PHUNZILO 2
Kukambilana Mwacibadwa
2 Akorinto 2:17
ZOFUNIKILA: Muzikamba mwacibadwa ndiponso moona mtima, poonetsa mmene nkhaniyo imakukhudzilani imwe komanso omvela anu.
MOCITILA:
Mwa pemphelo, konzekelani bwino. Pemphelani kuti Mulungu akuthandizeni kuika maganizo anu pa uthenga wanu, osati pa inu mwini. Sumikani maganizo anu pa mfundo zazikulu zimene mufuna kuzimveketsa. Fotokozani mfundozo m’mawu anu-anu; osati kukamba mawuwo ndendende mmene awalembela iyai.
Kukamba mocokela pa mtima. Ganizilani cifukwa cake kuli kofunika kuti omvela anu amve nkhani yanu. Lunjikitsani maganizo anu pa iwo. Mukatelo, kaimidwe kanu, magesca, nkhope yanu, zonse zidzaonetsa kuona mtima kwanu, komanso mzimu waubwenzi.
Yang’anani omvela anu. Muziyang’ana omvela anu pokamba nawo. Pokamba nkhani, muziti mwayang’anako uyu, mwapita pa wina, basi telo, m’malo mongomwaza maso cisawawa pamwamba pa mitu ya omvela anu.