MUTU 13
‘Ufotokoze za Kachisiyu’
MFUNDO YAIKULU: Tanthauzo la masomphenya a kachisi waulemerero amene Ezekieli anaona
1-3. (a) N’chifukwa chiyani Ezekieli ayenera kuti analimbikitsidwa ataona masomphenya a malo aakulu a kachisi? (Onani chithunzi choyambirira.) (b) Kodi tikambirana chiyani m’mutuwu?
YEREKEZERANI kuti mukuona Ezekieli ali ndi zaka 50. Tsopano akuganizira zaka 25 zimene wakhala ali ku ukapolo. Nthawi yonseyi kachisi wa ku Yerusalemu wakhala ali bwinja. Ngati Ezekieli ankayembekezera kuti nthawi ina adzatumikira ngati wansembe m’kachisimo ndiye kuti zimene ankayembekezerazo sizikanathekanso. Panali patatsala zaka 56 kuti ukapolo uthe. Choncho Ezekieli ankadziwa kuti zinali zosatheka kuti akhale nthawi yaitali choncho n’kuona anthu a Yehova akubwerera kudziko lawo komanso kuona kachisi akumangidwanso. (Yer. 25:11) Kodi Ezekieli ankamva chisoni akaganizira zimenezi?
2 Yehova anasonyeza chifundo posankha kuti amuonetse Ezekieli masomphenya amenewa amene akanalimbikitsa munthu wokhulupirikayu komanso kumupatsa chiyembekezo. M’masomphenyawo mneneriyo anatengedwa n’kumupititsa kudziko lakwawo ndipo anakamuimika paphiri lalitali kwambiri. Ali kumeneko anakumana ndi “munthu wamwamuna amene maonekedwe ake anali ofanana ndi kopa.” Mwamuna ameneyu anali mngelo ndipo anamutenga n’kumamuonetsa chilichonse m’kachisi wochititsa chidwi. (Werengani Ezekieli 40:1-4.) Zonse zinkaoneka ngati zinali zenizeni. Kwa Ezekieli zimene ankaonazo zinali zolimbitsa chikhulupiriro, zochititsa mantha komanso mwina zodabwitsa pang’ono. Ngakhale kuti kachisi amene anaona anali ndi zinthu zambiri zimene ankazidziwa, anali wosiyana kwambiri ndi kachisi wa ku Yerusalemu amene ankamudziwa.
3 Machaputala 9 omalizira a buku la Ezekieli akufotokoza za masomphenya ochititsa chidwiwa. Tsopano tiyeni tikambirane za maganizo amene tikuyenera kukhala nawo pamene tikuphunzira za masomphenyawa kuti tiwamvetse. Kenako tiona ngati zimene Ezekieli anaona zinali kachisi wamkulu wauzimu amene Paulo anamufotokoza patapita zaka zambiri. Pomalizira tikambirana zimene masomphenyawa ankatanthauza kwa Ezekieli ndi anzake amene anali nawo ku ukapolo.
Tikuyenera Kusintha Njira Yofotokozerera Zinthu
4. Kodi tinkafotokoza chiyani m’mbuyomu zokhudza masomphenya a kachisi, nanga panopa timafotokoza zotani?
4 M’mbuyomo mabuku athu anafotokoza kuti Ezekieli anaona kachisi wamkulu wauzimu wa Yehova, amenenso mtumwi Paulo mouziridwa anamufotokoza m’kalata imene analembera Aheberi.a Potengera mfundo imeneyi, tinkaona kuti n’zomveka kunena kuti mbali zambiri za masomphenya a Ezekieli zinali ndi tanthauzo lophiphiritsa. Ponena zimenezi tinkagwiritsa ntchito zimene Paulo anafotokoza zokhudza chihema. Koma pambuyo popemphera, kuphunzira komanso kuganizira mozama za masomphenya a kachisi, taona kuti pakufunika njira yosavuta yofotokozera tanthauzo la masomphenya amenewa.
5, 6. (a) Kodi Paulo anasonyeza bwanji kudzichepetsa pamene ankafotokoza za chihema? (b) Kodi Paulo ananena chiyani zokhudza zinthu zina za pachihema, nanga maganizo akewa tingawagwiritse ntchito bwanji kuti timvetse masomphenya a kachisi amene Ezekieli anaona?
