PHUNZILO 5
Kuŵelenga Bwino
1 Timoteyo 4:13
ZOFUNIKILA: Ŵelengani mokweza mawu, komanso ndendende mmene awalembela.
MOCITILA:
Konzekelani bwino. Dziŵani cifukwa cimene analembela nkhaniyo. Yesezani kuŵelenga magulu a mawu, osati liwu limodzi-limodzi. Samalani kuti musaikilepo mawu, kulumphila, kapena kuchula mawu ena ofananako. Samalani zizindikilo zonse za m’kalembedwe.
Chulani liwu lililonse moyenelela. Ngati simudziŵa mochulila bwino liwu, iyang’aneni mu dikishonale, kapena imvetseleni pa lekoding’i ya cofalitsa, kapena funsilani kwa munthu amene amaŵelenga bwino.
Muzikamba momveka bwino. Muzichula mawu mowamveketsa bwino, mutaŵelamutsa mutu wanu na kutsegula bwino pakamwa panu. Yesetsani kumawachula bwino-bwino mawu.