Nyimbo 34
Zochita Zathu Zizigwirizana ndi Dzina Lathu
(Yesaya 43:10-12)
1. Yehova wamphamvu yonse wam’yaya,
Wangwiro m’chilungamo, m’chikondi.
Ndinu gwero la cho’nadi ndi nzeru,
Mulamula monga Mfumu m’mwamba.
Timakondwa pokutumikirani
Ndiponso kulengeza Ufumu.
(KOLASI)
Ndi mwayidi kukhala Mboni zanu,
Tichite monga mwa dzina lathu.
2. Pokutumikirani ndi abale
Timakhaladi mogwirizana.
Pophunzitsa ena cho’nadi chanu,
Timakhalanso osangalala.
Timadziwikanso ndi dzina lanu,
Ndi mwayi wathu kulitchukitsa.
(KOLASI)
Ndi mwayidi kukhala Mboni zanu,
Tichite monga mwa dzina lathu.
(Onaninso Deut. 32:4; Sal. 43:3; Dan. 2:20, 21.)