5 Zikuoneka kuti ndi nzeru kuti tisamaganize kuti mbali iliyonse ya masomphenya a kachisi amene Ezekieli anaona, ili ndi tanthauzo lophiphiritsa. Chifukwa chiyani? Taganizirani chitsanzo chochititsa chidwi chotsatirachi. Pamene Paulo ankafotokoza za chihema komanso kachisi wauzimu anatchula zinthu zina zomwe zinali m’chihema ngati chofukizira cha golide, chivindikiro cha likasa ndi mtsuko wagolide mmene munali mana. Kodi ananena kuti zinthu zimenezi zili ndi tanthauzo lophiphiritsa? Zikuoneka kuti mzimu woyera sunamutsogolere kuti anene zimenezo. M’malo mwake Paulo analemba kuti: “Koma ino si nthawi yofotokoza zinthu zimenezi mwatsatanetsatane.” (Aheb. 9:4, 5) Paulo anali wofunitsitsa kutsatira zimene mzimu woyera unkamuuza komanso kuyembekezera Yehova modzichepetsa.—Aheb. 9:8.
6 Tinganenenso zofanana ndi zimenezi pa nkhani yokhudza masomphenya a Ezekieli a kachisi. Masomphenya amenewo alinso ndi mfundo zosiyanasiyana ndipo zikuoneka kuti ndi bwino kuyembekezera kuti Yehova afotokoze mfundo zina momveka bwino ngati pakufunika kutero. (Werengani Mika 7:7.) Ndiye kodi tinene kuti mzimu wa Yehova sunatithandize kumvetsa mfundo zina zokhudza masomphenyawa? Yankho ndi lakuti watithandiza.
Kodi Ezekieli Anaona Kachisi Wamkulu Wauzimu?
7, 8. (a) Kodi pali kusintha kotani kokhudza mmene tinkamvera mfundo zina? (b) Kodi kachisi amene Ezekieli anaona m’masomphenya akusiyana bwanji ndi kachisi wauzimu amene Paulo anafotokoza?
7 Monga tanenera kale, kwa zaka zambiri mabuku athu ankafotokoza kuti Ezekieli anaona kachisi wamkulu wauzimu wa Yehova, amenenso Paulo anamufotokoza mouziridwa m’kalata imene analembera Aheberi. Koma titaphunziranso mozama za nkhaniyi zatipangitsa kukhulupirira kuti Ezekieli sanaone kachisi wamkulu wauzimu. Chifukwa chiyani tikutero?
8 Choyamba, kachisi amene Ezekieli anaona sakugwirizana ndi zimene Paulo anafotokoza mouziridwa. Taganizirani izi: Mtumwi Paulo anafotokoza momveka bwino kuti chihema cha Mose chinali mthunzi kapena chifaniziro cha chinthu chinachake chachikulu. Mofanana ndi kachisi wa Solomo komanso wa Zerubabele amene anamangidwa mofanana, chihema chinalinso ndi chipinda china chomwe chinali “Malo Oyera Koposa.” Paulo ananena kuti chipinda chimenechi ndi ‘malo oyera opangidwa ndi manja a anthu’ ndipo anafotokoza kuti anali “chithunzi cha malo enieniwo,” osati malo enieniwo. Kodi malo enieniwo anali ati? Paulo anafotokoza kuti ndi “kumwamba kwenikweniko.” (Aheb. 9:3, 24) Ndiye kodi Ezekieli anaona kumwamba? Ayi. Masomphenya a Ezekieli sasonyeza kuti ankaona zinthu zakumwamba.—Yerekezerani ndi Danieli 7:9, 10, 13, 14.
9, 10. Pa nkhani ya nsembe, kodi kachisi amene Ezekieli anaona m’masomphenya akusiyana bwanji ndi kachisi wauzimu amene Paulo anafotokoza?
