Malifalensi a Kabuku ka Umoyo ndi Utumiki
© 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
MARCH 2-8
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU YESAYA 41-42
“Usacite Mantha”
Yang’anani kwa Yehova Kuti Akulimbikitseni
13 Yehova analimbikitsa Ayuda amene anali akapolo ku Babulo mwa kuwapatsa ciyembekezo cosangalatsa cakuti adzamasulidwa. Ngakhale n’telo iye anadziwa kuti iwo adzakumana ndi zovuta pa nthawi ya kumasulidwa kwawo. Yehova anakambilatu kuti kumapeto kwa ukapolo wawo, mfumu yamphamvu idzagonjetsa mzinda wa Babulo komanso mitundu yoyandikana ndi mzindawo. (Yes. 41:2-5) Kodi Ayuda anafunika kucita mantha? Ayi. Cifukwa zaka zambili izi zisanacitike, Yehova analimbikitsa atumiki ake powauza kuti: “Usacite mantha, cifukwa ndili ndi iwe. Usade nkhawa cifukwa ine ndine Mulungu wako.” (Welengani Yesaya 41:10-13.) Kodi Yehova anatanthauza ciyani pokamba kuti “ine ndine Mulungu wako”? Sanali kukumbutsa Ayuda kuti ayenela kumulambila, cifukwa iwo anali kudziwa kale zimenezi. Koma anali kuwakumbutsa kuti iye akali kumbali yawo ndipo adzawathandiza.—Sal. 118:6
Yesaya 41:10—“Usacite Mantha, Pakuti Ndili Nawe”
“Ndili nawe.” Yehova anauza anthu omulambila kuti sayenela kuopa cifukwa sali okha. Popeza Yehova amaona mabvuto amene amakumana nao komanso amamva mapemphelo ao, zili ngati iye ali pamodzi nao.—Salimo 34:15; 1 Petulo 3:12.
“Ine ndine Mulungu wako.” Yehova amakhazikitsa mtima pansi anthu amene amamulambila powakumbutsa kuti iye amaonabe kuti ndi Mulungu wao ndiponso kuti io ndi anthu ake. Atumiki a Mulungu sayenela kukaikila kuti iye adzawathandiza zivute zitani.—Salimo 118:6; Aroma 8:32; Aheberi 13:6.
“Ndikulimbitsa. Ndithu ndikuthandiza. Ndikugwila mwamphamvu ndi dzanja langa lamanja lacilungamo.” Yehova anagwilitsa nchito mfundo zitatu pofuna kutsindika mfundo imodzi yakuti iye sangalephele ngakhale pang’ono kuthandiza anthu ake. Anagwilitsa nchito mawu ofanizila poonetsa zimene iye amacita anthu ake akafunikila thandizo. Munthu akagwa, Mulungu amatambasula dzanja lake lamanja kuti amudzutse.—Yesaya 41:13.
Njila yaikulu imene Mulungu amalimbitsila komanso kuthandizila anthu ake ndi mwa kugwilitsa nchito Mau ake, Baibo. (Yoswa 1:8; Aheberi 4:12) Mwacitsanzo, m’Baibo muli malangizo anzelu othandiza anthu amene akukumana ndi mavuto monga umphawi, matenda kapena kufeledwa. (Miyambo 2:6, 7) Mulungu angagwilitsenso nchito mzimu wake woyela, kapena kuti mphamvu yake yogwila nchito, kuti apatse anthu ake mphamvu zopilila mavuto.—Yesaya 40:29; Luka 11:13.
“Usacite Mantha. Ndikuthandiza”
Mawu a Yehova amenewa ndi olimbikitsa kwambili. Yelekezelani kuti Yehova akuuza inu mawu amenewa. Vesi imeneyi siikamba kuti mukuyenda pamodzi ndi Yehova ndipo iye wakugwilani dzanja, ngakhale kuti zimenezo zingakhale zosangalatsa. Ngati mungayende naye pamodzi, ndiye kuti dzanja lake lamanja lingagwile dzanja lanu lamanzele. Koma Yehova amaseŵenzetsa ‘dzanja lake lamanja lacilungamo’ ndi kugwila ‘dzanja lanu lamanja,’ ngati kuti akukudonsani kuti mucoke pa malo oipa. Amacita izi, uku akukulimbikitsani kuti: “Usacite mantha. Ineyo ndikuthandiza.”
Kodi mumaona Yehova monga Tate wacikondi ndi Bwenzi lapamtima? Kodi mumakhulupilila kuti adzakuthandizani pamene mwakumana ndi mavuto? Yehova amakukondani ndipo amafuna kukuthandizani. Mukakumana ndi mavuto, Yehova amafuna kuti muzidzimva otetezeka cifukwa amakukondani kwambili. Zoona, iye ndi “thandizo lopezeka mosavuta pa nthawi ya masautso.”—Sal. 46:1.
Kufufuza Cuma Cauzimu
w01-CN 10/1 20 ¶3
Kodi Kukhulupilika Kumatanthauzanji?
Yehova anamuuza mnzake Abulahamu kuti: “Ine ndine cishango cako.” (Genesis 15:1; Yesaya 41:8) Iye sanangonena mauwa ,koma anacitadi zimenezo. Yehova anamuteteza ndi kum’pulumutsa Abulahamu ndi banja lake kwa Farao, ndi kwa Abimeleki. Anamuthandiza Abulahamu kupulumutsa Loti m’manja mwa mafumu anai amene anamugwila. Yehova anabwezeletsa mphamvu zobeleka za Abulahamu amene anali ndi zaka 100 ndi za Sara amene anali ndi zaka 90, kuti Mbewu imene anailonjeza idzabadwe kudzela mwa iwo. Yehova anali kulankhula ndi Abulahamu nthawi zonse kudzela m’masomphenya, maloto, ndi angelo amithenga. Inde, Yehova anakhulupilika kwa Abulahamu panthawi imene anali moyo ndiponso patapita nthawi yaitali iye atamwalila. Kwa zaka mazana ambili, Yehova anasungabe malonjezo ake kwa mbadwa za Abulahamu, mtundu wa Isiraeli, ngakhale kuti mtunduwu unali wopulupudza. Ubale wa Yehova ndi Abulahamu unasonyeza tanthauzo la kukhulupilika kwenikweni lomwe ndi kucitapo kanthu cifukwa ca cikondi.—Genesis, macaputala 12 mpaka 25.
