NYIMBO 83
“Ku Nyumba ndi Nyumba”
Yopulinta
(Machitidwe 20:20)
1. Mwa cimwemwe tilalika
Ku nyumba ndi nyumba.
Mu mizinda na mu midzi
Konse timafika.
Tilengeza za Ufumu
Kwa onse pa dziko.
Tiŵauza: “Yesu Khristu
Tsopano ni Mfumu.”
2. Timalengeza kwa ena
Za cipulumutso,
Ca amene aitana
Pa dzina la M’lungu.
Koma ‘dzaitana bwanji
Ngati samudziŵa?
Conco tidzaŵadziŵitsa
Dzina la Yehova.
3. Tiyeni tilalikile
Ku nyumba ndi nyumba.
Anthu asankhe kumvela
Kapena kukana.
Dzina la Mulungu wathu
Tidzalilengeza.
Tisaleke kulalika
Ku nyumba ndi nyumba.
(Onaninso Mac. 2:21; Aroma 10:14.)