Nyimbo 150
Kudzipeleka na Mtima Wonse
Yopulinta
(Mateyu 9:37, 38)
Yehova amatipatsa
Zinthu zotisangalatsa.
Afuna tisangalale
Pamene timtumikila.
(KOLASI)
Mokondwa tifuna,
kudzipeleka.
Ndipo kulikonse,
tipita mofunitsitsa.
Kuno tili kuli nchito,
Yofunika kuigwila.
Tionetsa khama lathu,
Pothandiza anthu onse.
(KOLASI)
Mokondwa tifuna,
kudzipeleka.
Ndipo kulikonse,
tipita mofunitsitsa.
Kulikonse kuli anthu,
Na ku malo akutali.
Tipita kukalengeza
Uthenga kwa anthu onse.
(KOLASI)
Mokondwa tifuna,
kudzipeleka.
Ndipo kulikonse,
tipita mofunitsitsa.
(Onaninso Yoh. 4:35; Mac. 2:8; Arom. 10:14.)