MARCH 9-15
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU YESAYA 43-44
Ulosi Umene Unalembedwa Kukali Zaka 200 Kuti Ukwanilitsidwe
Bai-bulo Ni Buku Yocokela Kwa Mulungu
13 M’Baibulo muli maulosi osiyana-siyana. Ndipo ambili anakwanilitsika kale. Mwacitsanzo, Yesaya analosela kuti mzinda wa Babulo udzawonongedwa. (Yesaya 13:19) Mzindawo unali wocinjilizika kwambili. Unali ndi mpanda utali wa zipupa, mageti olimba, ndi mtsinje. Koma Yesaya anafotokoza mwatsatane-tsatane mmene adani adzaugonjetsela mzinda umenewo. Analosela kuti madzi adzauma mu mtsinje ndipo mageti adzasiyidwa otseguka. Iye anati adani adzagonjetsa mzindawo mosalimbana ndi aliyense. Anacita kuchula ngakhale dzina la munthu amene adzagonjetsa Babulo kuti ni Koresi.—Ŵelengani Yesaya 44:27–45:2; onani Zakumapeto 4.
14 Patapita zaka 200 kucokela pamene Yesaya analemba ulosi umenewu, panafika gulu la asilikali kuti awononge mzinda wa Babulo. Muganiza mtsogoleli wawo anali ndani? Monga mwa ulosi, anali Koresi, mfumu ya ku Perisiya. Zinthu zinali m’malo tsopano kuti mbali zonse zokhudza ulosi umenewo zikwanilitsike.
15 Usiku umene adani anazungulila mzinda, Ababulo anali paphwando. Mitima inali phee m’malo, ali ndi cidalilo conse kuti mzinda wawo unali wocinjilizika mokwana. Unali wochingika ndi mpanda utali wacipupa ndi mtsinje wozungulila. Koma kunja, Koresi ndi asilikali anali kukumba cimfolo copatutsila madzi kuti acepe mu mtsinjewo. Pamene madzi anapunguka kwambili, asilikali aku Perisiya aja anangoyenda ndi kuwoloka bwino-bwino. Nanga kodi cimpanda cacipupa citali-tali cija, anacigumula bwanji kuti aloŵe mkati mwa mzinda? Iyo siinali nkhani. Anangopeza kuti mageti ali citsegukile. Monga mwa mau a ulosi, asilikali aja analanda mzindawo popanda kumenya nkhondo.
Kodi Mumatha Kuona Zimene Zekariya Anaona?
AYUDA anakondwela ngako pamene Yehova “analimbikitsa mtima wa Koresi mfumu ya Perisiya,” kumasula Aisiraeli amene anali mu ukapolo ku Babulo kwa zaka zambili. Mfumuyo inalengeza kuti Ayuda abwelele kudziko la kwawo, “n’kukamanganso nyumba ya Yehova Mulungu wa Isiraeli.” (Ezara 1:1, 3) Cinali cilengezo cokondweletsa kwambili! Izi zinatanthauza kuti kulambila Mulungu woona kunali kudzabwezeletsedwa m’dziko limene iye anapatsa anthu ake.
Kufufuza Cuma Cauzimu
Mafunso Ocokela kwa Oŵelenga
Citsanzo caciŵili ni ulosi wonena za Koresi, yemwe anali kudzamasula Ayuda kucoka ku ukapolo, komanso kupeleka lamulo lomanganso kacisi wa Yehova. (Yes. 44:26–45:4) Mfumu Koresi ya ku Perisiya inakwanilitsa ulosi umenewu. (Ezara 1:1-4) Komabe, Koresi sanali kulambila Mulungu woona. Yehova anaseŵenzetsa Koresi kukwanilitsa ulosiwu popanda kumuphela ufulu wodzisankhila zocita pa amene ayenela kumulambila ayi.—Miy. 21:1.
MARCH 16-22
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU YESAYA 45-47
“Ine Ndine Mulungu Ndipo Palibe Aliyense Wofanana Ndi Ine”
“Dzina Lanu Liyeletsedwe”
14 Satana wakhala akucita zilizonse zimene angathe kuti alepheletse Yehova kukwanilitsa colinga cake. Koma walephela. Baibo imafotokoza zimene Yehova wakhala akucita, ndipo imaonetsa kuti palibe wolamulila wina wacikondi komanso wabwino monga Atate wathu, Yehova Mulungu. N’zoona kuti kupanduka kwa Satana na onse amene asankha kukhala kumbali yake kumamuŵaŵa kwambili Yehova. (Sal. 78:40) Ngakhale n’conco, pofuna kuthetsa nkhaniyi, iye wacita zinthu mwanzelu, moleza mtima, komanso mwacilungamo. Iye wacitanso zinthu zambili zoonetsa kuti ni wamphamvuzonse. Koposa zonse, cikondi cake cimaonekela m’zocita zake zonse. (1 Yoh. 4:8) Ndipo Yehova akupitilizabe kuyeletsa dzina lake.
cl-CN 42 ¶14
“Yehova Ali Ndi Mphamvu Zambiri”
14 Monga mmene tionere, Mulungu amagwiritsa ntchito mphamvu zake polenga, powononga, poteteza komanso pobwezeretsa zinthu. Mwachidule tingoti pochita chilichonse chimene chikufunika kuti akwaniritse zolinga zake. (Yesaya 46:10) Pa zochitika zina, Yehova amagwiritsa ntchito mphamvu zake pofuna kutiphunzitsa zinthu zofunika zokhudza iyeyo komanso mfundo zake. Chofunika kwambiri n’chakuti iye amagwiritsa ntchito mphamvu zake pofuna kukwaniritsa chifuniro chake, chomwe ndi kuyeretsa dzina lake pogwiritsa ntchito Ufumu wa Mesiya. Zimenezi zimasonyeza kuti ulamuliro wake ndi wabwino kwambiri. Ndipotu palibe chimene chingalepheretse cholinga chakechi.
