LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • th phunzilo 15 tsa. 18
  • Kukamba Motsimikiza

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kukamba Motsimikiza
  • Citani Khama pa Kuŵelenga na Kuphunzitsa
  • Nkhani Zofanana
  • Kukamba Mwaumoyo
    Citani Khama pa Kuŵelenga na Kuphunzitsa
  • Kukambilana Mwacibadwa
    Citani Khama pa Kuŵelenga na Kuphunzitsa
  • Nkhani Yophunzitsadi Kanthu Omvela
    Citani Khama pa Kuŵelenga na Kuphunzitsa
Citani Khama pa Kuŵelenga na Kuphunzitsa
th phunzilo 15 tsa. 18

PHUNZILO 15

Kukamba Motsimikiza

Lemba losagwila mawu

1 Atesalonika 1:5

ZOFUNIKILA: Onetsani kuti mumakhulupilila kuti zimene mukamba n’zoona komanso n’zofunika ngako.

MOCITILA:

  • Muzikonzekela mokwanila. Iŵelengeni nkhaniyo mpaka mutamvetsetsa mfundo zazikulu, komanso mmene Malemba amatsimikizila kuti n’za zoona. Yesani kufotokoza mfundo zanu mwa mawu ocepa komanso osavuta kumva. Unikani bwino mmene mfundozo zingawapindulitsile omvela anu. Pemphelelani mzimu woyela.

    Tumalangizo tothandizila

    Yesezani nkhani yanu mokweza mawu kuti muizolowele na kukaikamba bwino.

  • Seŵenzetsani mawu okhutilitsa omvela. M’malo mokamba mawu ndendende mmene anawalembela m’cofalitsa, akambeni m’mawu anu-anu. Lankhulani m’njila yoonetsa kuti mudziŵa zimene mukamba.

  • Kambani mocokela pansi pa mtima. Kambani na mawu omveka bwino. Komanso muziwayang’ana omvela anu.

    Tumalangizo tothandizila

    Kukamba motsimikiza sikutanthauza kukamba mopanda ulemu, modzimvela, kapena molamula. M’malo mwake, lankhulani mwaubwenzi komanso mwacikondi.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2022)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2022 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani