NYIMBO 10
Tamandani Yehova, Mulungu Wathu!
Yopulinta
(Salimo 145:12)
1. Imbani mosangalala!
Lalikilani kwa onse:
“Yehova, Atate wathu
Adzalamulila kosatha!”
Iye anasankha Yesu Khristu
Kuti atilamulile.
Uzani onse za madalitso
Ufumu udzabweletsa.
(KOLASI)
Imbani mosangalala!
Tamandani Yehova Mfumu!
2. Imbani, sekelelani!
Lengezani za Yehova!
Na mtima wosangalala
Lalikilani za Ufumu.
Yehova M’lungu ni wacifundo,
Amasamalila onse.
Ndipo iye ni wodzicepetsa,
Amayankha mapemphelo.
(KOLASI)
Imbani mosangalala!
Tamandani Yehova Mfumu!
(Onaninso Sal. 89:27; 105:1; Yer. 33:11.)