Muzivomeleza Kuti Pali Zimene Simudziwa
18 Ngakhale kuti sitidziwa za mawa, tidziwa kuti Yehova watilonjeza moyo wosatha m’tsogolo. Ena akakhala kumwamba, ndipo ena pano padziko lapansi. Ndipo tidziwa kuti sanganame komanso kuti palibe ciliconse cingamulepheletse kukwanilitsa malonjezo ake onse. (Tito 1:2) Iye yekha ndiye amene ‘amanenelatu zimene zidzacitike, ndipo kale kwambili ananenelatu zinthu zimene zidzacitike m’tsogolo.’ Umu ndi mmene zinalili kumbuyoku ndipo zidzakhalanso conco m’tsogolo. (Yes. 46:10) Sitikayika konse kuti palibe cimene cingalepheletse Yehova kutikonda. (Aroma 8:35-39) Adzatipatsa nzelu, citonthozo, komanso mphamvu zimene tikufunikila kuti tipilile zilizonse zimene zingatigwele. Ndife otsimikiza kuti Yehova adzatithandiza ndi kutidalitsa.—Yer. 17:7, 8.
Kalata Yotithandiza Kupilila Mpaka Mapeto
13 Pomwe anali kuyembekezela kuti athaŵe, Akhristu a Ciheberiwo anafunika kukhala na umoyo wosalila zambili. Iwo anafunika kutsatila uphungu umene anapatsidwa wakuti “musamakonde ndalama.” (Ŵelengani Aheberi 13:5.) Ena a iwo anali atakumanapo kale na mavuto azacuma komanso njala yaikulu. (Aheb. 10:32-34) Ngakhale kuti pa nthawi ina iwo anali okonzeka kupilila zovuta kaamba ka uthenga wabwino, n’kutheka kuti ena a iwo anayamba kuona kuti kukhala na zinthu zambili za kuthupi n’kumene kukanawateteza. Koma ndalama sizinakakwanitsa kuwateteza ku ciwonongeko cimene cinali kubwela. (Yak. 5:3) Ndipo cikanakhala covuta kuti anthu amene anali na cuma cambili athaŵe n’kusiya nyumba zawo komanso katundu wawo.
14 Kukhala na cikhulupililo colimba cakuti mapeto a dzikoli afika posacedwa, kudzatithandiza kupewa kukondetsetsa cuma. Pa nthawiyo anthu adzatayila, “siliva wawo . . . m’misewu.” Adzatelo cifukwa adzazindikila kuti “siliva wawo kapena golide wawo sadzatha kuwapulumutsa pa tsiku limene Yehova adzasonyeze mkwiyo wake waukulu.” (Ezek. 7:19) M’malo mothela nthawi yathu kufunafuna ndalama zambili, tiyenela kupanga zisankho zimene zidzatithandiza kukhala umoyo wosalila zambili, kwinaku tikutumikila Yehova. Izi zitanthauza kuti tiyenela kupewa nkhongole zosafunikila. Tizipewanso kuseŵenzetsa nthawi yathu yoculuka kusamalila katundu amene tili naye kale. Kuwonjezela apo, tizisamala kuti tisamaone cuma kukhala cinthu cofunika kwambili pa umoyo wathu. (Mat. 6:19, 24) Pamene tikuyandikila mapeto a dongosolo lino la zinthu, cikhulupililo cathu cidzayesedwa pa nkhani yokondetsetsa zinthu zakuthupi komanso pa nkhani zina.
Kufufuza Cuma Cauzimu
w11-CN 1/1 14 ¶2-3
Kodi Mulungu Anadziwiratu Kuti Adamu ndi Hava Adzachimwa?
Malemba amasonyezanso kuti Yehova ndi “wanzeru yekhayo.” (Aroma 16:27) Angelo a Mulungu anaona zinthu zambiri zimene iye anachita zosonyeza kuti alidi ndi nzeru zopanda malire. Yehova atalenga zinthu zapadziko lapansi, iwo “anayamba kufuula ndi chisangalalo.” (Yobu 38:4-7) Ndi zosakayikitsa kuti angelo amenewa ankaonetsetsa mwachidwi zonse zimene zinkachitika m’munda wa Edeni. Angelo anaona Mulungu akulenga kumwamba ndiponso zinthu zochititsa chidwi kwambiri za padziko lapansi. Ndiye kodi zikanakhala zomveka kwa iwo kuona kuti kenako Mulungu wanzeru ameneyu, akulenganso anthu awiri koma akudziwiratu kuti anthuwo sapita patali? N’zoonekeratu kuti zimenezi zikanakhala zosamveka.
Komabe mwina wina anganene kuti, ‘Kodi zingatheke bwanji kuti Mulungu, yemwe ndi wanzeru zonse, asadziwiretu za m’tsogolo?’ N’zoonadi kuti Yehova ali ndi nzeru zazikulu ndipo amatha kudziwa “za mapeto kuyambira pa chiyambi.” (Yesaya 46:9, 10) Koma iye sakakamizika kugwiritsa ntchito nzeru zake zonse zodziwiratu zinthu monga mmene zilili kuti kawirikawiri sagwiritsira ntchito mphamvu zake zonse pochita zinthu. Yehova amasankha mwanzeru zinthu zimene akufuna kuzidziwiratu. Ndipo amachita zimenezo akaona kuti ndi pofunikira komanso ngati zikugwirizana ndi mmene zinthu zili pa nthawiyo.
MARCH 23-29
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU YESAYA 48-49
Mapindu Amene Timapeza Tikamamvela Yehova
Mmene Tingapangile Zisankho Zabwino
1. Kodi Baibo ingakuthandizeni bwanji kupanga zisankho zabwino?
Musanapange cisankho, yambani mwapemphela kwa Yehova kuti akuthandizeni. Kenako, fufuzani m’Baibo kuti mudziŵe mmene iye akuionela nkhaniyo. (Ŵelengani Miyambo 2:3-6.) Pa nkhani zina, Yehova amapeleka lamulo lacindunji lomveka bwino. Zikakhala conco, cisankho canzelu cimene muyenela kupanga ni kungotsatila lamulo limenelo.
