NYIMBO 5
Nchito Zodabwitsa za Mulungu
Yopulinta
(Salimo 139)
1. Inu Mulungu mumadziŵa,
Nikagona olo nikauka.
Zilizonse ine nimaganiza,
Inu Atate Yehova,
muzidziŵa.
Munaona ziwalo zanga,
Pamene ninali kupangiwa.
Palibe cimene cinabisika.
Nidzakutamandani.
ndinu wamphamvu.
Nzelu zanu Mulungu n’zodabwitsa
Zimenezi nimadziŵa bwino.
Nikavutika mumanithandiza,
Mzimu wanu umanilimbitsa.
Yehova ningayende kuti
Kumene ningakubisameni?
M’manda kodi,
kumwamba olo m’nyanja?
Kulikonse imwe M’lungu munipeza.
(Onaninso Sal. 66: 3; 94: 19; Yer. 17:10.)