9 Chinthu chachikulu chimene chikusiyanitsa masomphenya a Ezekieli ndi zimene Paulo anafotokoza n’chokhudza nsembe. Ezekieli anamva Yehova akupereka malangizo kwa anthu, akalonga komanso kwa ansembe okhudza mmene angaperekere nsembe. Iwo ankayenera kupereka nsembe chifukwa cha machimo awo. Ankayeneranso kupereka nsembe zamgwirizano zimene ankayenera kudyera limodzi m’chipinda chodyera cha pakachisi. (Ezek. 43:18, 19; 44:11, 15, 27; 45:15-20, 22-25) Kodi nsembe ngati zimenezi, zimene zinkaperekedwa mobwerezabwereza zimaperekedwanso m’kachisi wamkulu wauzimu?
Kachisi amene Ezekieli anaona m’masomphenya si kachisi wamkulu wauzimu
10 Yankho lake ndi lomveka bwino komanso losavuta. Paulo anafotokoza kuti: “Pamene Khristu anabwera monga mkulu wa ansembe wa zinthu zabwino zimene zakwaniritsidwa, anadzera mʼchihema chachikulu ndi changwiro kwambiri chimene sichinapangidwe ndi manja a anthu, kutanthauza kuti sichipezeka padzikoli. Iye analowa mʼmalo oyera ndi magazi ake, osati ndi magazi a mbuzi kapena a ngʼombe zazingʼono zamphongo. Analowa kamodzi kokha mʼmalo oyerawo ndipo anatipulumutsa kwamuyaya.” (Aheb. 9:11, 12) Choncho m’kachisi wamkulu wauzimu, ndi nsembe imodzi yokha imene inaperekedwa ndipo sipakufunikiranso nsembe zina. Nsembe imeneyi ndi nsembe ya dipo ndipo inaperekedwa ndi Yesu Khristu amene ndi Mkulu wa Ansembe wamkulu kuposa onse. Apa n’zoonekeratu kuti kachisi amene Ezekieli anamuona m’masomphenya, kumene kunkaperekedwa nsembe zambiri za mbuzi komanso ng’ombe zamphongo, sanali kachisi wamkulu wauzimu.
11. M’masiku a Ezekieli n’chifukwa chiyani sinali nthawi yabwino yoti Yehova aulule choonadi chokhudza kachisi wamkulu wauzimu?
11 Zimenezi zikutifikitsa pa chifukwa chachiwiri chimene tikunenera kuti Ezekieli sanaone kachisi wamkulu wauzimu: Nthawi ya Mulungu yoti aulule choonadi chimenechi inali isanakwane. Kumbukirani kuti choyamba masomphenya a Ezekieli ankapita kwa Ayuda omwe anali ku ukapolo ku Babulo. Ayudawo ankatsatira Chilamulo cha Mose. Ukapolowo utatha iwo ankayenera kubwerera ku Yerusalemu n’kukatsatira Chilamulo chimenecho pa nkhani yokhudza kulambira koyera ndipo ankayenera kumanganso kachisi ndi guwa lake lansembe. Kenako ankayenera kupitiriza kupereka nsembe kumeneko ndipo anachitadi zimenezi kwa zaka pafupifupi 600. Taganizirani mmene Ayudawo akanamvera zikanakhala kuti m’masomphenya a Ezekieli anawaonetsa kachisi wauzimu. Kodi akanamva bwanji kuona mkulu wa ansembe akupereka moyo wake ngati nsembe, kenako n’kuthetsa nsembe zina zonse? Kodi zikanatheka kuti amvetse masomphenya amenewo? Kodi zimenezi sizikanapangitsa kuti asiye kumvera Chilamulo cha Mose? Monga mwa nthawi zonse Yehova amaulula mfundo za choonadi pa nthawi yoyenera komanso pamene anthu ake ali okonzeka.
12-14. Kodi pali kugwirizana kotani pakati pa kachisi amene Ezekieli anaona ndi zimene Paulo anafotokoza zokhudza kachisi wauzimu? (Onani bokosi lakuti “Akachisi Osiyana Ofotokoza Zinthu Zosiyana.”)