Koma bwanji ngati palibe lamulo lacindunji la m’Baibo lokuuzani zocita? Yehova adzakutsogolelanibe mu “njila imene muyenela kuyendamo.” (Yesaya 48:17) Kodi amacita zimenezo motani? Mwa kupeleka mfundo za m’Baibo zimene zingakutsogoleleni. Kodi mfundo za m’Baibo n’ciyani? Ni mfundo za coonadi zotiunikila maganizo a Mulungu na mmene amaonela zinthu. Nthawi zambili tikaŵelenga nkhani m’Baibo, timatha kudziŵa mmene Yehova akuionela nkhaniyo.
ijwbq-CN nkhani 44 ¶2-3
Kodi Baibulo Limati Mungasankhe Nokha Zochita Kapena Mulungu Analemberatu Tsogolo Lanu?
● Mulungu analenga anthu m’chifaniziro chake. (Genesis 1:26) Nyama zimangoyendera nzeru zachibadwa koma ife anthu timafanana ndi Mlengi wathu chifukwa chakuti timatha kusonyeza makhalidwe monga chikondi ndi chilungamo. Mofanananso ndi Mlengi wathu, tili ndi ufulu wosankha.
● Zimene timasankha zimakhudza tsogolo lathu. Baibulo limatilimbikitsa kuti ‘tisankhe moyo mwa kumvera mawu a Yehova Mulungu,’ kapena kuti tisankhe kumvera malamulo ake. (Deuteronomo 30:19, 20) Tikanakhala kuti tilibe ufulu wosankha, mawu amenewa akanakhala osamveka ndipo tikananena kuti Mulungu ndi wankhanza kwambiri potiuza zimenezi. M’malo motikakamiza kuchita zimene iye amanena, Mulungu amatichonderera mokoma mtima kuti: “Zingakhale bwino kwambiri mutamvera malamulo anga! Mukatero mtendere wanu udzakhala ngati mtsinje.”—Yesaya 48:18.
“Dzilimbitseni Pamaziko a Cikhulupililo Canu Coyela Kopambana”
8 Palembali, Yehova akutikumbutsa kuti zinthu zimatiyendela bwino ngati timamumvela. Iye walonjeza mapindu aŵili amene tidzapeza tikakhala omvela. Loyamba, mtendele wathu udzakhala ngati mtsinje wabata, wokhala ndi madzi ambili amene saphwila. Laciŵili, cilungamo cathu cidzakhala ngati mafunde a m’nyanja. Mukakhala m’mbali mwa nyanja ndi kuyang’ana mmene mafunde amayendela, mumadziŵa kuti mafundewo ndi acikhalile ndipo adzapitiliza kuyenda m’nyanja imeneyo kwamuyaya. Yehova wanena kuti, cilungamo canu naconso sicidzatha ngati mumumvela. Malinga ngati muyesetsa kukhala okhulupilika kwa iye, sadzalola kuti mugwedezeke. (Ŵelengani Salimo 55:22.) Kodi malonjezo ogwila mtima amenewa salimbitsa cikhulupililo canu pa Yehova ndi malamulo ake olungama?
Kufufuza Cuma Cauzimu
ip-2-CN 144-145 ¶16-20
“Nthawi Yondikomela”
16 Kodi nthaŵi yokoma imeneyi inali liti? M’zochitika zoyambirira, mawuŵa anali mbali ya ulosi wa kubwezeretsedwa ndipo analosera kuti Ayuda adzabwerako ku ukapolo. Mtundu wa Israyeli unakhala ndi nthaŵi yokoma pamene anakhoza ‘kukhazikitsa dziko’ ndi kukhalanso “m’zoloŵa zopasuka m’malo abwinja.” (Yesaya 49:8b) Iwo sanalinso “omangidwa” ku Babulo. Paulendo wawo wobwerera kwawo, Yehova anaonetsetsa kuti iwo sanakhale ndi “njala” kapena “ludzu,” ngakhalenso ‘thukuta pena dzuŵa silinawatenthe.’ Aisrayeli omwazikanawo anabwerera kwawo ‘kuchokera kutali, kuchokera kumpoto ndi kumadzulo.’ (Yesaya 49:9-12) Ngakhale kuti pali kukwaniritsidwa kochititsa chidwi koyambirira kumeneku, Baibulo limasonyeza kuti ulosi umenewu ukuchitikanso m’njira zina.
17 Choyamba, pakubadwa kwa Yesu, angelo analengeza kuti anthu akhale ndi mtendere ndi kukondweretsedwa, kapena kuti kuyanjidwa, ndi Mulungu. (Luka 2:13, 14) Si anthu onse amene anakondwera nawo chonchi, koma okhawo amene anakhulupirira Yesu. Kenako Yesu anaŵerenga poyera ulosi wa pa Yesaya 61:1, 2 ndipo anati ulosiwo unali kugwira ntchito pa iye monga wolengeza “chaka chosankhika cha Ambuye.” (Luka 4:17-21) Mtumwi Paulo ananena kuti Kristu anatetezedwa mwapadera ndi Yehova m’masiku a thupi lake. (Aheberi 5:7-9) Motero nthaŵi yokondweretsedwa imeneyi ikunena za mmene Mulungu anayanjira Yesu pamene anali ndi moyo monga munthu.
18 Komabe, pali kukwaniritsidwa kwinanso kwa ulosiwu. Atagwira mawu a Yesaya onena za nthaŵi yokoma, Paulo ananenanso kuti: “Taonani, tsopano ndiyo nyengo yabwino yolandiridwa, taonani, tsopano ndilo tsiku la chipulumutso.” (2 Akorinto 6:2) Paulo analemba mawu ameneŵa patapita zaka 22 Yesu atafa. Mwachionekere, ndi kubadwa kwa mpingo wachikristu pa Pentekoste wa mu 33 C.E., Yehova anafutukula chaka chake chomukomera kotero kuti aphatikizepo otsatira Yesu odzozedwa.
