LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
Mabuku a m’Cinyanja (2000-2026)
Tulukani
Loŵani
LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Takulandilani
Ici ni cida cofufuzila m'mabuku olembewa na Mboni za Yehova mu vitundu volekana-lekana.
Ngati mufuna kucita daunilodi, yendani pa jw.org.
Cilengezo
Taikaponso vitundu vina: Chedungun (Coast), Dominican Sign Language, French (Canada)
  • Lelo

Sondo, September 6

Ndinu woyenela, inu Yehova Mulungu wathu kulandila ulemelelo, ulemu ndi mphamvu cifukwa munalenga zinthu zonse.​—Chiv. 4:11.

Cifukwa copambana cimene timalalikila uthenga wabwino n’cakuti timamukonda Yehova Mulungu na dzina lake loyela. Timaona ulaliki wathu monga njila imene timatamandila Mulungu amene timam’konda. Timavomeleza na mtima kuti Yehova Mulungu ni woyenela kulandila ulemelelo, ulemu, na mphamvu kwa alambili ake okhulupilika. Timam’patsa ulemelelo na ulemu tikamauzako ena umboni wosatsutsika wakuti ‘analenga zinthu zonse’ komanso kuti tilipo cifukwa ca iye. Timam’patsa mphamvu, inde mphamvu zathu, tikamaseŵenzetsa nthawi yathu, mphamvu zathu, komanso zinthu zathu potengako mbali mokwanila m’nchito yolalikila malinga na mmene zinthu zilili kwa ife. (Mat. 6:33; Luka 13:24; Akol. 3:23) Mwacidule, tinganene kuti timakonda kukamba za Mulungu amene timakonda. Timalimbikitsidwanso kuuzako ena za dzina lake komanso zimene limatanthauza. w24.05 17 ¶11

Kusanthula Malemba Tsiku ndi Tsiku—2026

Mande, September 7

Iye .  . amapeleka mphoto kwa anthu amene amamufunafuna ndi mtima wonse.​—Aheb. 11:6.

Yehova amatithandiza kukhala na mtendele komanso kukhala acimwemwe, ndipo m’tsogolo adzatipatsa moyo wosatha. Tili na ciyembekezo cakuti adzatifupa cifukwa ali na cifuno komanso mphamvu zocitila zimenezi. Ndipo izi zimatisonkhezela kukangalika pa kulambila kwathu monga mmene atumiki okhulupilika a Mulungu a m’nthawi zakumbuyo anacitila. Izi n’zimene Timoteyo wa m’zaka za zana loyamba anacita. (Aheb. 6:​10-12) Timoteyo anaika ciyembekezo cake mwa Mulungu wamoyo. (1 Tim. 4:10) Conco anali na zifukwa zabwino zotumikilila Mulungu molimbika na kudzipeleka na mtima wonse. Anacita bwanji zimenezi? Mtumwi Paulo anamulimbikitsa kuti anole maluso ake a kuphunzitsa mumpingo komanso mu ulaliki. Anam’limbikitsanso kuti akhale citsanzo cabwino kwa okhulupilila anzake, acinyamata na acikulile omwe. Anapatsidwanso nchito zina zovuta zomwe zinaphatikizapo kupeleka uphungu wamphamvu koma wacikondi kwa amene anali kuufunikila. (1 Tim. 4:​11-16; 2 Tim. 4:​1-5) Timoteyo sanakaikile kuti Yehova adzamupatsa mphoto cifukwa ca nchito imene anali kugwila.​—Aroma 2:​6, 7. w24.06 22-23 ¶10-11

Kusanthula Malemba Tsiku ndi Tsiku—2026

Ciwili, September 8

Yehova ankacenjeza Aisiraeli ndi Ayuda kudzela mwa aneneli ake onse.​—2 Maf. 17:13.

Nthawi zambili, Yehova anali kuseŵenzetsa aneneli kuti akacenjeze na kuwongolela anthu ake. Mwacitsanzo, kudzela mwa mneneli wake Yeremiya, Mulungu anawauza kuti: “Bwelela Isiraeli wopanduka iwe. Sindidzakuyangʼana mokwiya cifukwa ndine wokhulupilika . . . Sindidzakhala wokwiya mpaka kalekale. Koma vomelezani kuti ndinu olakwa cifukwa mwapandukila Yehova Mulungu wanu.” (Yer. 3:​12, 13) Kupitila mwa Yoweli, Yehova anati: “Bwelelani kwa ine ndi mtima wonse.” (Yow. 2:​12, 13) Mulungu anauzila Yesaya kuti alengeze kuti: “Dziyeletseni. Cotsani zocita zanu zoipa pamaso panga. Lekani kucita zoipa.” (Yes. 1:​16-19) Ndipo kudzela mwa Ezekieli, Yehova anafunsa kuti: “Kodi ine ndimasangalala ndi imfa ya munthu wocimwa? Kodi zimene ine ndimafuna si zoti munthu wocimwayo alape nʼkupitiliza kukhala ndi moyo? Inetu sindisangalala ndi imfa ya munthu aliyense, . . . conco siyani kucita zoipa kuti mupitilize kukhala ndi moyo.” (Ezek. 18:​23, 32) Yehova amakondwela akaona anthu akulapa cifukwa amafuna kuti anthuwo akhale na moyo mpaka kale-kale! w24.08 9 ¶5-6

Kusanthula Malemba Tsiku ndi Tsiku—2026
Takulandilani
Ici ni cida cofufuzila m'mabuku olembewa na Mboni za Yehova mu vitundu volekana-lekana.
Ngati mufuna kucita daunilodi, yendani pa jw.org.
  • Cinyanja
  • Gawilani
  • Makonda
  • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenela Kutsatila
  • Mfundo Yosunga Cisinsi
  • Kusunga Cinsinsi
  • JW.ORG
  • Loŵani
Gawilani