NYIMBO 139
Yelekeza Uli M’dziko Latsopano
(Chivumbulutso 21:1-5)
1. Udzione, unione
Tili tonse m’dziko latsopano.
Ganizila za mtendele
Umene udzakhala m’dziko.
Anthu ali na cimwemwe
Mu ulamulilo wa M’lungu.
Dziko latsopano layandikila.
Na mtima wonse
tidzaimba mokondwa:
(KOLASI)
“Yehova M’lungu tiyamikila
Pa zonse imwe mwaticitila.
Mwacimwemwe ise tikuimbilani.
Zitamando na ulemu zonse n’zanu.”
2. Mudzione, munione,
Tili tonse m’dziko latsopano.
Zinthu zonse ni zabwino
Palibe zocititsa mantha.
Ananena, zacitika;
Monga mwa cifunilo cake.
Akufa onse adzaŵaukitsa;
Capamodzi
tidzaimbila Yehova:
(KOLASI)
“Yehova M’lungu tiyamikila
Pa zonse imwe mwaticitila.
Mwacimwemwe ise tikuimbilani.
Zitamando na ulemu zonse n’zanu.”
(Onaninso Sal. 37:10, 11; Yes. 65:17; Yoh. 5:28; 2 Pet. 3:13.)