19 Nanga bwanji otsatira Yesu a masiku ano amene siodzozedwa monga oloŵa ufumu wakumwamba wa Mulungu? Kodi amene ali ndi chiyembekezo cha padziko lapansi angapindule ndi nyengo yolandiridwa imeneyi? Inde. Buku la m’Baibulo la Chivumbulutso limasonyeza kuti ino ndi nthaŵi yomukomera Yehova chifukwa cha khamu lalikulu limene ‘lidzatuluka m’chisautso chachikulu’ kuti likasangalale ndi moyo padziko lapansi la paradaiso. (Chivumbulutso 7:13-17) Motero, Akristu onse angatengerepo mwayi pa nyengo yokhala ndi malire imeneyi yomwe Yehova akukondwera ndi anthu opanda ungwiro.
20 Asanalengeze za nthaŵi yolandirika ya Yehova, mtumwi Paulo anayamba wapereka chenjezo. Akudandaulira Akristu kuti ‘asalandire chisomo cha Mulungu kwachabe.’ (2 Akorinto 6:1) Moyenerera, Akristu amagwiritsa ntchito mpata uliwonse kuti asangalatse Mulungu ndi kuchita chifuno chake. (Aefeso 5:15, 16) Amapindula potsatira uphungu wa Paulo wakuti: “Tapenyani, abale, kuti kapena ukakhale mwa wina wa inu mtima woipa wosakhulupira, wakulekana ndi Mulungu wamoyo; komatu dandauliranani nokha tsiku ndi tsiku, pamene patchedwa, Lero; kuti angaumitsidwe wina wa inu ndi chenjerero la uchimo.”—Aheberi 3:12, 13.
APRIL 6-12
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU YESAYA 50-51
Muzimvela Yesu Amene Anaphunzitsidwa ndi Mulungu
Kuphunzitsa Atumiki a Ufumu
5 Yehova anaphunzitsa Mwana wake pasadakhale mocitila utumiki wake padziko lapansi. Taganizilani ulosi umene umafotokoza za ubale wa pakati pa Mlangizi Wamkulu ameneyu ndi Mwana wake woyamba kubadwa. (Ŵelengani Yesaya 50:4, 5.) Ulosiwu umanena kuti Yehova anali kudzutsa Mwana wakeyo “m’mawa uliwonse.” Mau ophiphilitsa amenewa amatikumbutsa zimene mphunzitsi amacita pothandiza mwana wa sukulu m’mawa n’colinga cakuti amuphunzitse. Buku lina lofotokoza Baibulo limati: “Monga . . . mwana wa sukulu, Yehova anali kumulowetsa m’kalasi ndi kumuphunzitsa zimene afunika kulalikila ndi mmene ayenela kulalikilila.” Panthawi imene Yesu analandila maphunzilo amenewo, Yehova anamuphunzitsa ‘zoyenela kunena ndi kulankhula.” (Yoh. 12:49) Atateyo anaphunzitsanso Mwana wake mmene angaphunzitsile ena. Ali padziko lapansi, Yesu anagwilitsila nchito bwino zimene anaphunzila mwa kukwanilitsa utumiki wake komanso mwa kuphunzitsa otsatila ake mmene angacitile utumiki wao.
cf-CN 133 ¶13
“Ndimakonda Atate”
13 Mwanayu asanabwere padziko lapansi, anaphunzira zambiri kuchokera kwa Atate wake. Ulosi wopezeka pa Yesaya 50:4-6 umasonyeza kuti Yehova anaphunzitsa Mwana wake mwapadera kwambiri kuti akwaniritse udindo wake monga Mesiya. Ngakhale kuti zina mwa zinthu zimene anaphunzirazo zinali zokhudza mavuto amene Wodzozedwa wa Yehova adzakumane nawo, Mwanayu anaphunzirabe modzipereka. Kenako Yesu anabwera padziko lapansi ndipo ngakhale atakula, sanasiye kupita kunyumba ya Atate wake kukalambira komanso kukaphunzira zinthu zimene Yehova ankafuna kuti anthu azidziwe. N’chifukwa chake Baibulo limanena kuti nthawi zonse Yesu ankapezeka pakachisi ndiponso kusunagoge. (Luka 4:16; 19:47) Kuti tipitirize kukonda Yehova, nthawi zonse tiyenera kumapezeka pamisonkhano ya Chikhristu, pamene timalambira Yehova ndi kuphunzira zambiri zokhudza iyeyo.
Kufufuza Cuma Cauzimu
ip-2-CN 166 ¶2-3
Mawu Otonthoza kwa Anthu a Mulungu
2 Kwa anthu amene ali mu Yuda amene akuika mitima yawo pa iye, Yehova akuti: “Ndimvereni, inu anthu amene mukufunafuna chilungamo, Inu amene mukufunafuna Yehova.” (Yesaya 51:1a) ‘Kufunafuna chilungamo’ kukusonyeza kuchitapo kanthu. Amene ‘akufunafuna chilungamo’ sadzangonena chabe kuti ali anthu a Mulungu. Adzayesetsa ndi changu chonse kukhala olungama ndi kukhala mogwirizana ndi chifuno cha Mulungu. (Salmo 34:15; Miyambo 21:21) Adzayang’ana kwa Yehova monga Gwero lokhalo la chilungamo, ndipo ‘adzafunafuna Yehova.’ (Salmo 11:7; 145:17) Sikuti iwo adzakhala asanadziŵebe kuti Yehova ndani kapena kuti n’kumufikira motani m’pemphero ayi. Koma, iwo adzayesetsa kuyandikana naye kwambiri, kumulambira, kupemphera kwa iye, ndi kufunafuna kuti aziwatsogolera pa zonse zimene achita.
3 Komabe, awo amene akufunafunadi chilungamo mu Yuda ndi ochepa kwambiri, ndipo zimenezi zikhoza kuwachititsa mantha ndi kuwakhumudwitsa kwambiri. Motero pogwiritsa ntchito fanizo la malo okhumbapo miyala, Yehova akuwalimbikitsa kuti: “Yangʼanani kuthanthwe limene munasemedwako, ndi pamalo okumbapo miyala pamene munakumbidwa. Yangʼanani kwa atate anu Abulahamu, ndi kwa Sara amene anakuberekani. Chifukwa Abulahamu anali munthu mmodzi pamene ndinamuitana, koma ndinamudalitsa ndi kuchulukitsa mbadwa zake.” (Yesaya 51:1b, 2) ‘Thanthwe’ limene Ayuda anasemedwako ndi Abulahamu, munthu wochuka m’mbiri yakale amene mtundu wa Isiraeli umamunyadira kwambiri. (Mateyu 3:9; Yohane 8:33, 39) Ndiye kholo lake laumunthu la mtunduwo. ‘Malo okhumbapo miyala’ ndi Sara, amene m’mimba mwake munatuluka Isake kholo la Isiraeli.
