anapangidwa ku Yerusalemu, zikusonyeza kuti dzombe lam’chipululu limakhala ndi mapuloteni okwana 75 peresenti. Ambiri masiku ano akamadya ziwalazi amachotsa mutu, miyendo, mapiko komanso mimba yake. Mbali yotsalayo, yomwe ndi chifuwa ndi imene amadya ndipo amaidya yaiwisi kapena yophika. Ziwalazi zimakoma ngati nkhanu ndipo zimakhala ndi mapuloteni ambiri.
Uchi
Chithunzichi chikusonyeza chisa cha njuchi (1) ndi uchi (2). Uchi umene Yohane ankadya unkapangidwa ndi mtundu winawake wa njuchi zakutchire zomwe zinkapezeka zambiri m’deralo. Njuchi zimenezi zinali zolusa kwambiri ndipo zinkakonda kukhala m’malo otentha, monga m’chipululu cha Yudeya. Anthu sankachita ulimi wa njuchi zimenezi. Komabe chakumayambiriro kwa zaka za m’ma 800 B.C.E., anthu a ku Isiraeli ankaweta njuchi m’ming’oma yadothi. Ming’oma yambiri yamtunduwu inapezeka m’tauni ina (yomwe panopo imatchedwa Tel Rehov), imene ili m’chigwa cha Yorodano. Zikuoneka kuti uchi wa m’ming’omayi unali wa njuchi zochokera ku dziko limene panopa ndi Turkey.
Kufufuza Mfundo Zothandiza
nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Mat. 1:3
Tamara: Ndi mzimayi woyamba pa azimayi 5 omwe Mateyu anawatchula pamndandanda wa mzere umene Mesiya anabadwira. Azimayi enawo ndi Rahabi ndi Rute omwe sanali Aisiraeli (vesi 5), Batiseba, “mkazi wa Uriya” (vesi 6), ndiponso Mariya (vesi 16). Mwina azimayiwa anatchulidwa pamndandandawu womwe unali ndi mayina ambiri a azibambo chifukwa choti panali zinthu zina zapadera zimene aliyense wa iwo anachita kuti akhale kholo la Yesu.
nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Mat. 3:11
ndikukubatizani: kapena “kukuviikani.” Mawu achigiriki omwe anamasuliridwa kuti kubatiza (ba·ptiʹzo) amatanthauza “kuviika kapena kumiza.” Ubatizo wotchulidwa m’Baibulo unkachitika mwa kuviika munthu yense m’madzi. Nthawi ina Yohane ankabatizira anthu m’chigwa cha Yorodano kufupi ndi ku Salimu “chifukwa kunali madzi ambiri kumeneko.” (Yoh. 3:23) Ndiponso pamene Filipo ankabatiza nduna ya ku Itiyopiya, onse awiri “anatsika ndi kulowa m’madzimo.” (Mac. 8:38) Mawu achigiriki omwewa ndi amene anagwiritsidwanso ntchito m’Baibulo la Septuagint pa 2 Mafumu 5:14 pofotokoza za Namani kuti anapita “ku Yorodano n’kukamira maulendo 7.”
JANUARY 8-14
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MATEYU 4-5
“Zimene Tikuphunzira pa Zomwe Yesu Anaphunzitsa pa Ulaliki Wapaphiri”
nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Mat. 5:3
Odala (osangalala kapena achimwemwe): Kukhala odala sikumangotanthauza kukhala ndi chimwemwe chifukwa choti zinthu zikuyenda bwino. M’malomwake mawuwa amatanthauza mmene munthu amamvera Mulungu akamamudalitsa komanso kumukonda. Mawuwa amagwiritsidwanso ntchito pofotokoza zokhudza Mulungu ndi Yesu muulemerero wawo wakumwamba.—1Tim. 1:11; 6:15.
