NYIMBO 82
“Onetsani Kuwala Kwanu”
Yopulinta
(Mateyu 5:16)
1. Yesu Mbuye wathu
Analamula,
Kuti tiwalitse
Kuwala kwathu.
Tiphunzitse ena
Mau a M’lungu.
Ndipo tiunikile
Kuwala kwake.
2. Ise tilengeze
Kwa anthu onse,
Mau a Yehova
Mulungu wathu.
Ndipo tigaŵile
Onse co’nadi,
Tiŵaphunzitse onse
Ofuna kumva.
3. Tikonde anansi
Tiŵasamale.
Makhalidwe athu
Aunikile.
Tidzakondweletsa
Atate wathu,
Ndipo tidzakhaladi
Mabwenzi Ake.
(Onaninso Sal. 119:130; Mat. 5:14, 15, 45; Akol. 4:6.)