PHUNZILO 19
Yesetsani Kuwafika pa Mtima Omvela
Miyambo 3:1
ZOFUNIKILA: Thandizani omvela anu kuona kufunika kwa zimene akuphunzila kuti acitepo kanthu.
MOCITILA:
Thandizani omvela anu kudziunika. Funsani mafunso othandiza omvela anu kuunikanso maganizo awo.
Kambani mowalimbikitsa. Athandizeni kuganizila cifukwa cacikulu cocitila zinthu zabwino. Alimbikitseni kukhala na zolinga zabwino, monga kukonda Yehova, anthu anzawo, na ziphunzitso za m’Baibo. Kambilanani nawo omvela anu; osakamba mowalamula. M’malo mowacotsela ulemu, onetsetsani kuti atsala olimbikitsika, komanso ofunitsitsa kucitapo kanthu.
Apangitseni kumaonapo Yehova. Unikani mmene ziphunzitso za m’Baibo, mfundo zake, na malamulo opezekamo, zimaonetsela makhalidwe a Mulungu na cikondi cake pa ife. Limbikitsani omvela anu kukhala na mtima wofuna kudziŵa maganizo a Yehova kuti azicita zom’kondweletsa.