APRIL 13-19
CUMA COPEZA M’MAU A MULUNGU YESAYA 52-53
Yesu Anaonetsa Cikondi Cacikulu Zedi!
w10-CN 11/15 7 ¶2
Achinyamata, Pewani Kutengera Zochita za Anzanu
2 Kodi inu mumafuna kuchita zoti musangalatse anzanu? Ngati ndi choncho n’chifukwa chiyani? Kodi mwina mumafuna kuti iwo azikukondani? Maganizo amenewa paokha si olakwika. Ngakhale anthu akuluakulu amafunanso kukondedwa ndi anzawo. Palibe amene amasangalala akamasalidwa, kaya akhale wamng’ono kapena wamkulu. Komabe si nthawi zonse pamene anthu amakuyamikirani chifukwa chokana kuchita zoipa. Ngakhalenso Yesu anakumanapo ndi vuto limeneli koma iye ankachitabe zabwino. Anthu ena ankamutsatira ndipo anakhala ophunzira ake pomwe ena ankanyoza Mwana wa Mulunguyu ndipo ‘ankamuona ngati wopanda pake.’—Yes. 53:3.
Yesetsani Kukhala Ofatsa Kuti Mukondweletse Yehova
15 Cakumapeto kwa moyo wake padziko lapansi, Yesu anavutika maganizo kwambili. Iye anali kudziŵa kuti adzazunzidwa kwambili, komanso kuti adzaphedwa. (Yoh. 3:14, 15; Agal. 3:13) Patatsala miyezi ingapo asanaphedwe, Yesu anakamba kuti anavutika kwambili mumtima. (Luka 12:50) Ndipo kutatsala masiku ocepa asanaphedwe, iye anati: “Moyo wanga ukusautsika.” Yesu anaonetsa kuti ni wodzicepetsa komanso wogonjela pamene anakhuthulila Mulungu nkhawa zake m’pemphelo. Iye anati: “Atate ndipulumutseni ku nthawi yosautsayi. Komabe nthawi imeneyi iyenela kundifikila pakuti ndiye cifukwa cake ndinabwela. Atate lemekezani dzina lanu.” (Yoh. 12:27, 28) Nthawiyo itafika, Yesu molimba mtima anadzipeleka kwa adani a Mulungu, ndipo iwo anamupha mwankhanza ndi momunyazitsa. Ngakhale anavutika maganizo komanso kuzunzidwa kwambili, iye anacitabe cifunilo ca Mulungu. Ndithudi, Yesu n’citsanzo cabwino kwambili pankhani yokhalabe ofatsa.
Kufufuza Cuma Cauzimu
Yehova Amafuna Anthu Ake Kukhala Oyela
9Kulambila koyela. Sitifunika kukhala na mbali iliyonse m’kulambila konama. Pamene Aisiraeli anali akapolo ku Babulo, anali kukhala pakati pa anthu acipembedzo cacikunja ca makhalidwe oipa. Yesaya anakambilatu kuti Aisiraeli adzabwelela kwawo ku Isiraeli kukakhazikitsanso kulambila koyela. Ndipo Yehova anawauza kuti: “Tulukani mmenemo! Musakhudze cinthu ciliconse codetsedwa. Cokani pakati pake! Khalani oyela.” Sanafunikile kusakaniza kulambila kwawo Mulungu na ziphunzitso, makhalidwe, kapena miyambo ya cipembedzo conama ca ku Babulo.—Yesaya 52:11.
10Ngakhale masiku ano, Akhristu oona amapewa zipembedzo zonama. (Ŵelengani 1 Akorinto 10:21.) Kuzungulila dziko lonse, miyambo yambili, zikhalidwe, na zikhulupililo, zimazikidwa pa ziphunzitso zonama. Mwacitsanzo, anthu ambili amakhulupilila kuti munthu akafa, mzimu umacoka m’thupi mwake kukakhala kwina. Ndipo pamakhala zocitika zambili zokhudzana na cikhulupililo cimeneci. (Mlaliki 9:5, 6, 10) Akhristu ayenela kupewa miyambo imeneyo. N’zoona kuti acibanja angatikakamize kuti ticiteko miyambo ina. Koma pofuna kukhalabe oyela kwa Yehova, sitigonja ku mayeselo amenewo.—Machitidwe 5:29.
APRIL 20-26
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU YESAYA 54-55
Mungadzimane Ciani Kuti Muphunzitsidwe ndi Yehova?
w09-CN 9/15 21 ¶3
Maphunziro Ochokera kwa Mulungu Ndi Opambanadi
3 Chifukwa chakuti Yehova ndi wabwino, amalakalaka kuphunzitsa anthu opanda ungwiro. Polosera za Akhristu odzozedwa, lemba la Yesaya 54:13 limati: “Ana ako onse azidzaphunzitsidwa ndi Yehova, ndipo mtendere wa ana ako udzakhala wochuluka.” Mfundo imeneyi imagwiranso ntchito kwa “nkhosa zina” za Khristu. (Yoh. 10:16) Zimenezi zikuoneka bwino mu ulosi umene ukukwaniritsidwa masiku ano. Yesaya anaona m’masomphenya anthu a mitundu yonse akukhamukira ku kulambira koona. Iye anafotokoza kuti anthuwo akuuzana kuti: “Tiyeni tipite kukakwera phiri la Yehova, tipite kunyumba ya Mulungu wa Yakobo. Iye akatiphunzitsa njira zake, ndipo ife tidzayenda mʼnjira zakezo.” (Yes. 2:1-3) Ndi mwayi waukuludi kuphunzitsidwa ndi Mulungu!
