NYIMBO 143
Musaleke Kugwila Nchito, Kuyang’anila, na Kuyembekezela
Yopulinta
(Aroma 8: 20-25)
1. M’lungu wa nyengo na nthawi,
Dzina lake ni Yehova.
Posacedwa ‘dzayeletsa
Dzina lake loyela.
(KOLASI)
Moyo udzakhala wacimwemwe,
Pano padziko lapansi.
M’lungu watilonjeza.
2. Iye anakonza nthawi;
Yakuti Yesu abwele
Kudzacotsa ‘nthu oipa
Ndipo adzapambana.
(KOLASI)
Moyo udzakhala wacimwemwe,
Pano padziko lapansi.
M’lungu watilonjeza.
3. Olo tivutike bwanji,
Tidziŵa kuti Yehova,
Adzatipulumutsadi,
Na kuthetsa mavuto.
(KOLASI)
Moyo udzakhala wacimwemwe,
Pano padziko lapansi.
M’lungu watilonjeza.
(Onaninso Mat. 25:13; Luka 12:36.)