Mande, April 27
Nzelu zimateteza moyo wa amene ali ndi nzeluzo.—Mla. 7:12.
Pogwilitsa nchito fanizo, Yesu anaonetsa kuti n’kupanda nzelu kuunjika cuma padziko lapansi popanda kukhala “wolemela kwa Mulungu.” (Luka 12:16-21) Zamawa sizidziwika. (Miy. 23:4, 5; Yak. 4:13-15) Cifukwa cokhala otsatila a Yesu, timakumana ndi mavuto amene anthu ena sakumana nawo. Pa nkhaniyi, Yesu anati tiyenela kukhala okonzeka “kusiya” zinthu zathu zonse zakuthupi kuti tikhale otsatila ake. (Luka 14:33) Akhristu a ku Yudeya analolela kusiya zinthu zawo zakuthupi ali acimwemwe. (Aheb. 10:34) Masiku anonso, abale ambili alolela kutayikilidwa katundu wawo wakuthupi cifukwa cokana kukhalila mbali m’zandale. (Chiv. 13:16, 17) Cawathandiza n’ciyani kucita zimenezi? Iwo amakhulupilila ndi mtima wonse lonjezo la Yehova lakuti: “Sindidzakusiyani kapena kukutayani ngakhale pang’ono.” (Aheb 13:5.) Timacita zonse zotheka pokonzekela tsogolo lathu. Koma ngati zinthu za mwadzidzidzi zatigwela, timadalila kuti Yehova adzatithandiza. w25.03 29 ¶13-14
Ciwili, April 28
Popeza tamaliza kuphunzila mfundo zoyambilila zokhudza Khristu, tiyeni tiyesetse mwakhama kuti tikhale aakulu mwauzimu. Tisayambe kuyalanso maziko.—Aheb. 6:1.
Yehova satiyembekezela kufika pa ucikulile wauzimu pa ife tokha. Amene amatumikila monga abusa komanso aphunzitsi mu mpingo wa Cikhristu, ni okonzeka kutithandiza. Iwo amatithandiza kufika “pa msinkhu wa munthu wamkulu” mwauzimu, “ngati mmene Khristu analili.” (Aef. 4:11-13) Yehova amapelekanso mzimu wake woyela potithandiza kuti tikhale na “maganizo a Khristu.” (1 Akor. 2:14-16) Kuwonjezela apo, Mulungu anauzila anthu kulemba Mauthenga Abwino anayi, potionetsa mmene Yesu anali kuganizila komanso kucitila zinthu pamene anali kucita utumiki wake pa dziko lapansi. Mwa kutengela maganizo a Yesu na kacitidwe kake ka zinthu, tingakwanilitse colinga cathu cokhala Mkhristu wokhwima. Koma kuti tifike pa ucikulile wauzimu tiyenela kucita zambili kuposa pa kuphunzila “mfundo zoyambilila zokhudza Khristu,” zomwe ni ziphunzitso zoyambilila za Cikhristu. w24.04 4-5 ¶11-12
Citatu, April 29
Kuganiza bwino kudzakuyangʼanila, ndipo kuzindikila kudzakuteteza.—Miy. 2:11.
Tsiku lililonse timafunikila kupanga zisankho. Zisankho zina monga kusankha cakudya cam’mawa kapena nthawi yopita kukagona ndi zosavuta kupanga. Koma zina zimakhala zovuta. Zisankhozo zingakhudze thanzi lathu, cimwemwe cathu, okondedwa athu kapena ubwenzi wathu ndi Yehova. Timafuna kuti zisankho zimene tapanga zitipindulile ife eni komanso a m’banja mwathu. Koma koposa zonse, timafuna kuti zisankho zathu zizikondweletsa Yehova. (Aroma 12:1, 2) Sitepe imene munthu ayenela kutsatila kuti apange cisankho canzelu ndi kudziwa zoona zake zokhudza nkhaniyo. Zimenezi n’zofunika cifukwa ciyani? Tiyelekeze kuti munthu wapita kwa dokotala kukafunsa za matenda aakulu amene ali nawo. Kodi dokotala angapeleke mankhwala kwa munthuyo asanamupime kapena kumufunsako mafunso? Kutalitali! Mofanana ndi dokotala wabwino, inunso mungapange zisankho zanzelu ngati coyamba mumaganizila mfundo zonse zimene mwapeza zokhudzana ndi cisankho cimene mufuna kupanga. w25.01 14 ¶1-3