PHUNZILO 4
Kachulidwe ka Malemba Koyenela
Mateyu 22:41-45
ZOFUNIKILA: Konzekeletsani maganizo a omvela anu musanaŵelenge lemba.
MOCITILA:
Dziŵani cifukwa cimene mufuna kuŵelengela lembalo. Chulani lemba iliyonse mwa njila yokopa cidwi omvela anu ku mfundo yanu yofunika pa vesilo.
Muzichula Baibo kuonetsa maziko a mfundo zanu. Pokamba na ŵanthu okhulupilila za Mulungu, muzichula Baibo kuti ni Mawu a Mulungu, poonetsa kuti ndilo gwelo la nzelu zopambana.
Kopelani cidwi pa lembalo. Funsani funso limene lembalo lidzayankha. Kapena chulani vuto limene lembalo lidzaonetsa molithetsela. Kapenanso chulani mfundo imene lembalo lidzawathandiza kuimvetsa.