12 Nanga kodi pali kugwirizana kotani pakati pa masomphenya a kachisi amene Ezekieli anaona, ndi zimene Paulo anafotokoza zokhudza kachisi wauzimu? Kumbukirani kuti zimene Paulo anafotokoza zokhudza kachisi wauzimu sanazifotokoze potengera zimene Ezekieli anaona m’masomphenya a kachisi, koma anazifotokoza potengera chihema cha m’nthawi ya Mose. N’zoona kuti Paulo sanatchule zinthu zambiri zimene zinkapezeka m’kachisi wa Solomo komanso wa Zerubabele zimenenso Ezekieli anaona m’masomphenya a kachisi. Choncho zimene Paulo komanso Ezekieli analemba zinali zosiyana.b Komabe ngakhale kuti analemba zosiyana mfundo zake zinali zogwirizana. Kodi zinali zogwirizana bwanji?
13 Tinganene kuti nkhani za m’Baibulo ziwirizi zikugwirizana m’njira iyi: Pa zimene Paulo ananena tikuona zomwe Yehova wachita pa nkhani yakulambira. Koma kuchokera kwa Ezekieli tikuona mfundo zimene Yehova amafuna kuti tizitsatira pa nkhani yakulambira. Pofuna kutiphunzitsa zimene Yehova wakonza pa nkhani ya kulambira koyera, Paulo anafotokoza tanthauzo la zinthu zimene zili m’kachisi wauzimu. Zinthu zake ndi ngati mkulu wa ansembe, nsembe, guwa la nsembe komanso Malo Oyera Koposa. Koma pofuna kutithandiza kumvetsa mfundo zapamwamba za Yehova zokhudza kulambira koyera, masomphenya a Ezekieli okhudza kachisi amatipatsa chithunzi chimene chimatithandiza kuona mfundo zosiyanasiyana zimene tikuphunzira zokhudza mfundo za Yehova zamakhalidwe abwino.
14 Ndiye kodi tikuphunzirapo chiyani pa mfundo za choonadi zimene tazimvetsa bwino? Sizikutanthauza kuti masomphenya amene Ezekieli anaona ndi osafunika kwenikweni kwa ife masiku ano. Kuti tione mmene masomphenyawo akutithandizira, tiyeni tionenso mmene anathandizira Ayuda okhulupirika m’nthawi ya Ezekieli komanso pambuyo pake.
Kodi Masomphenyawo Ankatanthauza Chiyani kwa Ayuda Amene Anali ku Ukapolo?
15. (a) Kodi uthenga waukulu wa masomphenya amene Ezekieli anaona unali wotani? (b) Kodi zimene zili mu Ezekieli chaputala 8 zikusiyana bwanji ndi zimene zili mu Ezekieli chaputala 40 mpaka 48?
15 Kuti tipeze yankho la m’Baibulo pa funso limeneli, tiyeni tione mafunso ena ofanana ndi amenewa amene angatithandize kuti tikhale ndi chithunzi chokwanira. Funso loyamba, kodi ndi uthenga uti wa ulosi umene ukupezeka m’masomphenyawa? Yankho lachidule ndi lakuti mfundo yaikulu ya uthengawu ndi yakuti kulambira koyera kudzabwezeretsedwa. N’zoonekeratu kuti Ezekieli anamvetsa mfundo imeneyi. Iye anali atalemba kale uthenga umene panopa uli m’chaputala 8 cha buku la Ezekieli. Mu uthenga umenewu Yehova anafotokoza momveka bwino mmene zinthu zinaipira pakachisi ku Yerusalemu. Ezekieli ayenera kuti anasangalala kwambiri kulemba uthenga wosiyana ndi umenewu, umene panopa ukupezeka m’chaputala 40 mpaka 48. M’machaputala amenewa tikuonadi chitsanzo cha kulambira koyera kumene Yehova ankafuna mogwirizana ndi Chilamulo cha Mose, osati kulambira koipitsidwa.
16. Kodi zimene Ezekieli anaona m’masomphenya a kachisi zikutsimikizira bwanji zimene Yesaya ananena zaka 100 nthawi ya Ezekieli isanafike?
