NYIMBO 79
Aphunzitseni Kucilimika
Yopulinta
(Mateyu 28:19, 20)
1. Tikondwa kuphunzitsa anthu
Okonda coonadi.
Onani mmene akulila
M’njila ya coonadi.
(KOLASI)
Yehova, mvelani pempho
Lakuti muŵasamale
Mu dzina la Yesu Khristu
Tipemphela akhale ocilimika.
2. Tinali kuŵapemphelela
M’mavuto awo onse.
Tinali kuŵasamalila.
Yehova ‘wadalitsa.
(KOLASI)
Yehova, mvelani pempho
Lakuti muŵasamale
Mu dzina la Yesu Khristu
Tipemphela akhale ocilimika.
3. Akhale odalila M’lungu,
Na Mwana wake Yesu.
Amvele ndipo apilile,
Tifuna apambane.
(KOLASI)
Yehova, mvelani pempho
Lakuti muŵasamale
Mu dzina la Yesu Khristu
Tipemphela akhale ocilimika.
(Onaninso Luka 6:48; Mac. 5:42; Afil. 4:1.)