PHUNZILO 14
Kumveketsa Bwino Mfundo Zazikulu
Aheberi 8:1
ZOFUNIKILA: Thandizani omvela anu kukutsatilani m’nkhani yanu. Onetsani bwino mmene mfundo yaikulu iliyonse ikugwilizanila na colinga canu, komanso na mutu wa nkhani.
MOCITILA:
Khalani na colinga. Kodi colinga ca nkhani yanu ni kupeleka cidziŵitso, kukhutilitsa omvela anu pa nkhani inayake, kapena ni kuwalimbikitsa? Poikamba, onetsetsani kuti mfundo zazikulu zonse zikuthandizila kukwanilitsa colinga cimeneco.
Gogomezani mutu wa nkhani. M’nkhani yanu yonse, muzikumbutsanso mutu wanu wa nkhani mwa kubweleza mawu ake ofunika kwambili, kapena kuchula mawu ena ofanana nawo tanthauzo.
Mfundo zanu zazikulu zizimveka bwino komanso mosavuta. Sankhani cabe mfundo zothandizila kumveketsa mutu wa nkhani, zimenenso mungazifotokoze bwino m’nthawi imene mwapatsidwa. Cepetsani mfundo zikulu-zikulu, fotokozani iliyonse payokha-payokha, ndipo cokani pa ina kupita pa inzake moonekela bwino.