Lamlungu, August 30
Yehova ali pafupi ndi anthu a mtima wosweka.—Sal. 34:18.
Ngakhale ena akuchitireni zopanda chilungamo, musamakayikire kuti Yehova amakukondani komanso amakuonani kuti ndinu wamtengo wapatali. Ngati ‘mukudzimvera chisoni mumtima’ muzikumbukira kuti Yehova anaona zabwino mumtima mwanu ndipo anakukokerani kwa iye. (Yoh. 6:44) Nthawi zonse iye ndi wokonzeka kukuthandizani chifukwa amakukondani kwambiri. Chitsanzo cha Yesu chingatithandize kudziwa mmene Yehova amamvera. Ali padziko lapansi, Yesu ankakomera mtima komanso kuchitira chifundo anthu omwe ankaonedwa ngati osafunika. (Mat. 9:9-12) Mwachitsanzo, mayi wina yemwe ankadwala matenda aakulu atagwira chovala chake pokhulupirira kuti achira, Yesu anamulimbikitsa komanso kumuyamikira chifukwa cha chikhulupiriro chake. (Maliko 5:25-34) Yesu anatengera makhalidwe a Atate wake. (Yoh. 14:9) Choncho musamakayikire kuti Yehova amakuonani kuti ndinu wamtengo wapatali ndiponso amaona makhalidwe anu abwino, kuphatikizapo chikhulupiriro ndi chikondi chanu kwa iye. w24.10 40:4-5
Lolemba, August 31
Sungani misozi yanga mʼthumba lanu lachikopa.—Sal. 56:8.
Pa moyo wake, Davide ankakumana ndi mavuto osiyanasiyana omwe ankamuchititsa kulira. Anthu ena ankadana naye ndipo ena omwe ankawakhulupirira anamukhumudwitsa. (1 Sam. 19:10, 11; 2 Sam. 15:10-14, 30) Pa nthawi ina iye analemba kuti: “Ndafooka chifukwa cha kuusa moyo kwanga. Usiku wonse ndimanyowetsa bedi langa ndi misozi, ndimalira ndipo misozi imadzaza pabedi panga.” (Sal. 6:6) Ngakhale kuti Davide anakumana ndi mavuto ambiri, sankakayikira kuti Yehova amamukonda. Iye analemba kuti: “Chifukwa Yehova adzamva mawu a kulira kwanga.” (Sal. 6:8) Mawu a mulemba lalero amasonyeza bwino mmene Yehova amatikondera. Davide ankamva ngati kuti Yehova akusunga misozi yake m’botolo kapena akuilemba m’buku. Davide sankakayikira kuti Yehova ankaona komanso kukumbukira mavuto ake. Ankakhulupirira kuti Atate wake wachikondi akudziwa zimene akukumana nazo komanso mmene zikumukhudzira. w24.12 51:11-12
Lachiwiri, September 1
Pitirizani kudziyesa kuti muone ngati mukadali ndi chikhulupiriro.—2 Akor. 13:5.
Sikuti tizingoyesetsa kuti tikule mwauzimu koma tiziyesetsanso kuti tikhalebe aakulu mwauzimu. Kuti zimenezi zitheke tiyenera kupewa kudzidalira. (1 Akor. 10:12) Tifunika “kupitiriza kudziyesa” kuti tione ngati tikupitabe patsogolo. M’kalata yake yopita kwa Akhristu a ku Kolose, mtumwi Paulo anatsindika kufunika kokhalabe olimba mwauzimu. Ngakhale kuti iwo anali aakulu kale mwauzimu, Paulo anawachenjeza kuti asapusitsidwe ndi nzeru za anthu. (Akol. 2:6-10) Epafura, yemwe zikuoneka kuti ankawadziwa bwino anthu a mumpingomo, ankawapempherera nthawi zonse kuti “apitirize kukhala olimba mwauzimu.” (Akol. 4:12) Kodi tikuphunzirapo chiyani? Paulo ndi Epafura ankadziwa kuti pamafunika khama komanso kuthandizidwa ndi Mulungu kuti munthu akhalebe wolimba mwauzimu. Iwo ankafuna kuti Akhristu a ku Kolose akhalebe olimba mwauzimu ngakhale kuti ankakumana ndi mavuto. w24.04 14:16-17