NYIMBO 28
Kukhala Bwenzi la Yehova
Yopulinta
(Salimo 15)
1. Ndani angakhale
Bwenzi lanu M’lungu?
Ndani mungakhulupilile?
Angakudziŵeni?
Ni uja amene
Amakumvelani.
Komanso wokhulupilika,
Wokonda co’nadi.
2. Ndani angakhale
Bwenzi lanu M’lungu?
Ndani amene mungakonde
Nakumudalitsa?
Ni uja amene
Amakukwezani.
Iye amanena zoona,
Ni woona mtima.
3. Nkhawa zathu zonse
Timakuuzani.
Ndipo mumatisamalila,
Tsiku lililonse.
Tifuna kukhala
Bwenzi lanu M’lungu.
Palibe bwenzi tingapeze
Monga inu M’lungu.
(Onaninso Sal. 139:1; 1 Pet. 5:6, 7.)