118 Yamikani Yehova anthu inu, pakuti iye ndi wabwino.+
Kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+
2 Tsopano Isiraeli anene kuti:
“Kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.”+
3 A nyumba ya Aroni anene kuti:+
“Kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.”+
4 Oopa Yehova anene kuti:+
“Kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.”+
5 M’masautso anga ndinaitana Ya.+
Ya anandiyankha ndi kundiika pamalo otakasuka.+
6 Yehova ali kumbali yanga, sindidzaopa.+
Munthu wochokera kufumbi angandichite chiyani?+
7 Yehova ali kumbali yanga pamodzi ndi anthu amene akundithandiza,+
Ndipo ine ndidzayang’ana anthu odana nane atagonja.+
8 Kuthawira kwa Yehova n’kwabwino+
Kusiyana ndi kudalira munthu wochokera kufumbi.+
9 Kuthawira kwa Yehova n’kwabwino+
Kusiyana ndi kudalira anthu olemekezeka.+
10 Mitundu yonse ya anthu inandizungulira,+
Koma ndinali kuikankhira kutali m’dzina la Yehova.+
11 Mitunduyo inandizungulira, ndithu inandizungulira kumbali zonse.+
Koma ndinali kuikankhira kutali m’dzina la Yehova.
12 Inandizungulira ngati njuchi,+
Koma inazima ngati moto wa zitsamba zaminga.+
Ndinali kuikankhira kutali m’dzina la Yehova.+
13 Munandikankha kwambiri kuti ndigwe,+
Koma Yehova anandithandiza.+
14 Ya ndiye malo anga obisalapo ndi mphamvu zanga,+
Iye amandipulumutsa.+
15 M’mahema+ a olungama+
Mumamveka mfuu yachisangalalo ndipo muli chipulumutso.+
Dzanja lamanja la Yehova limachita zamphamvu.+
16 Dzanja lamanja la Yehova likudzikweza pamwamba.+
Dzanja lamanja la Yehova limachita zamphamvu.+
17 Sindidzafa, koma ndidzakhalabe ndi moyo,+
Kuti ndilengeze ntchito za Ya.+
18 Ya anandilanga mwamphamvu,+
Koma sanandipereke ku imfa.+
19 Nditsegulireni zipata zachilungamo,+ anthu inu.
Ndidzalowamo ndipo ndidzatamanda Ya.+
20 Ichi ndi chipata cha Yehova.+
Olungama adzalowamo.+
21 Ndidzakutamandani, chifukwa munandiyankha+
Ndi kundipulumutsa.+
22 Mwala umene omanga nyumba anaukana+
Wakhala mwala wofunika kwambiri wapakona.+
23 Umenewu wachokera kwa Yehova,+
Ndipo ndi wodabwitsa m’maso mwathu.+
24 Ili ndi tsiku limene Yehova wapanga.+
Tidzakondwera ndi kusangalala pa tsiku limeneli.+
25 Haa! Inu Yehova, chonde tipulumutseni.+
Haa! Inu Yehova, chonde tithandizeni kuti zinthu zitiyendere bwino.+
26 Wodala ndi Iye wobwera m’dzina la Yehova.+
Takudalitsani anthu inu potuluka m’nyumba ya Yehova.+
27 Yehova ndiye Mulungu,+
Ndipo amatipatsa kuwala.+
Kongoletsani gulu la anthu amene ali pachikondwerero+ ndi nthambi za mitengo,+ anthu inu.
Likongoletseni mpaka kukafika panyanga za guwa lansembe.+
28 Inu ndinu Mulungu wanga, ndipo ndidzakutamandani.+
Ndinu Mulungu wanga, ndipo ndidzakukwezani.+
29 Yamikani Yehova anthu inu, pakuti iye ndi wabwino.+
Kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+