16 Kuti anthu azilambira Yehova m’njira imene iye amafuna, kulambirako kunayenera kukwezedwa. Zaka zoposa 100 m’mbuyomo, mouziridwa mneneri Yesaya analemba kuti: “Mʼmasiku otsiriza, Phiri la nyumba ya Yehova lidzakhazikika pamwamba penipeni pa mapiri akuluakulu, ndipo lidzakwezedwa kupitirira mapiri angʼonoangʼono.” (Yes. 2:2) Yesaya anaoneratu kuti kulambira Yehova komwe ndi kulambira koyera kudzabwezeretsedwa komanso kukwezedwa ndipo zidzangokhala ngati kwaikidwa paphiri lalitali kwambiri. Ndiye kodi Ezekieli anali kuti pa nthawi imene ankaona masomphenya ochokera kwa Mulunguwa? Anali “paphiri lalitali kwambiri,” ndipo ankaona nyumba ya Yehova. (Ezek. 40:2) Choncho masomphenya a Ezekieliwa akutsimikizira kuti kulambira koyera kudzabwezeretsedwa.
17. Fotokozani mwachidule zimene zili mu Ezekieli chaputala 40 mpaka 48.
17 Tiyeni tione mwachidule zimene Ezekieli anaona komanso kumva mogwirizana ndi zimene zili mu Ezekieli chaputala 40 mpaka 48. Iye ankaonerera pamene mngelo ankayeza mageti, mpanda, mabwalo komanso malo opatulika a kachisi. (Ezek. 40-42) Kenako panachitika zinthu zochititsa chidwi kwambiri: Yehova anafika pakachisipo mwaulemerero. Yehova anapereka malangizo kwa anthu ake osamverawo, kwa ansembe komanso kwa atsogoleri. (Ezek. 43:1-12; 44:10-31; 45:9-12) Ezekieli anaona mtsinje ukutuluka m’malo opatulika n’kukathera m’Nyanja Yakufa. Mtsinjewo unabweretsa moyo komanso madalitso. (Ezek. 47:1-12) Kenako anaona dzikolo likugawidwa m’zigawo zosiyanasiyana ndipo kulambira koyera kunkachitika chapakati penipeni pa dzikolo. (Ezek. 45:1-8; 47:13–48:35) Kodi zimenezi zinkatanthauza chiyani? N’zoonekeratu kuti Yehova ankatsimikizira anthu ake kuti kulambira koyera kudzabwezeretsedwa komanso kudzakwezedwa. Anawatsimikizira kuti adzadalitsa nyumba yake yolambiriramo chifukwa iye azidzakhala mmenemo ndipo adzachititsa kuti madalitso adzayende kuchoka m’kachisi wake n’kumachiritsa anthu, kupereka moyo komanso kubweretsa bata m’dziko lolonjezedwa.
18. Kodi zimene zinali m’masomphenya a kachisi zinali zenizeni kapena zophiphiritsa? Fotokozani.
18 Funso lachiwiri, kodi zimene Ezekieli anaona m’masomphenyawa zinali zenizeni kapena zophiphiritsa? Zinali zophiphiritsa. N’zoonekeratu kuti Ezekieli ndi anzake amene anali nawo ku ukapolo, amene ankawafotokozera masomphenyawo, anaoneratu kuti zimene anaona m’masomphenyawo zinali zophiphiritsa. N’chifukwa chiyani tikutero? Musaiwale kuti Ezekieli anaona kachisi ameneyu ali “paphiri lalitali kwambiri.” Ngakhale kuti zimenezi zikugwirizana kwambiri ndi ulosi wa Yesaya, sizikugwirizana ndi malo amene panali kachisi. Kachisi wa Solomo anali paphiri la Moriya ku Yerusalemu ndipo tsiku lina ntchito yomanganso kachisiyu ikanachitikira kumeneko. Koma kodi limeneli linali ‘phiri lalitali kwambiri’? Ayi. Ndipotu phiri la Moriya linazunguliridwa ndi timapiri tina ting’onoting’ono timene tinali totalika mofanana ndi phiri limeneli kapena kuposa pang’ono. Komanso malo amene panali kachisi amene Ezekieli anaona, anali aakulu kwambiri. Chifukwa chakuti malowo anali aakulu kwambiri komanso anali kumpanda, sizikanatheka kuti akwane pamwamba pa phiri la Moriya. Ngakhale mzinda wa Yerusalemu wa m’nthawi ya Solomo unali waung’ono kwambiri moti malowa sakanakwanamo. Kuwonjezera pamenepo Ayuda omwe anachoka ku ukapolowo sakanayembekezera kuti mtsinje weniweni udzatuluka m’malo opatulika a kachisi n’kumakathirira Nyanja Yakufa n’kuchititsa kuti m’nyanja imeneyo mukhale zinthu zamoyo. Chomaliza, popeza kuti Dziko Lolonjezedwa linali lamapiri, zinali zosatheka kuti malire amene ankagawidwa kwa mafuko osiyanasiyana awadule moongoka monga mmene masomphenyawo akufotokozera. Choncho zimene zili m’masomphenyawa ndi zophiphiritsa osati zochitika zenizeni.
