Citatu, July 9
Yehova Ambuye Wamkulu Koposa, conde, ndikumbukileni ndi kundipatsa mphamvu.—Ower. 16:28.
N’ciyani cimabwela m’maganizo mwanu mukamva dzina lakuti Samisoni? Ngati mumaganizila za mwamuna wamphamvu zodabwitsa, simunaphonye. Koma Samisoni anapanga cisankho coipa cimene pambuyo pake cinam’bweletsela mavuto aakulu kwambili. Ngakhale n’conco, Yehova anayang’ana pa kukhulupilika kumene Samisoni anaonetsa pom’tumikila. Anaonetsetsanso kuti nkhani yake yalembedwa m’Baibo kuti itipindulile. Yehova anaseŵenzetsa Samisoni kucita zinthu zodabwitsa kuti athandize anthu ake osankhidwa, Aisiraeli. Patapita zaka mahandiledi Samisoni atamwalila, Yehova anauzila mtumwi Paulo kuti aphatikize dzina la Samisoni pa mndandanda wa maina a anthu a cikhulupililo colimba. (Aheb. 11:32-34) Citsanzo ca Samisoni cingatilimbikitse. Iye anadalila Yehova ngakhale panthawi zovuta. Citsanzo ca Samisoni cingatilimbikitse kwambili, ndipo tingaphunzile zambili kwa iye. w23.09 2 ¶1-2
Cinayi, July 10
Zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu.—Afil. 4:6.
Cimene tingacite kuti tikhale opilila, ni kupemphela kwa Yehova mocokela pansi pa mtima nthawi zonse, na kumuuza nkhawa zathu. (1 Ates. 5:17) N’kutheka kuti pali pano simukukumana na mayeso aakulu. Ngakhale n’telo, muyenela kupemphabe citsogozo kwa Yehova mukakhumudwa kapena kuthedwa nzelu. Ngati pali pano mumatembenukila kwa Mulungu kuti akuthandizeni pa zovuta za tsiku na tsiku, simudzazengeleza kukacita zimenezo mukadzakumana na mavuto aakulu m’tsogolomu. Ndipo mudzakhala wotsimikiza kuti iye amadziŵa nthawi yabwino yokuthandizani, komanso mmene angacitile zimenezo. (Sal. 27:1, 3) Tikamapilila mavuto pali pano, tingadzapililenso cisautso cacikulu m’tsogolomu. (Aroma 5:3) N’cifukwa ciyani tikutelo? Abale na alongo athu ambili aona kuti akapilila mayeso oyesa cikhulupililo cawo, amatha kupililanso ena. Kupilila kumawayenga na kulimbitsa cidalilo cawo cakuti Yehova ni wokonzeka komanso wofunitsitsa kuwathandiza. Ndipo cidaliloco cimawathandiza kupilila mayeso alionse.—Yak 1:2-4. w23.07 3 ¶7-8
Cisanu, July 11
Ndavomela zimene wapempha.—Gen. 19:21.
Kudzicepetsa kwa Yehova na cifundo cake, zimamulimbikitsa kukhala wololela. Mwacitsanzo, kudzicepetsa kwa Yehova kuonaonekela bwino atatsala pang’ono kuwononga anthu oipa a mu Sodomu. Kupitila mwa angelo ake, Yehova anauza munthu wolungama Loti kuti athaŵile kumapili. Koma Loti anaopa kupita kumeneko. Conco, anacondelela Mulungu kuti amulole pamodzi na banja lake kuti athaŵile mu mzinda waung’ono wa Zowari, umene unayenelanso kuwonongedwa. Yehova akanafuna akanaumilila ndithu kuti Loti angotsatila malangizowo ndendende. Koma m’malo mwake, iye anamva pempho la Loti, ngakhale kuti izi zinatanthauza kusawononga mzinda wa Zowari. (Gen. 19:18-22) Patapita zaka mahandiledi, Yehova anaonetsa cifundo kwa anthu a ku Nineve. Anatuma mneneli Yona kukalengeza kuti mzindawo pamodzi na anthu oipa okhala mmenemo adzawonongedwa. Koma anthu a ku Nineve atalapa, Yehova anawamvela cisoni, ndipo sanauwononge mzindawo.—Yona 3:1, 10; 4:10, 11. w23.07 21 ¶5