PHUNZILO 6
Kumveketsa Bwino Cifukwa Coŵelengela Lemba
Yohane 10:33-36
ZOFUNIKILA: Osangoŵelenga lemba basi n’kupita pa mfundo yotsatila iyai. Onetsetsani kuti omvela anu akuona bwino-bwino kugwilizana kwa lemba imene mwaŵelenga na mfundo imene mukufotokoza.
MOCITILA:
Onetsani mawu ofunikila. Mukaŵelenga lemba, onetsani mawu okhudzana na mfundo yanu yaikulu. Mungacite zimenezi mwa kuwabweleza mawu amenewo, kapena kufunsapo funso lopangitsa omvela anu kuwachula mawu ofunikilawo.
Gogomezani mfundo yanu. Ngati poŵelenga lemba mwamveketsa bwino cifukwa coliŵelengela, fotokozani mmene mawu ofunikila a pa lembalo amaonetsela cifukwaco.
Mveketsani mosavuta colinga ca lembalo. Pewani kufotokozapo mfundo zina zosathandiza kweni-kweni kumveketsa mfundo yaikulu. Malinga na zimene omvela anu akudziŵa kale pa nkhaniyo, onani kuti ni mfundo zingati zimene mungafunike kufotokoza kuti mumveketse mfundo yanu.