w18 11 4 ¶6-7
“Gula Coonadi Ndipo Usacigulitse”
6 Ŵelengani Yesaya 55:1-3. Mawu a Yehova amene Yesaya analemba pa mavesi amenewa, atithandiza kumvetsa bwino zimene kugula coonadi kumatanthauza. Pa lembali, Yehova anayelekezela mawu ake na madzi, mkaka, na vinyo. Mofanana ndi madzi akumwa ozizila bwino, coonadi ca m’Mawu a Mulungu cimatitsitsimula. Komanso, monga mmene mkaka umalimbitsila matupi athu na kuthandiza ana kukula, mawu a Yehova amatilimbikitsa na kutithandiza kukula mwauzimu. Kuwonjezela apo, mawu a Yehova ali monga vinyo. Motani? Baibo imakamba kuti vinyo amabweletsa cisangalalo. (Sal. 104:15) Conco, pamene Yehova anauza anthu ake kuti ‘agule vinyo,’ anaonetsa kuti tikamatsatila mfundo za m’Mawu ake mu umoyo wathu, timakhala acimwemwe. (Sal. 19:8) Ndithudi, amenewa ni mawu ofanizila ocititsa cidwi, oonetsa mapindu amene timapeza ngati tiphunzila na kuseŵenzetsa coonadi ca m’Baibo. Conco, tingakambe kuti, timagula coonadi mwa kucita khama kuphunzila Mawu a Mulungu na kuseŵenzetsa zimene timaphunzila. Lomba tiyeni tikambilane zinthu zisanu zimene tingatailepo kuti tigule coonadi.
KODI MUNATAILAPO CIANI KUTI MUGULE COONADI?
7 Nthawi. Ici ni cinthu cimene munthu aliyense amatailapo kuti apeze coonadi. Zimafuna nthawi kuti munthu amvetsele uthenga wa Ufumu na kuti aziŵelenga Baibo na mabuku ophunzilila Baibo. Zimafunanso nthawi kuti tizicita phunzilo laumwini, kukonzekela misonkhano komanso kukapezekapo. Conco, timafunika ‘kugula nthawi,’ kapena kuti kuiwombola ku zinthu zosafunika kweni-kweni. (Ŵelengani Aefeso 5:15, 16, na mawu a munsi.) Kodi zimatenga nthawi itali bwanji kuti munthu aphunzile mfundo zoyambilila za coonadi ca m’Baibo? Zimadalila mmene zinthu zilili mu umoyo wa munthuyo. Komabe, kuphunzila nzelu za Yehova, njila zake, na nchito zake, kulibe malile. (Aroma 11:33) Nsanja ya Mlonda yoyambilila inayelekezela mfundo imodzi ya coonadi na “duŵa laling’ono.” Ndiyeno, inakamba kuti: “Musakhutile ndi duŵa limodzi cabe la coonadi. Ngati kupeza duŵa limodzi, kapena kuti mfundo imodzi ya coonadi kunali kokwanila, Mulungu sakanapeleka mfundo zambili za coonadi. Pitilizani kusakila ena ambili, musaleke.” Conco, tingacite bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi nili na cidziŵitso coculuka bwanji ca coonadi?’ Olo tikakhale na moyo wamuyaya, sitidzakwanitsa kuphunzila zonse zokhudza Yehova. Masiku ano, cofunika kwambili ni kuseŵenzetsa nthawi yathu mwanzelu kuti tiphunzile mfundo zambili za coonadi mmene tingathele. Ganizilani citsanzo ca munthu wina amene anali na njala ya coonadi.
be-CN 14 ¶3-5
“Lunjikitsani Maganizo Anu”
Pali zinthu zambiri zimene zimatilepheretsa kutchera khutu. Tingakhale ndi nkhaŵa m’maganizo mwathu. Phokoso komanso kuyendayenda kwa anthu m’katimo posonkhana kapena panja kungaticheutsa. Kusamva bwino m’thupi kungatilepheretse kuika maganizo pa nkhani. Amene ali ndi ana aang’ono kaŵirikaŵiri amapeza kuti maganizo awo amayendayenda. Kodi chingatithandize n’chiyani kuti tizisunga maganizo athu pa pulogalamu?
Kaŵirikaŵiri, maso ndiwo amatsogolera maganizo athu. Gwiritsani ntchito maso anu kuti akuthandizeni kusunga maganizo pamodzi mwa kuyang’ana wolankhulayo. Pamene atchula lemba m’Baibulo—ngakhale lodziŵika—litseguleni, ndipo m’tsatireni pamene akuŵerenga. Kanizani mutu wanu kucheukira phokoso lililonse kapena munthu amene akuyenda. Ngati maso anu akupereka zocheukitsa zambiri ku maganizo anu, mungaphonye zambiri zimene zikulankhulidwa ku pulatifomu.
Ngati “zolingalira” zina zikukulepheretsani kuika maganizo anu pa pulogalamu, pempherani kwa Yehova kuti akhazikitse pansi maganizo ndi mtima wanu kuti mutchere khutu. (Sal. 94:19; Afil. 4:6, 7) Chitani zimenezo mobwerezabwereza ngati kuli kofunika. (Mat. 7:7, 8) Misonkhano yampingo ndi chogaŵira cha Yehova. Khalani ndi chidaliro chakuti iyenso amafuna kuti mupindule nayo.—1 Yoh. 5:14, 15.
Kufufuza Cuma Cauzimu
“Usayang’ane Uku ndi Uku Mwamantha, Pakuti Ndine Mulungu Wako”
14 Mfundo yoyamba ni yakuti, monga otsatila a Yesu, timayembekezela kuzondewa. (Mat. 10:22) Yesu anakambilatu kuti ophunzila ake adzazunzidwa kwambili m’masiku otsiliza. (Mat. 24:9; Yoh. 15:20) Yaciŵili, zimene Yesaya analosela zionetsa kuti kuwonjezela pa kutizonda, adani athu adzaseŵenzetsa zida zosiyana-siyana polimbana nafe. Zida zimenezo, ni cinyengo camacenjela, mabodza amkunkhuniza, cizunzo coopsa, na zina zotelo. (Mat. 5:11) N’zoona kuti Yehova sadzaletsa adani athu kuseŵenzetsa zida zimenezi polimbana nafe. (Aef. 6:12; Chiv. 12:17) Koma sitifunika kucita mantha. Cifukwa ciani?