anthu amene amazindikira zosowa zawo zauzimu: Mawu achigiriki omwe anamasuliridwa kuti “anthu amene amazindikira,” kwenikweni amatanthauza “anthu osauka (opemphapempha).” M’nkhaniyi akunena za anthu osowa, amene amadziwa zimene akusowazo. Mawu omwewa ndi amene anagwiritsidwanso ntchito pofotokoza za Lazaro, “wopemphapempha” pa Luka 16:20, 22. Mawu achigiriki omwe m’Mabaibulo ena anawamasulira kuti “osauka mumzimu,” amanena za anthu amene amadziwa kuti ndi osauka mwauzimu ndipo akufuna kuti Mulungu aziwatsogolera.
nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Mat. 5:7
achifundo: M’Baibulo mawu akuti “achifundo” komanso “chifundo” sikuti amangotanthauza kukhululukira winawake kapena kulekerera osapereka chilango. Nthawi zambiri mawuwa amatanthauza kukonda komanso kumvera chisoni ena, zimene zimachititsa kuti munthu akhale wofunitsitsa kuwathandiza.
nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Mat. 5:9
amene amabweretsa mtendere: Anthu oterewa sikuti amangokhala mwamtendere ndi ena koma amayesetsanso kubweretsa mtendere pamene palibe mtenderewo.
Kufufuza Mfundo Zothandiza
nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Mat. 4:9
kundiweramira kamodzi kokha: Mawu achigiriki omwe amamasuliridwa kuti “kuweramira,” amasonyeza zinthu zomwe zangochitika kamodzi. Choncho mawu akuti “kundiweramira kamodzi kokha” akusonyeza kuti Mdyerekezi sanapemphe Yesu kuti amuweramire kambirimbiri koma kamodzi basi.
nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Mat. 4:23
kuphunzitsa . . . kulalikira: Kuphunzitsa n’kosiyana ndi kulalikira chifukwa mphunzitsi amachita zambiri kuposa kungolengeza. Iye amalangiza, kufotokoza komanso kupereka maumboni ogwira mtima a zimene akufotokozazo.
JANUARY 15-21
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MATEYU 6-7
“Pitirizani Kufunafuna Ufumu Choyamba”
nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Mat. 6:24
kapolo: M’chigiriki mawuwa amanena za kugwira ntchito ngati kapolo koma kapolo wake wokhala ndi mbuye m’modzi yekha. Apa Yesu ankafotokoza kuti Mkhristu sangakhale wodzipereka kwa Mulungu n’kumachita zonse zimene Mulunguyo amafuna, pa nthawi imodzimodziyo n’kumafunafunanso chuma.
nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Mat. 6:33
pitirizani kufunafuna: Mawu achigiriki omwe anamasuliridwa kuti pitirizani kufunafuna, amasonyeza kuchita zinazake mobwerezabwereza osasiya. Otsatira a Yesu samangofunafuna Ufumu kwa kanthawi kenako n’kusiya kumachita zinthu zina. M’malomwake, nthawi zonse amaona kuti Ufumu ndi wofunika kwambiri pa moyo wawo.
Ufumu: M’mabuku ena akale achigiriki mawuwa analembedwa kuti “Ufumu wa Mulungu.”
chilungamo: Anthu amene amafunafuna chilungamo cha Mulungu amakhala ofunitsitsa kuchita chifuniro chake ndipo amatsatira mfundo zake pa nkhani ya zabwino ndi zoipa. Zimenezi zikusiyana kwambiri ndi zimene Afarisi ankachita, iwo ankafuna kukhazikitsa chilungamo chawochawo.—Mat. 5:20.
chake: Akunena za chilungamo cha Mulungu, yemwe ndi ‘Atate wakumwamba’ wotchulidwa pa Mat. 6:32.
