NYIMBO 96
Buku Lake la Mulungu ni Cuma
(Miyambo 2:1)
1. Pali buku limene mau ake,
Tikaŵelenga timakondwela.
Mfundo zake zodabwitsa n’zamphamvu;
Zimatipatsa ciyembekezo.
Bukulo ndilo Baibo yoyela
Analemba anauzilidwa.
Anali amuna okonda M’lungu.
Analemba mwa mphamvu ya mzimu.
2. Analemba nkhani za cilengedwe,
Mmene M’lungu anacipangila.
Analemba za moyo m’paradaiso
Komanso mmene unasinthila.
Analemba za mngelo wina wake
Amene anatsutsa Yehova.
Izi zinabweletsadi mavuto
Koma Yehova adzapambana.
3. Lomba yafika nthawi tikondwele,
Yesu wayamba kulamulila.
Tilalikile uthenga wabwino
Wonena za Ufumu wa M’lungu.
M’buku lake muli zosangalatsa;
Mulidi cakudya coculuka.
Limatipatsa mtendele wambili.
Tifunika tiziliŵelenga.
(Onaninso 2 Tim. 3:16; 2 Pet. 1:21.)