LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • sn nyimbo 114
  • Buku la Mulungu Ndi Chuma Chamtengo Wapatali

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Buku la Mulungu Ndi Chuma Chamtengo Wapatali
  • Imbirani Yehova
  • Nkhani Zofanana
  • Buku Lake la Mulungu ni Cuma
    ‘Imbani Mokweza ndi Mosangalala’ kwa Yehova
  • Funani Cipulumutso ca Mulungu
    ‘Imbani Mokweza ndi Mosangalala’ kwa Yehova
Imbirani Yehova
sn nyimbo 114

Nyimbo 114

Buku la Mulungu Ndi Chuma Chamtengo Wapatali

(Miyambo 2:1)

1. Pali buku limene mawu ake

Amatibweretsera chimwemwe.

Mfundo zake zodabwitsa n’zamphamvu,

Zimathandiza ’khungu aone.

Bukuli ndi Baibulo loyera.

Olilemba anauziridwa,

Ankakonda Yehova M’lungu wawo.

Mzimu wake unawathandiza.

2. Analemba zokhudza chilengedwe.

Mmene M’lungu anachilengera.

Analembanso za Paradaiso

Ndiponsotu mmene anathera.

Analemba za mngelo winawake

Amene ananyoza Yehova.

Zinabweretsa chisoni pa anthu

Koma Yehova adzapambana.

3. Masiku ano tili ndi chimwemwe,

Ufumu wa Mulungu wayamba.

Yehova ’kupatsa chipulumutso

Kwa onse omwe amamukonda.

M’buku lake muli zosangalatsa,

Chakudya chamwanaalirenji.

Limatipatsa mtendere wambiri,

N’lofunika kuliwerengadi.

(Onaninso 2 Tim. 3:16; 2 Pet. 1:21.)

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2022)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2022 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani