Mawu Amunsi
a Yesu anakamba kuti cikondi n’cimene cimadziŵikitsa Akhristu oona. Kukonda abale na alongo athu kumatisonkhezela kukhala anthu obweletsa mtendele, opanda tsankho, komanso oceleza. Kucita izi nthawi zina kungakhale kovuta. M’nkhani ino, tikambilana malangizo amene angatithandize kuti tipitilize kukondana kwambili kucokela mu mtima.