15 Onani mfundo yacitatu imene tiyenela kukumbukila. Yehova anakamba kuti, “Cida ciliconse” cimene cidzaseŵenzetsedwa kuti citivulaze “sicidzapambana.” Monga mmene cipupa cingatitetezele ku mvula yoopsa yamkuntho, nayenso Yehova amatiteteza kwa “anthu ankhanza” amene amazunza anzawo. (Ŵelengani Yesaya 25:4, 5.) Ndithudi, adani athu sadzakwanitsa kutiwononga kothelatu!—Yes. 65:17
APRIL 27–MAY 3
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU YESAYA 56-57
Kudziwa Kuti Yehova ndi Mulungu Wathu Kumatibweletsela Cimwemwe
ip-2-CN 269 ¶14-16
Yehova Amatsitsimutsa Mzimu wa Odzichepetsa
14 Komabe, nthaŵi ya kupirira kwa Mulungu idzatha. Polingalira za nthaŵi imeneyo, Yehova akulengeza kuti: “Ineyo ndidzanena za ‘chilungamoʼ chako ndi ntchito zako, ndipo sizidzakupindulira. Ukamafuula popempha thandizo, Mafano amene unasonkhanitsa sadzakupulumutsa. Mphepo idzaulutsa mafano onsewo ndipo mpweya udzawakankhira kutali.” (Yesaya 57:12, 13a) Yehova adzavumbula chilungamo chabodza cha Yuda. Sadzapindula ndi ntchito zake zachinyengo. ‘Zosonkhanitsa’ zake, mafano omwe ali nawo, sadzamupulumutsa. Pamene tsoka lifika, milungu imene amaidalira idzauluzika ndi kuwomba chabe kwa mphepo.
15 Mawu a Yehova akuchitika mu 607 B.C.E. Chimenecho ndicho chaka chimene Mfumu Nebukadinezara ya Babulo ikuwononga Yerusalemu, ikuwotcha kachisi, ndi kutenga ukapolo anthu ena. “Choncho Ayuda anatengedwa kudziko lawo nʼkupita nawo ku ukapolo.”—2 Mafumu 25:1-21.
16 Mofananamo, mafano ambirimbiri a Matchalitchi Achikristu sadzawapulumutsa pa tsiku la mkwiyo wa Yehova. (Yesaya 2:19-22; 2 Atesalonika 1:6-10) Matchalitchi Achikristu adzafafanizidwa limodzi ndi ‘Babulo Wamkulu’ yense, amene ndi zipembedzo zonse zonyenga za padziko lapansi. Chilombo chofiiritsa chophiphiritsa ndi nyanga zake khumi ‘zidzam’khalitsa [Babulo Wamkulu] wabwinja wausiwa, nizidzadya nyama yake, nizidzam’psereza ndi moto.’ (Chivumbulutso 17:3, 16, 17) Ndifetu okondwa kwambiri kuti tinamvera lamulo lakuti: “Tulukani mmenemo, anthu anga; kuti mungayanjane ndi machimo ake, ndi kuti mungalandireko ya miliri yake”! (Chivumbulutso 18:4, 5) Tisabwererenso kwa iye kapena ku njira zake.
“Ufumu Wanga Suli Mbali ya Dziko Lino”
16 Ndithudi! Kusintha kumeneku n’kofunika ngako. Baibo imayelekezela mtundu wa anthu na nyanja imene ikuwinduka, imene ikulephela kukhala bata. (Yes. 17:12; 57:20, 21; Chiv. 13:1) Pamene mavuto a zandale akucititsa anthu kukhala osagwilizana komanso aciwawa, ise Akhristu takhalabe ogwilizana ndi amtendele. Ndipo pamene Yehova aona kusagwilizana kwa anthu padzikoli, amanyadila kuona mgwilizano umene uli pakati pa anthu ake.—Ŵelengani Zefaniya 3:17.
w99-CN 10/1 11 ¶4
“Mphindi ya Mtendere” Ili Pafupi!
4 Popeza kuti Yehova ndi “Mulungu wa mtendere,” anthu amene amakonda Mulungu ndipo amalemekezadi mfundo zake zolungama ndi okhawo amene amakhala ndi mtendere. Inde, Yehova sapereka mtendere kwa wina aliyense. “’Oipa alibe mtendere,’ akutero Mulungu.” Zili choncho chifukwa chakuti anthu oipa amakana kutsogozedwa ndi mzimu woyera wa Mulungu, umene chipatso chake ndicho mtendere.—Aroma 15:33; Yesaya 57:21; Agalatiya 5:22.
Kufufuza Cuma Cauzimu
w07-CN 1/15 10 ¶3
Mfundo Zazikulu za M’buku la Yesaya—Gawo 2
56:6—Kodi “alendo” ndani ndipo ‘amatsatira pangano la Yehova’ m’njira yotani? “Alendo” ndiwo “nkhosa zina” za Yesu. (Yohane 10:16) Amatsatira pangano la Yehova latsopano mwa kumvera malamulo okhudza panganolo, kuchita zinthu mogwirizana ndi zonse zimene zakonzedwa kudzera m’panganolo, kudya chakudya chauzimu chofanana ndi Akhristu odzozedwa, ndi kuwathandiza m’ntchito yolalikira za Ufumu ndi kupanga ophunzira.
w06-CN 11/1 27 ¶1
Kulemekeza Misonkhano Yathu Yopatulika
YEHOVA wasonkhanitsa anthu ake, Akhristu odzozedwa ndi anzawo, kuti amulambire pa ‘phiri lake lopatulika.’ Akuwasangalatsa ‘m’nyumba yake yopemphereramo,’ yomwe ndi kachisi wake wauzimu, kapena kuti “nyumba yopemphereramo mitundu yonse.” (Yesaya 56:7; Maliko 11:17) Zochitika zimenezi zikusonyeza kuti kulambira kwa Yehova n’koyera, kosadetsedwa, ndi kokwezeka. Mwa kulemekeza moyenerera misonkhano yathu yomwe timaphunzirako ndi kulambirako, timasonyeza kuti timaona zinthu zopatulika monga mmene Yehova amazionera.