Kufufuza Mfundo Zothandiza
nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Mat. 7:28, 29
linadabwa: Mawu achigiriki amene anamasuliridwa kuti linadabwa amatanthauza “kudabwa kwambiri mpaka kufika pochita kakasi.” Zimenezi zikusonyeza kuti mawu a Yesu ankawafika anthu pamtima kwambiri.
kaphunzitsidwe kake: Mawuwa akunena za mmene Yesu ankaphunzitsira, njira zimene ankagwiritsa ntchito pophunzitsa komanso zimene anaphunzitsa kuphatikizapo malangizo amene anapereka pa Ulaliki Wapaphiri.
osati monga alembi awo: M’malo mophunzitsa mfundo za arabi ngati mmene alembi ankachitira, Yesu ankaphunzitsa monga woimira Yehova, ngati munthu waulamuliro ndipo ankaphunzitsa zochokera m’Mawu a Mulungu.—Yoh. 7:16.
JANUARY 22-28
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MATEYU 8-9
“Yesu Ankakonda Anthu”
nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Mat. 8:3
kumukhudza: Chilamulo cha Mose chinkanena kuti munthu wakhate ayenera kukhala kwayekha pofuna kuteteza anthu ena kuti asatenge matendawo. (Lev. 13:45, 46; Num. 5:1-4) Koma atsogoleri achipembedzo chachiyuda anapanga malamulo ena owonjezera. Mwachitsanzo iwo ankati munthu ankayenera kutalikirana ndi wakhate pamtunda wa mamita pafupifupi 1.8 ndipo ngati tsikulo kuli mphepo ankayenera kutalikirana naye mamita pafupifupi 45. Malamulo amenewa ankachititsa kuti anthu akhate azichitiridwa nkhanza. Nkhani zina zimanena kuti rabi wina ankabisala akaona akhate komanso wina ankathamangitsa akhate kuti asamuyandikire powagenda ndi miyala. Mosiyana ndi arabiwa, Yesu anakhudzidwa kwambiri ataona wakhate wina moti anachita zimene Ayuda ena ankaziona kuti ndi zosayenera. Iye anamukhudza munthu wakhateyo ngakhale kuti akanatha kumuchiritsa ndi mawu okha.—Mat. 8:5-12.
Ndikufuna: Sikuti Yesu anachiritsa munthu wakhate uja chifukwa choti anamupempha kapenanso chifukwa chongokakamizika. Koma iye anachita zimenezi chifukwa ankafunitsitsa kumuthandiza.
nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Mat. 9:10
kudya patebulo: Kapena “kudya chakudya.” Kudya patebulo ndi munthu wina kunkasonyeza kuti anthuwo ndi ogwirizana. Choncho Ayuda a m’nthawi ya Yesu sankadya limodzi ndi anthu omwe sanali Ayuda.
okhometsa msonkho: Ayuda ambiri ankatolera ndalama za misonkho m’malo mwa akuluakulu a boma la Roma. Anthu ankadana ndi Ayuda amenewo chifukwa choti anagwirizana ndi ulamuliro wina komanso ankakakamiza anthu kuti apereke ndalama zambiri kuposa msonkho wovomerezeka. Okhometsa msonkho ankasalidwa ndi Ayuda anzawo ndipo ankawaika m’gulu la anthu ochimwa komanso mahule.—Mat. 11:19; 21:32.
nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Mat. 9:36
anawamvera chisoni: Mawu achigiriki omwe anagwiritsidwa ntchito pomasulira mawuwa amanena za “matumbo,” posonyeza mmene munthu akumvera kuyambira mkati mwa thupi lake kusonyeza kuti wakhudzidwa kwambiri. Amenewa ndi amodzi mwa mawu achigiriki amphamvu kwambiri amene amasonyeza kuti munthu wakhudzidwa.
