PHUNZILO 20
Mawu Otsiliza Ogwila Mtima
Mlaliki 12:13, 14
ZOFUNIKILA: M’mawu anu othela, limbikitsani omvela anu kuona ubwino wa zimene aphunzila kuti akazigwilitsile nchito.
MOCITILA:
Gwilizanitsani mawu anu otsiliza na mfundo yaikulu ya nkhani yanu. Bwelezaninso mfundo zazikulu, kapena zikambeninso m’mawu ena.
Limbikitsani omvela anu. Afotokozeleni zofunika kucita, komanso zifukwa zake zomveka. Kambani mocokela pa mtima, komanso mwa cidalilo.
Mawu anu otsiliza azikhala osavuta kumva komanso acidule. Osabweletsaponso mfundo zatsopano. Mwa mawu ocepa cabe, alimbikitseninso kucitapo kanthu.