Lolemba, September 7
Amapereka mphoto kwa anthu amene amamufunafuna ndi mtima wonse.—Aheb. 11:6.
Yehova amatipatsa mtendere komanso amatithandiza kukhala osangalala ndipo adzatipatsa moyo wosatha m’tsogolo. Timakhulupirira kwambiri kuti iye amafunitsitsa kutipatsa mphoto ndipo ali ndi mphamvu yochitira zimenezo. Tikamamukhulupirira kwambiri, timapitiriza kumutumikira ndi mtima wonse ngati mmene atumiki ake akale ankachitira. Izi ndi zimenenso Timoteyo anachita. (Aheb. 6:10-12) Timoteyo ankakhulupirira kwambiri kuti Mulungu wamoyo adzamupatsa mphoto. (1 Tim. 4:10) N’chifukwa chake iye ankachita khama potumikira Mulungu. Kodi iye ankachita bwanji zimenezi? Mtumwi Paulo anamulimbikitsa kuti ayesetse kukhala mphunzitsi wabwino pa ntchito yolalikira komanso mumpingo. Iye ankafunikanso kukhala chitsanzo chabwino kwa Akhristu anzake, achinyamata ndi achikulire omwe. Anapatsidwanso ntchito yovuta yomwe inkaphatikizapo kupereka malangizo amphamvu koma achikondi kwa anthu omwe angafunikire malangizowo. (1 Tim. 4:11-16; 2 Tim. 4:1-5) Timoteyo sankakayikira kuti Yehova adzamupatsa mphoto.—Aroma 2:6, 7. w24.06 25:10-11
Lachiwiri, September 8
Yehova ankachenjeza Aisiraeli ndi Ayuda kudzera mwa aneneri ake onse.—2 Maf. 17:13.
Nthawi zonse Yehova ankagwiritsa ntchito aneneri pofuna kuchenjeza komanso kuthandiza anthu ake kuti asinthe. Mwachitsanzo, kudzera mwa Yeremiya, Mulungu ananena kuti: “Bwerera Isiraeli wopanduka iwe. Sindidzakuyangʼana mokwiya chifukwa ndine wokhulupirika . . . Sindidzakhala wokwiya mpaka kalekale. Koma vomerezani kuti ndinu olakwa chifukwa mwapandukira Yehova.” (Yer. 3:12, 13) Kudzera mwa Yoweli, Yehova anati: “Bwererani kwa ine ndi mtima wonse.” (Yow. 2:12, 13) Anauzanso Yesaya kuti alengeze kuti: “Dziyeretseni. Chotsani zochita zanu zoipa pamaso panga. Lekani kuchita zoipa.” (Yes. 1:16-19) Ndiponso kudzera mwa Ezekieli, Yehova anafunsa kuti: “Kodi ine ndimasangalala ndi imfa ya munthu wochimwa? Kodi zimene ine ndimafuna si zoti munthu wochimwayo alape n’kupitiriza kukhala ndi moyo? Inetu sindisangalala ndi imfa ya munthu aliyense, . . choncho siyani kuchita zoipa kuti mupitirize kukhala ndi moyo.” (Ezek. 18:23, 32) Yehova amasangalala akaona kuti anthu alapa chifukwa iye amafuna kuti iwo apitirize kukhala ndi moyo mpaka kalekale. w24.08 32:5-6
Lachitatu, September 9
Malemba onse anauziridwa ndi Mulungu, ndipo ndi othandiza.—2 Tim. 3:16.
Anthu onse a Mulungu amalandira chakudya chauzimu, malangizo komanso chitetezo chimene amafunikira. Chitsanzo chosonyeza kuti Yehova alibe tsankho masiku ano ndi chakuti amathandiza anthu padziko lonse kuti apeze Baibulo. Malemba opatulika analembedwa m’zilankhulo zitatu: Chiheberi, Chiaramu ndi Chigiriki. Kodi anthu amene amalankhula bwino zilankhulo zoyambirirazi ndi amene amakhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova kuposa ena? Ayi si choncho. (Mat. 11:25) Yehova satiitana kuti tikhale alendo ake chifukwa choti tinaphunzira kwambiri kapena timadziwa zilankhulo zoyambirira za Baibulo. Choncho iye amalola kuti anthu padziko lonse adziwe nzeru zake, kaya ndi ophunzira kapena ayi. Baibulo lomwe ndi Mawu ake lamasuliridwa m’zilankhulo zambiri ndipo anthu padziko lonse angathe kupindula ndi zimene limaphunzitsa komanso angadziwe zimene angachite kuti akhale anzake.—2 Tim. 3:16, 17. w24.06 23:13-15