JANUARY 29–FEBRUARY 4
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MATEYU 10-11
“Yesu Ankatsitsimula Ena”
nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Mat. 10:29, 30
Mpheta: Mawu achigiriki akuti strou·thiʹon, amanena za kambalame kakang’ono. Nthawi zambiri mawuwa ankalembedwa ponena za mpheta zomwe zinali mbalame zotchipa kwambiri poyerekeza ndi mbalame zina zimene anthu ankagula kuti akadye.
amazigulitsa kakhobidi kamodzi kochepa mphamvu: Kakhobidi komwe akunena apa kankatchedwa “asariyoni” ndipo ndalama imeneyi ndi yomwe inali malipiro a munthu amene wagwira ntchito kwa 45 minitsi. (sgd tsa. 62 18-B.) Pamene Yesu anali paulendo wake wachitatu wolalikira ku Galileya ananena kuti mpheta ziwiri zinkagulidwa asariyoni imodzi. Paulendo winanso pamene ankalalikira ku Yudeya, patatha pafupifupi chaka chimodzi, Yesu ananena kuti mpheta 5 zinkagulidwa ndi ndalama zimenezi ziwiri. (Luka 12:6) Nkhani zimenezi zikusonyeza kuti mpheta zinali zotchipa kwambiri moti munthu akagula mpheta 4 ankamupatsa imodzi yaulere.
tsitsi lenilenilo la m’mutu mwanu amaliwerenga: Ofufuza amati m’mutu mwa munthu aliyense muli tsitsi loposa 100,000. Mfundo yoti Yehova amawerenga ngakhale tinthu ting’onoting’ono monga tsitsi, imatithandiza kudziwa kuti iye amachita chidwi kwambiri ndi mtumiki wake aliyense.
nwtsty zithunzi ndi mavidiyo
Mpheta
Mpheta zinali mbalame zotchipa kwambiri poyerekeza ndi mbalame zina zimene anthu ankagula kuti akadye. Munthu ankatha kugula mbalame ziwiri ndi malipiro omwe ankalandira akagwira ntchito kwa 45 minitsi. Mawu achigiriki omwe anawamasulira kuti mpheta pavesili amangotanthauza mitundu yosiyanasiyana ya mbalame zing’onozing’ono kuphatikizapo mpheta zomwe zimapezeka m’nyumba za anthu komanso mpheta za ku Spain zimene zimapezekabe zambiri ku Israel.
nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Mat. 11:28
olemedwa: Anthu amene Yesu ankawaitana kuti apite kwa iye anali “olemedwa” ndi nkhawa komanso otopa ndi ntchito. Kulambira Yehova kunali kutasanduka katundu wolemera chifukwa cha miyambo ya anthu imene inaphatikizidwa m’Chilamulo cha Mose. (Mat. 23:4) Ngakhale tsiku la Sabata, lomwe linkafunika kukhala lotsitsimula, linayambanso kukhala lolemetsa.—Eks. 23:12; Maliko 2:23-28; Luka 6:1-11.
ndidzakutsitsimutsani: Mawu achigiriki omwe amatanthauza “kutsitsimutsa” angatanthauzenso kupuma (Mat. 26:45; Maliko 6:31) kapena kupezanso mphamvu (2 Akor. 7:13; Filim. 7). Nkhaniyi ikusonyeza kuti kusenza “goli” la Yesu (Mat. 11:29) kukuphatikizapo kugwira ntchito osati kungokhala n’kumapuma. Mawu achigiriki osonyeza kuti golili ndi la Yesu, akutithandiza kudziwa kuti iyeyo ndi amene amathandiza komanso kupereka mphamvu kwa anthu omwe atopa koma akufuna kusenzabe goli lake lofewa.
nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Mat. 11:29
senzani goli langa: Yesu anagwiritsa ntchito mawu akuti “goli” mophiphiritsira pofuna kutanthauza kugonjera ulamuliro komanso kutsatira malangizo. Yesu akanakhala kuti ankanena za goli lokhala ndi anthu awiri, limene Mulungu anamusenzetsa, ndiye kuti zikanatanthauza kuti ankauza ophunzira ake kuti asenze naye limodzi goli lake ndipo iyeyo adzawathandiza. Zikanakhala choncho, mawuwa akanalembedwa kuti: “Senzani goli pamodzi ndi ine.” Koma ngati golili ndi limene Yesu wapatsa anthu ena kuti alisenze, ndiye kuti zikutanthauza kuti osenza goliwo azigonjera ulamuliro komanso malangizo monga otsatira ake.