Kalata Yoyamba kwa Timoteyo
1 Ndine Paulo, amene ndinakhala mtumwi wa Khristu Yesu mwa lamulo la Mulungu, Mpulumutsi wathu, komanso Khristu Yesu, ciyembekezo cathu. 2 Ndikulembela iwe Timoteyo,* mwana wanga weniweni m’cikhulupililo kuti:
Cisomo, cifundo, ndi mtendele wa Mulungu Atate wathu ndi Khristu Yesu Ambuye wathu zikhale nawe.
3 Nditatsala pang’ono kupita ku Makedoniya, ndinakupempha kuti ukhalebe ku Efeso. Ndipo apanso ndikukupempha kuti ukhalebe komweko kuti uletse anthu ena kuti asamaphunzitse zosiyana ndi ziphunzitso zathu. 4 Uwauze kuti asamamvetsele nkhani zabodza ndi zokumbana* mibadwo ya makolo. Cifukwa n’zosathandiza, zimangoyambitsa nkhani zopanda umboni, ndipo siziphunzitsa anthu ciliconse cocokela kwa Mulungu cokhudza cikhulupililo. 5 Copelekela malangizowa n’cakuti tikhale ndi cikondi cocokela mumtima woyela, m’cikumbumtima cabwino, ndiponso m’cikhulupililo copanda cinyengo. 6 Anthu ena akana kutsatila malangizowa, ndipo asoceletsedwa n’kuyamba kutsatila nkhani zacabe-cabe. 7 Iwo amafuna kukhala aphunzitsi a cilamulo, koma samvetsa zimene akukamba kapena mfundo zimene akuziumilila.
8 Tikudziwa kuti Cilamulo n’cabwino ngati munthu akucitsatila bwino. 9 Ndipo lamulo siliikidwa cifukwa ca munthu wolungama. Koma limaikidwa cifukwa ca anthu osamvela malamulo, oukila, osaopa Mulungu, ocimwa, osakhulupilika, onyoza zinthu zopatulika, opha atate ndi amai ao, opha anthu, 10 aciwelewele,* amuna ogona amuna anzao,* akuba anthu, abodza, olumbila monama, ndiponso ocita ciliconse cotsutsana ndi ciphunzitso colondola, 11 comwe n’cogwilizana ndi uthenga wabwino waulemelelo wocokela kwa Mulungu wacimwemwe, umene anauika m’manja mwanga.
12 Ndikuyamika Khristu Yesu Ambuye wathu, amene anandipatsa mphamvu n’kundipatsanso utumiki cifukwa anaona kuti ndine wokhulupilika. 13 Anatelo ngakhale kuti kale ndinali kunyoza Mulungu, kuzunza anthu ake, ndiponso ndinali wacipongwe. Anandicitila cifundo cifukwa ndinali kucita zinthu mosadziwa, komanso ndinalibe cikhulupililo. 14 Koma Mulungu Ambuye wathu anandicitila cisomo, ndipo ndinalandilanso cikhulupililo ndi cikondi ca Khristu Yesu. 15 Mau akuti Khristu Yesu anabwela m’dziko kudzapulumutsa ocimwa, ndi mau oona komanso oyenela kuwabvomeleza ndi mtima wonse. Pa ocimwa amenewa, ine ndiye wocimwa kwambili. 16 Komabe, ndinacitilidwa cifundo kuti Khristu Yesu aonetse kuleza mtima kwake konse kudzela mwa ine munthu wocimwa kwambili, kuti cikhale citsanzo kwa amene adzamukhulupilila kuti akapeze moyo wasatha.
17 Kwa Mfumu yamuyaya, yosafa, yosaoneka, amene iye yekhayo ndiye Mulungu, kukhale ulemu ndi ulemelelo mpaka muyaya. Ameni.
18 Mwana wanga Timoteyo, ndikukupatsa malangizowa mogwilizana ndi maulosi amene anakambilatu za iwe, kuti mogwilizana ndi maulosiwo upitilize kumenya nkhondo yabwino. 19 Ukhale ndi cikhulupililo komanso cikumbumtima cabwino cimene anthu ena acikankhila kumbali, moti cikhulupililo cao casweka ngati ngalawa. 20 Ena mwa anthuwa ndi Hemenayo ndi Alekizanda, ndipo ndawapeleka kwa Satana kuti akalangidwa, aphunzilepo kanthu n’kusiya kunyoza Mulungu.