NYIMBO 52
Tidzipeleka Monga Akhristu
Yopulinta
(Aheberi 10:7, 9)
1. Yehova Mulungu wathu
Ni Mlengi wa zonse,
Zakumwamba na pa dziko—
Zinthu zonse n’zake.
Anatipatsanso moyo
Kuti ‘se tidziŵe
Iye ni Mulungu woona,
Tidzamutumikila.
2. Yesu anabatizika.
Anadzipeleka
Kutumikila Yehova,
Mpaka imfa yake.
Analonjeza Yehova,
Monga wodzozedwa,
Kuti adzamutumikila
Na moyo wake wonse.
3. Yehova, Atate wathu,
Ise tadzikana.
Tadzipeleka kwa imwe,
Ndise anthu anu.
Munatuma Mwana wanu,
Kuti atifele.
Na mitima yoyamikila,
Tidzalambila imwe.
(Onaninso Mat. 16:24; Maliko 8:34; Luka 9:23.)