19-21. Kodi Yehova ankafuna kuti masomphenya amene Ezekieli anaona akhudze bwanji anthu, nanga n’chifukwa chiyani anayenera kuwakhudza mwa njira imeneyo?
19 Funso lachitatu, kodi masomphenyawa ankafunika kukhudza bwanji anthu a m’nthawi ya Ezekieli? Anthuwo ankayenera kuchita manyazi akaganizira mfundo zapamwamba za Yehova zokhudza kulambira koyera. Yehova anauza Ezekieli kuti ‘afotokozere nyumba ya Isiraeli za kachisiyu.’ Ezekieli ankayenera kufotokoza za kachisiyu mwatsatanetsatane kuti Aisiraeli “adziwe mmene anamangidwira.” N’chifukwa chiyani anthuwa ankayenera kuganizira za kachisiyu? Monga taonera, cholinga sichinali choti amange kachisiyu. Koma mogwirizana ndi zimene Yehova ananena, cholinga chake chinali choti “achite manyazi chifukwa cha zolakwa zawo.”—Werengani Ezekieli 43:10-12.
20 N’chifukwa chiyani masomphenya amenewa anachititsa kuti anthu a mtima wabwino akhudzike n’kuchita manyazi? Ganizirani zimene Ezekieli anauzidwa. Iye anauzidwa kuti: “Iwe mwana wa munthu, uchite chidwi, uonetsetse ndipo umvetsere mwatcheru zonse zimene ndikuuze zokhudza malangizo ndi malamulo a kachisi wa Yehova.” (Ezek. 44:5) Mobwerezabwereza, Ezekieli anamva zokhudza malangizo ndi malamulo amenewa. (Ezek. 43:11, 12; 44:24; 46:14) Ezekieli ankakumbutsidwanso mobwerezabwereza zokhudza miyezo ya Yehova kuphatikizapo kutalika kwa mkono umodzi komanso miyezo yolondola yoyezera kulemera kwa zinthu. (Ezek. 40:5; 45:10-12; yerekezerani ndi Miyambo 16:11.) Ndipotu maulendo oposa 50 m’masomphenya okhawa, Ezekieli analemba mawu a m’chilankhulo choyambirira amene anawamasulira kuti “kuyeza” komanso “muyezo.”
21 Kodi Yehova ankafuna kuuza chiyani anthu akewo potchula miyezo, kulemera kwa zinthu, malamulo komanso malangizo? Zikuoneka kuti ankawakumbutsa mwamphamvu mfundo yofunika yakuti: Yehova yekha ndi amene ali ndi udindo wopereka mfundo zimene tikuyenera kuzitsatira pa kulambira koyera. Amene anasiya kutsatira mfundo zimenezo ankayenera kuchita manyazi. Koma kodi masomphenyawa anaphunzitsa Ayudawo mfundo zimenezi m’njira ziti? Tiona zitsanzo zingapo m’mutu wotsatira. Zimenezi zitithandiza kuona mmene masomphenya ochititsa chidwiwa akutikhudzira masiku ano.
a Kachisi wauzimu ndi njira yolambirira Yehova movomerezeka kudzera mu nsembe ya Yesu Khristu. Ndipo timadziwa kuti anayamba kugwira ntchito mu 29 C.E.